2 Pedro 2 – NVI & CCL

Nueva Versión Internacional

2 Pedro 2:1-22

Los falsos maestros y su destrucción

1En el pueblo hubo falsos profetas. También entre ustedes habrá falsos maestros que encubiertamente introducirán herejías destructivas, al extremo de negar al mismo Soberano Señor que los rescató. Esto les traerá una pronta destrucción. 2Muchos los seguirán en sus prácticas vergonzosas y por causa de ellos se difamará el camino de la verdad. 3Llevados por la avaricia, estos falsos maestros se aprovecharán de ustedes con palabras engañosas. Desde hace mucho tiempo su condenación está preparada y su destrucción los acecha.

4Dios no perdonó a los ángeles cuando pecaron, sino que los arrojó al abismo, poniéndolos en cadenas de oscuridad y reservándolos para el juicio. 5Tampoco perdonó al mundo antiguo cuando mandó un diluvio sobre los impíos, aunque protegió a ocho personas, incluyendo a Noé, predicador de la justicia. 6Además, condenó a las ciudades de Sodoma y Gomorra, y las redujo a cenizas, poniéndolas como escarmiento para los impíos. 7Por otra parte, libró al justo Lot, que se encontraba abrumado por la vida desenfrenada de esos perversos; 8pues este justo, que convivía con ellos y amaba el bien, día tras día sentía que se le despedazaba el alma por las obras malvadas que veía y oía. 9Todo esto demuestra que el Señor sabe librar de la tentación a los que viven con devoción a Dios, y sabe también guardar a los injustos para castigarlos en el día del juicio. 10Esto les espera sobre todo a los que siguen los corrompidos deseos de la naturaleza humana y desprecian la autoridad.

¡Son atrevidos y arrogantes! No tienen reparo en insultar a los seres celestiales, 11mientras que los ángeles, a pesar de superarlos en fuerza y en poder, no pronuncian contra tales seres ninguna acusación insultante en la presencia del Señor. 12Pero aquellos blasfeman en asuntos que no entienden. Como animales irracionales, se guían únicamente por el instinto, pues nacieron para ser atrapados y degollados. Lo mismo que esos animales, perecerán también en su corrupción 13y recibirán el justo pago por sus injusticias. Su concepto de placer es entregarse a las pasiones desenfrenadas en pleno día. Son manchas y suciedad que gozan de sus placeres, mientras los acompañan a ustedes en sus comidas. 14Tienen los ojos llenos de adulterio y son insaciables en el pecar; seducen a las personas inconstantes; son expertos en la avaricia, ¡hijos de maldición! 15Han abandonado el camino recto y se han extraviado para seguir la senda de Balán, hijo de Bosor,2:15 Bosor. Var. Beor. a quien le encantaba el salario de la injusticia. 16Pero fue reprendido por su maldad: su burra —una muda bestia de carga—, habló con voz humana y refrenó la locura del profeta.

17Estos individuos son fuentes sin agua, niebla empujada por la tormenta, para quienes está reservada la más densa oscuridad. 18Pronunciando discursos arrogantes y sin sentido, seducen con los deseos naturales desenfrenados a quienes apenas comienzan a apartarse de los que viven en el error. 19Prometen libertad, cuando ellos mismos son esclavos de la corrupción, ya que cada uno es esclavo de aquello que lo ha dominado. 20Si, habiendo escapado de la contaminación del mundo por haber conocido a nuestro Señor y Salvador Jesucristo, vuelven a enredarse en ella y son vencidos, terminan en peores condiciones que al principio. 21Más les hubiera valido no conocer el camino de la justicia que abandonarlo después de haber conocido el santo mandamiento que se les dio. 22En su caso ha sucedido lo que acertadamente afirman estos proverbios: «El perro vuelve a su vómito»2:22 Pr 26:11. y «la puerca lavada, a revolcarse en el lodo».

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Petro 2:1-22

Aphunzitsi Onyenga

1Koma panalinso aneneri onama pakati pa Aisraeli, monga padzakhalanso aphunzitsi onyenga pakati panu. Iwo adzalowetsa mwamseri ziphunzitso zonama ndi zowononga, nadzakana Ambuye amene anawawombola, ndipo motero adzadziyitanira okha chiwonongeko mwadzidzidzi. 2Ambiri adzatsata njira zawo zochititsa manyazi ndipo chifukwa cha iwowa, anthu adzanyoza njira ya choonadi. 3Pofuna kupeza chuma, aphunzitsiwa adzakudyerani chuma chanu pokuwuzani nkhani zopeka. Chiweruzo chawo chinakonzedwa kale, ndipo chikuwadikira.

