Acts 18 – KJV & CCL

King James Version

Acts 18:1-28

1After these things Paul departed from Athens, and came to Corinth; 2And found a certain Jew named Aquila, born in Pontus, lately come from Italy, with his wife Priscilla; (because that Claudius had commanded all Jews to depart from Rome:) and came unto them. 3And because he was of the same craft, he abode with them, and wrought: for by their occupation they were tentmakers. 4And he reasoned in the synagogue every sabbath, and persuaded the Jews and the Greeks. 5And when Silas and Timotheus were come from Macedonia, Paul was pressed in the spirit, and testified to the Jews that Jesus was Christ. 6And when they opposed themselves, and blasphemed, he shook his raiment, and said unto them, Your blood be upon your own heads; I am clean: from henceforth I will go unto the Gentiles.

7¶ And he departed thence, and entered into a certain man’s house, named Justus, one that worshipped God, whose house joined hard to the synagogue. 8And Crispus, the chief ruler of the synagogue, believed on the Lord with all his house; and many of the Corinthians hearing believed, and were baptized. 9Then spake the Lord to Paul in the night by a vision, Be not afraid, but speak, and hold not thy peace: 10For I am with thee, and no man shall set on thee to hurt thee: for I have much people in this city. 11And he continued there a year and six months, teaching the word of God among them.

12¶ And when Gallio was the deputy of Achaia, the Jews made insurrection with one accord against Paul, and brought him to the judgment seat, 13Saying, This fellow persuadeth men to worship God contrary to the law. 14And when Paul was now about to open his mouth, Gallio said unto the Jews, If it were a matter of wrong or wicked lewdness, O ye Jews, reason would that I should bear with you: 15But if it be a question of words and names, and of your law, look ye to it; for I will be no judge of such matters. 16And he drave them from the judgment seat. 17Then all the Greeks took Sosthenes, the chief ruler of the synagogue, and beat him before the judgment seat. And Gallio cared for none of those things.

18¶ And Paul after this tarried there yet a good while, and then took his leave of the brethren, and sailed thence into Syria, and with him Priscilla and Aquila; having shorn his head in Cenchrea: for he had a vow. 19And he came to Ephesus, and left them there: but he himself entered into the synagogue, and reasoned with the Jews. 20When they desired him to tarry longer time with them, he consented not; 21But bade them farewell, saying, I must by all means keep this feast that cometh in Jerusalem: but I will return again unto you, if God will. And he sailed from Ephesus. 22And when he had landed at Cæsarea, and gone up, and saluted the church, he went down to Antioch. 23And after he had spent some time there, he departed, and went over all the country of Galatia and Phrygia in order, strengthening all the disciples.

24¶ And a certain Jew named Apollos, born at Alexandria, an eloquent man, and mighty in the scriptures, came to Ephesus. 25This man was instructed in the way of the Lord; and being fervent in the spirit, he spake and taught diligently the things of the Lord, knowing only the baptism of John. 26And he began to speak boldly in the synagogue: whom when Aquila and Priscilla had heard, they took him unto them, and expounded unto him the way of God more perfectly. 27And when he was disposed to pass into Achaia, the brethren wrote, exhorting the disciples to receive him: who, when he was come, helped them much which had believed through grace: 28For he mightily convinced the Jews, and that publickly, shewing by the scriptures that Jesus was Christ.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Machitidwe a Atumwi 18:1-28

Ku Korinto

1Zitatha izi, Paulo anachoka ku Atene ndipo anapita ku Korinto. 2Kumeneko anakumana ndi Myuda wina dzina lake Akula, nzika ya ku Ponto amene anali atangofika kumene kuchokera ku Italiya pamodzi ndi mkazi wake Prisila, chifukwa Klaudiyo analamula Ayuda onse kuti achoke ku Roma. Paulo anapita kukawaona. 3Popeza Paulo anali mʼmisiri wosoka matenti monga iwo, iye anakhala nawo namagwirira ntchito pamodzi. 4Tsiku la Sabata lililonse Paulo amakambirana ndi anthu mʼsunagoge, kufuna kukopa Ayuda ndi Agriki.

5Sila ndi Timoteyo atafika kuchokera ku Makedoniya, Paulo ankangogwira ntchito yolalikira yokha basi, kuchitira umboni Ayuda kuti Yesu ndiye Khristu. 6Koma pamene Ayuda anatsutsana naye ndi kumuchita chipongwe, iye anakutumula zovala zake nati, “Magazi anu akhale pamitu yanu! Ine ndilibe mlandu. Kuyambira tsopano ndipita kwa anthu a mitundu ina.”

