Luke 4 – KJV & CCL

King James Version

Luke 4:1-44

1And Jesus being full of the Holy Ghost returned from Jordan, and was led by the Spirit into the wilderness, 2Being forty days tempted of the devil. And in those days he did eat nothing: and when they were ended, he afterward hungered. 3And the devil said unto him, If thou be the Son of God, command this stone that it be made bread. 4And Jesus answered him, saying, It is written, That man shall not live by bread alone, but by every word of God. 5And the devil, taking him up into an high mountain, shewed unto him all the kingdoms of the world in a moment of time. 6And the devil said unto him, All this power will I give thee, and the glory of them: for that is delivered unto me; and to whomsoever I will I give it. 7If thou therefore wilt worship me, all shall be thine. 8And Jesus answered and said unto him, Get thee behind me, Satan: for it is written, Thou shalt worship the Lord thy God, and him only shalt thou serve. 9And he brought him to Jerusalem, and set him on a pinnacle of the temple, and said unto him, If thou be the Son of God, cast thyself down from hence: 10For it is written, He shall give his angels charge over thee, to keep thee: 11And in their hands they shall bear thee up, lest at any time thou dash thy foot against a stone. 12And Jesus answering said unto him, It is said, Thou shalt not tempt the Lord thy God. 13And when the devil had ended all the temptation, he departed from him for a season.

14¶ And Jesus returned in the power of the Spirit into Galilee: and there went out a fame of him through all the region round about. 15And he taught in their synagogues, being glorified of all.

16¶ And he came to Nazareth, where he had been brought up: and, as his custom was, he went into the synagogue on the sabbath day, and stood up for to read. 17And there was delivered unto him the book of the prophet Esaias. And when he had opened the book, he found the place where it was written, 18The Spirit of the Lord is upon me, because he hath anointed me to preach the gospel to the poor; he hath sent me to heal the brokenhearted, to preach deliverance to the captives, and recovering of sight to the blind, to set at liberty them that are bruised, 19To preach the acceptable year of the Lord. 20And he closed the book, and he gave it again to the minister, and sat down. And the eyes of all them that were in the synagogue were fastened on him. 21And he began to say unto them, This day is this scripture fulfilled in your ears. 22And all bare him witness, and wondered at the gracious words which proceeded out of his mouth. And they said, Is not this Joseph’s son? 23And he said unto them, Ye will surely say unto me this proverb, Physician, heal thyself: whatsoever we have heard done in Capernaum, do also here in thy country. 24And he said, Verily I say unto you, No prophet is accepted in his own country. 25But I tell you of a truth, many widows were in Israel in the days of Elias, when the heaven was shut up three years and six months, when great famine was throughout all the land; 26But unto none of them was Elias sent, save unto Sarepta, a city of Sidon, unto a woman that was a widow. 27And many lepers were in Israel in the time of Eliseus the prophet; and none of them was cleansed, saving Naaman the Syrian. 28And all they in the synagogue, when they heard these things, were filled with wrath, 29And rose up, and thrust him out of the city, and led him unto the brow of the hill whereon their city was built, that they might cast him down headlong. 30But he passing through the midst of them went his way, 31And came down to Capernaum, a city of Galilee, and taught them on the sabbath days. 32And they were astonished at his doctrine: for his word was with power.

33¶ And in the synagogue there was a man, which had a spirit of an unclean devil, and cried out with a loud voice, 34Saying, Let us alone; what have we to do with thee, thou Jesus of Nazareth? art thou come to destroy us? I know thee who thou art; the Holy One of God. 35And Jesus rebuked him, saying, Hold thy peace, and come out of him. And when the devil had thrown him in the midst, he came out of him, and hurt him not. 36And they were all amazed, and spake among themselves, saying, What a word is this! for with authority and power he commandeth the unclean spirits, and they come out. 37And the fame of him went out into every place of the country round about.

38¶ And he arose out of the synagogue, and entered into Simon’s house. And Simon’s wife’s mother was taken with a great fever; and they besought him for her. 39And he stood over her, and rebuked the fever; and it left her: and immediately she arose and ministered unto them.

