Exodus 27 – NIRV & CCL

New International Reader’s Version

Exodus 27:1-21

The Altar for Burnt Offerings

1“Build an altar out of acacia wood. It must be four feet six inches high and seven feet six inches square. 2Make a horn stick out from each of its upper four corners. The horns and the altar must be all one piece. Cover the altar with bronze. 3Make everything for the altar out of bronze. Make its pots to remove the ashes. Make its shovels, sprinkling bowls, meat forks, and pans for carrying ashes. 4Make a bronze grate for the altar. Make a bronze ring for each of the four corners of the grate. 5Put the grate halfway up the altar on the inside. 6Make poles out of acacia wood for the altar. Cover them with bronze. 7Put the poles through the rings. They will be on two sides of the altar for carrying it. 8Make the altar out of boards. Leave it hollow. It must look just like what I showed you on the mountain.

The Courtyard

9“Make a courtyard for the holy tent. The south side must be 150 feet long. It must have curtains that are made out of finely twisted linen. 10The curtains must be hung on 20 posts that have 20 bronze bases. The posts must have silver hooks and bands on them. 11The north side must also be about 150 feet long. It must have curtains with 20 posts that have 20 bronze bases. The posts must have silver hooks and bands on them.

12“The west end of the courtyard must be 75 feet wide. It must have curtains with ten posts that have ten bases. 13The east end of the courtyard, toward the sunrise, must also be 75 feet wide. 14On one side of the entrance you must put curtains that are 22 feet six inches long. Hang them on three posts. Each post must have a base. 15On the other side you must also put curtains that are 22 feet six inches long. Hang them on three posts. Each post must have a base.

16“For the entrance to the courtyard, provide a curtain 30 feet long. Make it out of blue, purple and bright red yarn and finely twisted linen. Have someone who sews skillfully make it. Hang it on four posts. Each post must have a base. 17All the posts that are around the courtyard must have silver bands and hooks. They must also have bronze bases. 18The courtyard must be 150 feet long and 75 feet wide. It must have curtains that are made out of finely twisted linen. They must be seven feet six inches high. The posts must have bronze bases. 19Make out of bronze all the other things used for any purpose in the holy tent. That includes all the tent stakes for the tent and the courtyard.

Oil for the Lampstand

20“Command the Israelites to bring you clear oil made from pressed olives. Use it to keep the lamps burning and giving light. 21Aaron and his sons must keep the lamps burning in the tent of meeting. The lamps will be outside the curtain in front of the tablets of the covenant law. The lamps must be kept burning in front of the Lord from evening until morning. This is a law for the Israelites that will last for all time to come.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Eksodo 27:1-21

Guwa Lansembe Yopsereza

1“Upange guwa lansembe lamatabwa amtengo wa mkesha. Likhale lofanana mbali zonse, msinkhu wake masentimita 137, mulitali mwake masentimita 229, mulifupi mwake masentimita 229. 2Upange nyanga imodziimodzi pa ngodya zake zinayizo kuti nyangazo ndi guwalo zikhale chinthu chimodzi, ndipo ulikute guwalo ndi mkuwa. 3Upange ziwiya zamkuwa izi zogwirira ntchito pa guwalo: miphika yochotsera phulusa, mafosholo, mabeseni owazira magazi, ngowe zokowera nyama ndi zosonkhezera moto. 4Upange sefa yachitsulo chamkuwa ndipo mʼngodya zake zinayizo upangiremo mphete zamkuwa. 5Uyike sefayo mmunsi mwa khoma la guwa lansembelo, ndipo ilekezere pakati pa guwa lansembelo. 6Upange nsichi zamtengo wa mkesha ndipo uzikutire ndi mkuwa. 7Pamene mukunyamula guwalo, muzilowetsa nsichizo mʼmphetemo mbali zonse ziwiri za guwalo. 8Guwalo likhale lamatabwa ndi logoba mʼkati mwake. Ulipange monga momwe ndinakuonetsera pa phiri paja.

Za Bwalo la Chihema

9“Upange bwalo la chihema. Mbali yakummwera ikhale yotalika mamita 46 ndipo ikhale ndi nsalu yotchinga yofewa yosalala yolukidwa bwino. 10Upangenso mizati makumi awiri, matsinde makumi awiri amkuwa, ndi ngowe zasiliva ndi zingwe za mizatiyo. 11Mbali yakumpoto ikhalenso yotalika mamita 46 ndipo ikhale ndi nsalu yotchinga. Pakhalenso mizati makumi awiri, matsinde amkuwa makumi awiri, ngowe zasiliva ndi zingwe za mizatiyo.

12“Mbali yakumadzulo ya bwalolo ikhale yotalika mamita 23 ndipo ikhale ndi nsalu yotchinga, nsichi khumi ndi matsinde khumi. 13Mbali yakummawa, kotulukira dzuwa, kutalika kwa bwalo kukhale mamita 23. 14Mbali imodzi yachipata kukhale nsalu yotchinga yotalika mamita asanu ndi awiri, mizati itatu ndi matsinde atatu. 15Ndipo ku mbali inayo kukhale nsalu yotchinga ya mamita asanu ndi awiri pamodzi ndi mizati itatu ndi matsinde atatu.

16“Pa chipata cha bwalolo pakhale nsalu yotchinga yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira ndiponso yofewa yosalala. Nsaluyo ikhale yotalika mamita asanu ndi anayi, yopangidwa ndi anthu aluso. Pakhalenso mizati yake inayi ndi matsinde akenso anayi. 17Mizati yonse yozungulira bwalolo ilumikizidwe ndi zingwe zasiliva. Ngowe zake zikhale zasiliva, koma matsinde ake akhale amkuwa. 18Kutalika kwa bwalolo kukhale mamita 46, mulifupi mwake mamita 23, msinkhu wake masentimita 230. Nsalu ya katani ikhale yofewa ndi yosalala bwino. Matsinde ake akhale amkuwa. 19Zipangizo zonse zogwiritsa ntchito zosiyanasiyana pa chihemacho, zikhomo za chihema ndi zabwalolo zikhale zamkuwa.

Mafuta Anyale

20“Lamula Aisraeli kuti akupatse mafuta anyale a olivi wabwino kwambiri kuti nyalezo ziziyaka nthawi zonse. 21Mʼchihema cha msonkhano, koma kunja kwa nsalu yotchinga Bokosi la Chipangano, Aaroni ndi ana ake azionetsetsa kuti nyale ikukhala chiyakire pamaso pa Yehova kuyambira madzulo mpaka mmawa. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pakati pa Aisraeli pa mibado yonse.”