7Ndipo Paulo anatuluka mʼsunagoge napita ku nyumba yoyandikana ndi sunagoge ya Tito Yusto, munthu wopembedza Mulungu. 8Krispo, mkulu wa sunagoge, pamodzi ndi a pa banja lake lonse anakhulupirira Ambuye; ndiponso Akorinto ambiri amene anamva Paulo akulalikira anakhulupiriranso nabatizidwa.

9Usiku wina Ambuye anaonekera kwa Paulo mʼmasomphenya namuwuza kuti, “Usaope, pitiriza kuyankhula, usakhale chete. 10Pakuti Ine ndili nawe, palibe aliyense amene adzakukhudza ndi kukuchitira choyipa, chifukwa mu mzinda muno ndili ndi anthu ambiri.” 11Choncho Paulo anakhala kumeneko chaka ndi miyezi isanu ndi umodzi akuphunzitsa Mawu a Mulungu.

12Galiyo ali mkulu wa boma wa ku Akaya, Ayuda mogwirizana anamugwira Paulo napita naye ku bwalo la milandu. 13Iwo anati, “Munthu uyu akukopa anthu kuti azipembedza Mulungu mwanjira zotsutsana ndi malamulo athu.”

14Pamene Paulo ankati ayankhule, Galiyo anati kwa Ayuda, “Ukanakhala mlandu wochita choyipa kapena wolakwira mnzake, bwenzi nditakumverani bwinobwino. 15Koma popeza ndi nkhani yokhudza mawu, mayina ndi malamulo anu, kambiranani nokhanokha. Ine sindidzaweruza zinthu zimenezi.” 16Kotero iye anawapirikitsa mʼbwalo la milandu. 17Kenaka iwo anagwira Sositene, mkulu wa sunagoge, ndipo anamumenya mʼbwalo la milandu momwemo. Koma Galiyo sanasamale zimenezi.

Prisila, Akula ndi Apolo

18Paulo anakhalabe ku Korinto masiku ambiri. Kenaka anawasiya abale nakwera sitima ya pamadzi kupita ku Siriya, pamodzi ndi Prisila ndi Akula. Asanakakwere sitima ya pamadzi, anameta tsitsi lake ku Kenkreya chifukwa anali atalumbira. 19Iwo anafika ku Efeso, kumene Paulo anasiyako Prisila ndi Akula. Iye yekha analowa mʼsunagoge nakambirana ndi Ayuda. 20Iwo atapempha kuti akakhale nawo nthawi yayitali, iye anakana. 21Koma pamene amachoka anawalonjeza kuti, “Ndidzabweranso Mulungu akalola.” Ndipo anakwera sitima ya pamadzi kuchoka ku Efeso. 22Pamene Paulo anafika ku Kaisareya, anakwera kukapereka moni ku mpingo kenaka anatsikira ku Antiokeya.

23Atakhala kwa kanthawi ku Antiokeya, Paulo anachokako nayendera madera onse a ku Galatiya ndi ku Frugiya kulimbikitsa ophunzira onse.

Za Apolo

24Pa nthawi yomweyi Myuda wina dzina lake Apolo, mbadwa ya ku Alekisandriya anafika ku Efeso. Anali munthu wophunzira ndi wodziwa bwino Malemba. 25Apoloyu anaphunzitsidwa njira ya Ambuye, ndipo anayankhula ndi changu chachikulu naphunzitsa za Yesu molondola, ngakhale amadziwa ubatizo wa Yohane wokha. 26Iye anayamba kuyankhula mʼsunagoge molimba mtima. Pamene Prisila ndi Akula anamva, iwo anamuyitanira ku nyumba yawo ndipo anamufotokozera njira ya Mulungu molongosoka bwino.

27Pamene Apolo anafuna kupita ku Akaya, abale anamulimbikitsa, nalemba kalata kwa ophunzira a kumeneko kuti amulandire. Atafika kumeneko, anathandiza kwambiri amene anakhulupirira mwachisomo. 28Pakuti iye anatsutsa Ayuda mwamphamvu pamaso pa anthu, natsimikiza kuchokera mʼMalemba kuti Yesu ndiye Khristu.