40¶ Now when the sun was setting, all they that had any sick with divers diseases brought them unto him; and he laid his hands on every one of them, and healed them. 41And devils also came out of many, crying out, and saying, Thou art Christ the Son of God. And he rebuking them suffered them not to speak: for they knew that he was Christ. 42And when it was day, he departed and went into a desert place: and the people sought him, and came unto him, and stayed him, that he should not depart from them. 43And he said unto them, I must preach the kingdom of God to other cities also: for therefore am I sent. 44And he preached in the synagogues of Galilee.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Luka 4:1-44

Kuyesedwa kwa Yesu

1Yesu, wodzazidwa ndi Mzimu Woyera, anachoka ku mtsinje wa Yorodani ndipo anatsogozedwa ndi Mzimu Woyerayo kupita ku chipululu, 2kumene anayesedwa ndi mdierekezi masiku makumi anayi. Sanadye kena kalikonse pa masiku amenewo, ndipo pa mapeto pake anamva njala.

3Mdierekezi anati kwa Iye, “Ngati ndiwe Mwana wa Mulungu, uza mwala uwu kuti usanduke buledi.”

4Yesu anayankha kuti, “Zalembedwa: ‘Munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha.’ ”

5Mdierekezi anamutengera Iye pamalo aatali ndipo mʼkamphindi namuonetsa maufumu onse a dziko lapansi. 6Ndipo anati kwa Iye, “Ndidzakupatsani ulamuliro ndi ulemerero wawo; pakuti anandipatsa ine, ndipo ndingathe kupereka kwa aliyense amene ndikufuna. 7Ngati mutandilambira, zonsezi zidzakhala zanu.”

8Yesu anayankha kuti, “Zalembedwa: ‘Pembedza Yehova Mulungu wako ndi kumutumikira Iye yekha.’ ”

9Mdierekezi anapita naye ku Yerusalemu namuyimiritsa pamwamba penipeni pa Nyumba ya Mulungu. Ndipo anati, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu dziponyeni nokha pansi kuchokera pano. 10Pakuti kwalembedwa,

“Adzalamulira angelo ake za iwe

kuti akutchinjirize mosamala;

11ndipo adzakunyamula ndi manja awo,

kuti phazi lako lisagunde pa mwala.”

12Yesu anayankha kuti, “Mawu akuti, ‘Musamuyese Yehova Mulungu wanu.’ ”

13Mdierekezi atamaliza mayesero awa onse, anamusiya Iye kufikira atapeza mpata wina.

Yesu Akanidwa ku Nazareti

14Yesu anabwerera ku Galileya mu mphamvu ya Mzimu Woyera, ndipo mbiri yake inafalikira ku madera onse a ku midzi. 15Iye ankaphunzitsa mʼmasunagoge awo, ndipo aliyense ankamulemekeza.

16Iye anapita ku Nazareti, kumene anakulira, ndipo pa tsiku la Sabata anakalowa mʼsunagoge, monga mwa chikhalidwe chake. Ndipo anayimirira kuti awerenge malemba. 17Anamupatsa buku la mneneri Yesaya. Atalitsekula, anapeza pamalo pamene panalembedwa kuti,

18“Mzimu wa Ambuye ali pa Ine;

chifukwa wandidzoza

kuti ndilalikire Uthenga Wabwino kwa osauka.

Wandituma kuti ndilalikire kwa a mʼndende kuti amasulidwe

ndi kwa osaona kuti apenyenso,

kumasulidwa kwa osautsidwa,

19ndi kulalikira za nthawi imene Ambuye adzakomere mtima anthu awo.”

20Kenaka Iye anatseka bukulo, nalibwezera kwa wotumikira ndipo anakakhala pansi. Maso a aliyense mʼsunagogemo anali pa Iye, 21ndipo anawawuza kuti, “Lero malemba awa akwaniritsidwa mmene mwamveramu.”

22Onse anayankhula zabwino za Iye ndipo anadabwa ndi mawu ogwira moyo amene anatuluka mʼkamwa mwake. Iwo anafunsa kuti, “Kodi uyu si mwana wa Yosefe?”

23Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, mudzandiwuza mwambi uwu: Singʼanga, dzichiritse wekha! Chitanso mʼmudzi wa kwanu kuno zimene ife tamva kuti Iwe unazichita ku Kaperenawo.”

24Iye anapitiriza kuti, “Zoonadi, ndikukuwuzani kuti palibe mneneri amene amavomerezedwa ku mudzi kwawo. 25Ine ndikukutsimikizirani kunali amayi ambiri amasiye mu Israeli mʼnthawi ya Eliya, kumwamba kutatsekedwa kwa zaka zitatu ndi theka ndipo kunali njala yayikulu mʼdziko lonselo. 26Komabe Eliya sanatumidwe kwa mmodzi mwa iwo, koma kwa mkazi wamasiye wa ku Zerefati ku chigawo cha Sidoni. 27Ndipo kunali akhate ambiri ku Israeli mʼnthawi ya mneneri Elisa, koma panalibe mmodzi mwa iwo anachiritsidwa kupatula Naamani wa ku Siriya.”

28Anthu onse mʼsunagogemo anapsa mtima atamva izi. 29Anayimirira namutulutsira kunja kwa mzindawo, ndipo anamutengera pamwamba pa phiri pamene mzindawo unamangidwapo, ndi cholinga chakuti amuponyere ku phompho. 30Koma Iye anangoyenda pakati pa gulu la anthulo nachokapo.

Yesu Atulutsa Mzimu Woyipa

31Kenaka Iye anapita ku Kaperenawo, mudzi wa ku Galileya, ndipo pa Sabata anayamba kuphunzitsa anthu. 32Iwo anadabwa ndi chiphunzitso chake chifukwa uthenga wake unali ndi ulamuliro.

33Mʼsunagogemo munali munthu wogwidwa ndi mzimu woyipa. Iye analira ndi mawu akulu, akuti 34“Aa! Kodi mukufuna chiyani kwa ife, Yesu wa ku Nazareti? Kodi mwabwera kudzatiwononga? Ndikudziwa kuti ndinu ndani, ndinu Woyerayo wa Mulungu!”

35Yesu anachidzudzula kwambiri nati, “Khala chete! Tuluka mwa iye.” Chiwandacho chinamugwetsa munthuyo pansi pamaso pa onse ndipo chinatuluka wosamupweteka.

36Anthu onse anadabwa ndipo anati kwa wina ndi mnzake, “Kodi chiphunzitso ichi ndi chotani? Ndi ulamuliro ndi mphamvu Iye akulamulira mizimu yoyipa ndipo ikutuluka!” 37Ndipo mbiri yake inafalikira madera onse ozungulira.

Yesu Achiritsa Anthu Ambiri

38Yesu anatuluka mʼsunagoge ndipo anapita kwa Simoni. Tsopano mpongozi wake wa Simoni amadwala malungo akulu, ndipo anamupempha Yesu kuti amuthandize. 39Ndipo anawerama nadzudzula malungowo ndipo anamusiya. Anadzuka nthawi yomweyo nayamba kuwatumikira.

40Pamene dzuwa linkalowa, anthu anabweretsa kwa Yesu onse amene anali ndi matenda osiyanasiyana, ndipo atasanjika manja ake pa aliyense, anachiritsidwa. 41Komanso ziwanda zinkatuluka mwa anthu ambiri, zikufuwula kuti, “Inu ndinu Mwana wa Mulungu!” Koma Iye anazidzudzula ndipo sanazilole kuyankhula chifukwa zimadziwa kuti Iye ndi Khristu.

42Kutacha, Yesu anapita ku malo a yekha. Anthu ankamufunafuna Iye ndipo pamene anafika kumene anali, anthuwo anayesetsa kumuletsa kuti asawachokere. 43Koma Iye anati, “Ine ndikuyenera kulalikira Uthenga Wabwino wa ufumu wa Mulungu ku mizinda inanso chifukwa ichi ndi chimene ananditumira.” 44Ndipo Iye anapitirirabe kulalikira mʼmasunagoge a ku Yudeya.