Proverbs 13 – KJV & CCL

King James Version

Proverbs 13:1-25

1A wise son heareth his father’s instruction: but a scorner heareth not rebuke. 2A man shall eat good by the fruit of his mouth: but the soul of the transgressors shall eat violence. 3He that keepeth his mouth keepeth his life: but he that openeth wide his lips shall have destruction. 4The soul of the sluggard desireth, and hath nothing: but the soul of the diligent shall be made fat. 5A righteous man hateth lying: but a wicked man is loathsome, and cometh to shame. 6Righteousness keepeth him that is upright in the way: but wickedness overthroweth the sinner.13.6 the sinner: Heb. sin 7There is that maketh himself rich, yet hath nothing: there is that maketh himself poor, yet hath great riches. 8The ransom of a man’s life are his riches: but the poor heareth not rebuke. 9The light of the righteous rejoiceth: but the lamp of the wicked shall be put out.13.9 lamp: or, candle 10Only by pride cometh contention: but with the well advised is wisdom. 11Wealth gotten by vanity shall be diminished: but he that gathereth by labour shall increase.13.11 by labour: Heb. with the hand 12Hope deferred maketh the heart sick: but when the desire cometh, it is a tree of life. 13Whoso despiseth the word shall be destroyed: but he that feareth the commandment shall be rewarded.13.13 shall be rewarded: or, shall be in peace 14The law of the wise is a fountain of life, to depart from the snares of death. 15Good understanding giveth favour: but the way of transgressors is hard. 16Every prudent man dealeth with knowledge: but a fool layeth open his folly.13.16 layeth…: Heb. spreadeth 17A wicked messenger falleth into mischief: but a faithful ambassador is health.13.17 a faithful…: Heb. an ambassador of faithfulness 18Poverty and shame shall be to him that refuseth instruction: but he that regardeth reproof shall be honoured. 19The desire accomplished is sweet to the soul: but it is abomination to fools to depart from evil. 20He that walketh with wise men shall be wise: but a companion of fools shall be destroyed.13.20 destroyed: Heb. broken 21Evil pursueth sinners: but to the righteous good shall be repayed. 22A good man leaveth an inheritance to his children’s children: and the wealth of the sinner is laid up for the just. 23Much food is in the tillage of the poor: but there is that is destroyed for want of judgment. 24He that spareth his rod hateth his son: but he that loveth him chasteneth him betimes. 25The righteous eateth to the satisfying of his soul: but the belly of the wicked shall want.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Miyambo 13:1-25

1Mwana wanzeru amamvera malangizo a abambo ake,

koma mwana wonyoza samamvetsera chidzudzulo.

2Munthu amapeza zinthu zabwino chifukwa cha mawu ake,

koma anthu osakhulupirika amalakalaka zachiwawa basi.

3Iye amene amagwira pakamwa pake amateteza moyo wake,

koma amene amayankhula zopanda pake adzawonongeka.

4Munthu waulesi amakhumbira zinthu koma sapeza kanthu,

koma munthu wakhama adzalemera.

5Munthu wolungama amadana ndi zabodza,

koma zochita za munthu woyipa zimanyansa ndiponso zimachititsa manyazi.

6Chilungamo chimateteza munthu wangwiro,

koma tchimo limagwetsa munthu wochimwa.

7Wina amadziyesa kuti ndi wolemera chonsecho alibe kanthu kalikonse;

munthu wina amaoneka ngati wosauka chonsecho ali ndi chuma chambiri.

8Chuma cha munthu wolemera chitha kuwombola moyo wake,

koma munthu wosauka amamva chidzudzulo.

9Nyale ya munthu wolungama ndi yokondweretsa,

koma nyale ya munthu woyipa imazimitsidwa.

10Chipongwe chosamalabadirako za anthu ena chimadzetsa mikangano,

koma womva malangizo a anzawo ndiwo ali ndi nzeru.

11Chuma chochipeza mofulumira chidzatha pangʼonopangʼono

koma chuma chosonkhanitsidwa pangʼonopangʼono chidzachulukirachulukira.

12Chinthu chochiyembekezera chikalephereka chimalefula mtima,

koma chinthu chochilakalaka chikachitikadi chimakhala ngati mtengo wamoyo.

13Amene amanyoza malangizo adzawonongeka,

koma amene amasamala lamulo amalandira mphotho.

14Malangizo a munthu wanzeru ali ngati kasupe wamoyo;

amathandiza munthu kuti asakondwe mu msampha wa imfa.

15Munthu wa nzeru zabwino amapeza kuyanja pakati pa anthu,

koma munthu wosakhulupirika adzawonongeka.

16Munthu wochenjera amachita zinthu mwanzeru,

koma chitsiru chimaonetsa poyera uchitsiru wake.

17Wamthenga woyipa amagwetsa anthu mʼmavuto,

koma nthumwi yodalirika imabweretsa mtendere.

18Wokana mwambo adzasauka ndi kunyozedwa,

koma wosamala chidzudzulo adzalemekezedwa.

19Chinthu chochilakalaka chikachitika chimasangalatsa mtima,

koma zitsiru zimadana ndi kuleka zoyipa.

20Woyenda ndi anthu anzeru nayenso adzakhala wanzeru;

koma woyenda ndi zitsiru adzapwetekeka.

21Choyipa chitsata mwini,

koma wochita zolungama adzalandira mphotho yabwino.

22Munthu wabwino amasiyira zidzukulu zake cholowa,

koma chuma cha munthu wochimwa amachilandira ndi olungama.

23Tsala la munthu wosauka limalola chakudya chambiri,

koma anthu opanda chilungamo amachilanda.

24Amene sakwapula mwana wake, ndiye kuti amamuda,

koma wokonda mwana wake sazengereza kumulanga.

25Munthu wolungama amakhala ndi zakudya zoti adye nʼkukhuta,

koma mʼmimba mwa munthu woyipa mumakhala pululu ndi njala.