역대상 23 – KLB & CCL

Korean Living Bible

역대상 23:1-32

레위인들의 직무상 분류

1다윗이 나이 많아 늙었을 때 그는 자기 아들 솔로몬을 이스라엘의 왕 으로 삼고

2모든 이스라엘 지도자들과 제사장들과 레위인들을 한자리에 불러모았다.

3그때 다윗이 소집한 레위 사람들은 30세 이상의 남자들로 모두 38,000명이었다.

4다윗은 그 중에서 24,000명은 성전 업무를 맡아 보게 하고 6,000명은 사무관과 재판관으로,

54,000명은 문지기로, 나머지 4,000명은 다윗이 직접 만든 악기를 가지고 여호와를 찬양하는 성가대원으로 일하게 하였다.

6그런 다음 다윗은 그들을 레위의 세 아들 이름을 따서 게르손 계열, 고핫 계열, 므라리 계열로 나누었다.

7게르손 계열은 다시 라단파와 시므이파로 나뉘었는데

8라단의 아들은 여히엘, 세담, 요엘이었으며

923:9 원문에는 ‘시므이의 아들’ 로 되어 있으나 분명치 않다.라단의 자손 중에는 슬로못, 하시엘, 하란이 있었다. 이들은 모두 라단파의 족장들이었다.

10-11시므이의 아들은 야핫, 시나, 여우스, 브리아였으며 여우스와 브리아는 아들이 많지 않았으므로 통상 한집안으로 취급되었다. 이들은 모두 시므이파의 족장들이었다.

12고핫 계열은 아므람파, 이스할파, 헤브론파, 웃시엘파로 나뉘었다.

13그리고 아므람의 아들은 아론과 모세였다. 아론과 그의 자손은 백성들의 제물을 여호와께 바쳐서 제사를 드리고 항상 여호와를 섬기며 여호와의 이름으로 백성들을 축복하는 거룩한 직분을 맡았다.

14그러나 하나님의 사람 모세의 아들들은 단순히 레위 지파에만 포함되어 있었다.

15모세의 아들은 게르솜과 엘리에셀이었으며

16게르솜 집안의 족장은 스브엘이었고

17엘리에셀 집안의 족장은 르하뱌였다. 엘리에셀은 아들이 하나밖에 없었으나 그의 아들 르하뱌에게는 자녀들이 많았다.

18이스할의 아들은 그 집안의 족장인 슬로밋이었으며

19헤브론의 아들은 그 집안의 족장인 여리야, 아마랴, 야하시엘, 여가므암이었다.

20그리고 웃시엘의 아들은 그 집안의 족장인 미가와 잇시야였다.

21므라리 계열은 마흘리파와 무시파로 나뉘었으며 마흘리의 아들은 엘르아살과 기스였다.

22엘르아살은 아들 없이 죽었고 그의 딸들은 기스의 아들인 그의 사촌들과 결혼하였다.

23그리고 무시의 아들은 마흘리와 에델과 여레못이었다.

24이들은 여호와의 성전에서 섬기는 일을 맡은 레위의 후손들로서 각 계열과 파와 집안별로 조사된 20세 이상의 족장들이었다.

25다윗은 이스라엘의 하나님 여호와께서 자기 백성에게 평화를 주시고 항상 예루살렘에 계실 것이므로

26레위 사람이 더 이상 성막과 그 기구들을 이리저리 옮길 필요가 없다고 말하였다.

27그래서 다윗의 이 마지막 지시에 따라 20세 이상의 레위 사람들을 대상으로 인구 조사를 실시하였다.

28레위 사람들의 업무는 성전에서 제사를 드릴 때 아론의 후손인 제사장들을 돕고 또 성전을 관리하며 정결 의식을 행할 때 도와주는 일이었다.

29그리고 그들은 차림상의 빵과 곡식 제물에 쓰는 밀가루와 누룩을 넣지 않고 만든 과자와 구워서 만든 제물과 기름을 섞은 밀가루를 준비하고 또 성전 제물을 달아 보고 재기도 했으며

30매일 아침저녁으로 여호와 앞에 서서 감사와 찬양을 드리고

31안식일과 초하루와 그 밖의 모든 명절에 불로 태워 바치는 번제를 드릴 때 제사장들을 도와주었다. 이와 같이 그들은 일정한 규정에 따라 여호와 앞에서 섬기며

32성막과 성소를 돌보고 성전에서 제사장들의 여러 가지 일을 도와주었다.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mbiri 23:1-32

Fuko la Levi

1Davide atakalamba, ali ndi zaka zambiri, anayika Solomoni mwana wake kukhala mfumu ya Israeli.

2Iye anasonkhanitsanso pamodzi atsogoleri onse a Israeli, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi. 3Anawerenga Alevi kuyambira a zaka makumi atatu ndi kupitirirapo, ndipo chiwerengero cha amuna onse chinali 38,000. 4Davide anati, “Mwa amenewa, amuna 24,000 aziyangʼanira ntchito za mʼNyumba ya Mulungu ndipo 6,000 akhale akuluakulu ndi oweruza. 5Amuna 4,000 akhale alonda a pa zipata ndipo 4,000 azitamanda Yehova ndi zipangizo zoyimbira zimene ndazipereka ndi cholinga chimenecho.”