4Pakuti Mulungu sanalekerere angelo atachimwa paja, koma anawaponya mʼndende, nawayika mʼmaenje amdima, kuwasunga kuti adzaweruzidwe. 5Iye sanalekerere dziko lapansi kalelo, koma anapulumutsa Nowa, mlaliki wa chilungamo, ndi anthu ena asanu ndi awiri atadzetsa chigumula pa dziko lapansi kwa anthu akhalidwe losapembedza Mulunguyo. 6Mulungu anaweruza mizinda ya Sodomu ndi Gomora nayiwononga ndi moto, kuti ikhale chitsanzo cha zimene zidzachitikira anthu osapembedza Mulungu. 7Koma Iye anapulumutsa Loti, munthu wolungama, amene ankavutika ndi khalidwe lonyansa la anthu oyipa. 8(Pakuti munthu wolungamayo, pokhala pakati pawo tsiku ndi tsiku ankavutika mu mtima ndi makhalidwe awo oyipa amene ankawaona ndi kuwamva). 9Tsono mutha kuona kuti Ambuye amadziwa kuwapulumutsa kwake pa mayesero anthu opembedza. Amadziwanso kusunga osalungama kuti alangidwe mpaka tsiku la chiweruzo. 10Makamaka amene amatsata zilakolako zonyansa zathupi nanyoza ulamuliro.

Anthu amenewa ndi odzikuza, ndipo otsata chifuniro cha iwo eni, sasamala za munthu, saopa kuchitira chipongwe zolengedwa za mmwamba. 11Komatu ngakhale angelo, amene ali akulu ndi amphamvu kuwaposa, sayankhula za chipongwe pobweretsa chiweruzo pa iwo kuchokera kwa Ambuye. 12Koma anthu awa amachita chipongwe zinthu zimene sakuzidziwa. Ali ngati zirombo zopanda nzeru. Zirombo zolengedwa kuti zigwidwe ndi kuwonongedwa, ndipo ngati zirombozo adzawonongedwa.

13Iwo adzalangidwa chifukwa cha zoyipa zimene anachita. Koma chimene chimawakomera ndi kumangochita zokondweretsa thupi masanasana. Iwo ali ngati mawanga ndi zilema. Podya nanu pamodzi amakondwera kuchita za chinyengo. 14Ndi maso awo odzaza ndi chigololo, salekeza kuchimwa. Amanyengerera anthu osakhazikika. Iwo ndi akatswiri pa dyera ndi chuma, ndipo ndi ana otembereredwa! 15Iwo anasiya njira yolungama ndipo anapatuka kutsata njira ya Baalamu mwana wa Beori, amene anakonda malipiro a chosalungama. 16Koma anadzudzulidwa chifukwa cha kulakwa kwakeko. Bulu, nyama imene siyankhula, inayankhula ngati munthu kuletsa misala ya mneneriyo.

17Anthu amenewa ali ngati akasupe wopanda madzi, ndiponso ngati nkhungu yowuluzidwa ndi mphepo yamkuntho. Mulungu wawasungira mdima wandiweyani. 18Pakuti anayankhula mawu opanda pake ndi onyada, ndipo ndi zilakolako zoyipa za thupi amanyenga anthu amene angopulumuka kumene pakati pa anzawo oyipa. 19Amawalonjeza ufulu, pomwe iwo eni ndi akapolo a zizolowezi zowononga. Pajatu munthu amakhala kapolo wa chilichonse chimene chikumulamulira. 20Ngati anapulumuka ku zodetsa za dziko lapansi podziwa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu, pambuyo pake nagwidwanso ndi kugonjetsedwa ndi zomwezo, potsiriza adzakhala oyipa kuposa mmene analili poyamba. 21Kukanakhala bwino akanapanda kudziwa njira ya chilungamo, koposa ndi kuyileka atadziwa lamulo loyera limene Mulungu anawapatsa. 22Kwa iwo miyambi iyi ndi yoona, “Galu wabwerera ku masanzi ake,” ndipo, “Nkhumba imene inasamba, yakunkhunizikanso mʼmatope.”