6Davide anagawa Aleviwo mʼmagulumagulu motsatira ana a Levi awa: Geresoni, Kohati ndi Merari.

Banja la Geresoni

7Ana a Geresoni:

Ladani ndi Simei.

8Ana a Ladani:

Mtsogoleri Yehieli, Zetamu ndi Yoweli. Onse analipo atatu.

9Ana a Simei:

Selomoti, Haziyeli ndi Harani. Onse analipo atatu.

Awa anali atsogoleri a mabanja a Ladani.

10Ndipo ana a Simei anali:

Yahati, Zina, Yeusi ndi Beriya.

Awa anali ana a Semei. Onse analipo anayi.

11Mtsogoleri anali Yahati, ndipo Ziza anali wachiwiri, koma Yeusi ndi Beriya analibe ana aamuna ambiri. Kotero iwo anawerengedwa ngati banja limodzi ndipo anapatsidwa ntchito imodzinso yofanana.

Banja la Kohati

12Ana a Kohati:

Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli. Onse analipo anayi.

13Ana a Amramu:

Aaroni ndi Mose.

Aaroni ndi zidzukulu zake anapatulidwa kwamuyaya kuti azipereka zinthu zopatulika kwambiri monga nsembe pamaso pa Yehova, komanso kuti azitumikira pamaso pake ndi kumadalitsa anthu mʼdzina lake kwamuyaya. 14Ana a Mose munthu wa Mulungu anawerengedwa ngati gawo la fuko la Levi.

15Ana a Mose:

Geresomu ndi Eliezara.

16Zidzukulu za Geresomu:

Mtsogoleri anali Subaeli.

17Zidzukulu za Eliezara:

Mtsogoleri anali Rehabiya.

Eliezara analibe ana ena aamuna, koma ana a Rehabiya anali ochuluka kwambiri.

18Ana a Izihari:

Mtsogoleri anali Selomiti.

19Ana a Hebroni:

Mtsogoleri anali Yeriya, wachiwiri anali Amariya, Yahazieli anali wachitatu ndipo Yekameamu anali wachinayi.

20Ana a Uzieli:

Mtsogoleri anali Mika ndipo wachiwiri anali Isiya.

Banja la Merari

21Ana a Merari:

Mahili ndi Musi.

Ana a Mahili:

Eliezara ndi Kisi.

22Eliezara anamwalira wopanda ana aamuna. Iye anali ndi ana aakazi okhaokha. Abale awo, ana a Kisi, ndiwo amene anawakwatira.

23Ana a Musi:

Mahili, Ederi ndi Yeremoti. Onse analipo atatu.

24Izi zinali zidzukulu za Levi mwa mabanja awo, atsogoleri a mabanja monga momwe analembedwera mayina awo ndi monga momwenso anawerengedwera, banja lililonse pa lokha. Awa ndi anthu ogwira ntchito oyambira zaka makumi awiri zobadwa kapena kupitirirapo, amene amatumikira mʼNyumba ya Yehova. 25Popeza Davide anati, “Pakuti Yehova Mulungu wa Israeli, wapereka mpumulo kwa anthu ake ndipo wabwera kudzakhala mu Yerusalemu kwamuyaya, 26sikofunikiranso kuti Alevi azinyamula tenti kapena zipangizo za chipembedzo.” 27Potsata malangizo otsiriza a Davide, Alevi anawerengedwa kuyambira amuna a zaka makumi awiri zakubadwa kapena kupitirirapo.

28Ntchito ya Alevi inali kuthandiza zidzukulu za Aaroni pa ntchito yotumikira mʼNyumba ya Yehova monga kuyangʼanira mabwalo, zipinda zamʼmbali, kuyeretsa zinthu zonse zachipembedzo, ndiponso kuchita ntchito zina za mʼnyumba ya Mulungu. 29Iwo amayangʼanira buledi amene amayikidwa pa tebulo, ufa wa nsembe yachakudya, timitanda ta buledi wopanda yisiti: kuphika ndi kusakaniza, ndiponso miyeso yonse ndi kukula kwake. 30Iwo amayimiriranso mmawa uliwonse kuthokoza ndi kutamanda Yehova. Amachitanso chomwecho madzulo, 31ndiponso popereka nsembe zopsereza kwa Yehova pa Sabata ndi pa chikondwerero cha Mwezi Watsopano, ndi pa nthawi yosankhidwa ya Chikondwerero. Iwo amatumikira pamaso pa Yehova nthawi zonse mwa chiwerengero chawo ndi momwe analangizidwira.

32Ndipo kotero Alevi anachita ntchito yawo ya ku tenti ya msonkhano ya ku Malo Opatulika ndiponso molamulidwa ndi abale awo, zidzukulu za Aaroni, pa ntchito ya mʼNyumba ya Yehova.