ネヘミヤ 記 8 – JCB & CCL

Japanese Contemporary Bible

ネヘミヤ 記 8:1-18

8

律法を朗読するエズラ

1-5さて、第七の月の中旬になると、民はこぞって水の門の前の広場に集まって来ました。そして指導者エズラに、その昔、神がモーセに与えた律法を読んで聞かせてほしい、と願い出たのです。エズラはモーセの律法の巻物を取り寄せ、朗読する姿が誰からも見えるよう、特製の木の台に立ちました。そして、朝から昼まで朗読して聞かせたのです。巻物を開くと、人々はいっせいに立ち上がり、理解できる者は熱心に耳を傾けました。エズラの右側には、マティテヤ、シェマ、アナヤ、ウリヤ、ヒルキヤ、マアセヤが並び、左には、ペダヤ、ミシャエル、マルキヤ、ハシュム、ハシュバダナ、ゼカリヤ、メシュラムが並びました。

6エズラが、偉大なる神である主をほめたたえると、民はみな手を上げ、「アーメン、アーメン」とこたえてひざまずき、地面にひれ伏して、主を礼拝しました。 7-8エズラが巻物を読み上げると、レビ人のヨシュア、バニ、シェレベヤ、ヤミン、アクブ、シャベタイ、ホディヤ、マアセヤ、ケリタ、アザルヤ、エホザバデ、ハナン、ペラヤなどが人々の中に入って行き、その箇所の意味を説明しました。

9律法がどのように命じているかを理解すると、人々はみな泣きだしました。それで、エズラをはじめ、総督の私や補佐役のレビ人たちは、こう言い聞かせました。「このような日に泣いてはならない。きょうは神である主の聖なる日ではないか。 10ごちそうを食べてお祝いし、貧しい人には施しをする日なのだ。神である主を喜ぶことこそ、あなたがたの力なのだ。しょんぼりと悲しそうにしていてはいけない。」 11「静粛に、静粛に」と、レビ人も声をかけて回り、「そうです。泣くことはないのです。きょうは聖なる日で、悲しみの日ではありません」と言いました。 12人々は解散すると、それぞれお祝いのごちそうを食べ、施しをしました。神のことばを聞き、理解することができたので、大いに喜び、盛大に祝ったのです。

13翌日、諸族の指導者とレビ人はエズラに会い、律法をもっとくわしく調べることにしました。 14すると、その月には仮庵の祭りを祝い、イスラエル人はみな仮小屋に住むようにと、主がモーセに命じていたことがわかりました。 15その仮小屋についても、山で取って来たオリーブ、ミルトス、なつめやし、いちじくなどの枝で作るようにとあったので、エルサレムをはじめ全国民にそのおふれが出されました。 16人々は実際に出かけて枝を切り出し、自宅の屋上、庭内、神殿の庭、水の門、エフライムの門の広場などに小屋を建てました。 17そして祭りの七日間を、その中で暮らしたのです。誰もが喜びにあふれていました。この行事はヨシュアの時代以来、ずっと中断されていたのです。 18エズラはこの七日間、毎日、巻物を読み上げ、八日目には、モーセの律法に従って厳粛な閉会礼拝を執り行いました。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Nehemiya 8:1-18

1Anthu onse anasonkhana ngati munthu mmodzi pabwalo limene lili patsogolo pa Chipata cha Madzi. Iwo anawuza mlembi Ezara kuti abwere ndi buku la malamulo a Mose limene Yehova anapereka kwa Aisraeli.

2Choncho pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri wansembe Ezara, anabwera ndi buku la malamulo ku msonkhano wa amuna, akazi ndi ana onse amene ankatha kumvetsa zinthu bwino. 3Choncho Ezara anawerenga bukulo atayangʼana bwalo la Chipata cha Madzi kuyambira mmawa mpaka masana pamaso pa amuna, akazi ndi onse amene ankamvetsa bwino zinthu. Ndipo anthu onse anatchera khutu kuti amve malamulowo.

4Mlembi Ezara anayimirira pa nsanja ya mitengo imene anthu anamanga chifukwa cha msonkhanowu. Ku dzanja lake lamanja kunayimirira Matitiya, Sema, Anaya, Uriya, Hilikiya ndi Maaseya, ndipo kudzanja lake lamanzere kunali Pedaya, Misaeli, Malikiya, Hasumu, Hasibadana, Zekariya ndi Mesulamu.

5Tsono Ezara anatsekula buku, akuona popeza anayima pa nsanja. Pamene anafutukula bukulo anthu onse anayimirira. 6Ezara anatamanda Yehova, Mulungu wamkulu, ndipo anthu onse anakweza manja awo ndi kuyankha kuti, “Ameni, ameni.” Pambuyo pake onse anaweramitsa pansi mitu yawo napembedza Yehova akanali chizolikire choncho.

7Anthuwo atayimiriranso Alevi awa: Yesuwa, Bani, Serebiya, Yamini, Akubu, Sabetayi, Hodiya, Maaseya, Kerita, Azariya, Yozabadi, Hanani ndi Pelaya anawathandiza kuti amvetse bwino malamulowo. 8Iwo anawerenga buku la malamulo a Mulungu momveka bwino ndi kutanthauzira mawuwo kuti anthu amvetse bwino zowerengedwazo.

9Tsono bwanamkubwa Nehemiya pamodzi ndi wansembe ndi mlembi Ezara komanso Alevi amene amaphunzitsa anthu anati kwa anthu onse, “Lero ndi tsiku lopatulika kwa Yehova Mulungu wanu. Musakhale ndi chisoni ndipo musalire.” Anayankhula choncho popeza anthu onse ankalira atamva mawu a buku la malamulo lija.

10Nehemiya anatinso, “Pitani, kachiteni phwando ku nyumba ndipo mukawagawireko ena amene alibe kanthu kalikonse popeza lero ndi tsiku lopatulika kwa Yehova. Musakhale ndi chisoni, pakuti chimwemwe cha Yehova ndiye mphamvu yanu.”

11Alevi anakhalitsa bata anthu onse powawuza kuti, “Khalani chete, pakuti lero ndi tsiku lopatulika ndipo musakhale ndi chisoni.”

12Anthu onse anachoka kupita kukadya ndi kumwa. Chakudya china anatumiza kwa anzawo. Choncho panali chikondwerero chachikulu popeza tsopano anali atamvetsa bwino mawu a Mulungu amene anawawerengera ndi kuwafotokozerawo.

13Mmawa mwake atsogoleri a mabanja pamodzi ndi ansembe ndi alevi anasonkhana kwa Ezara, mlembi wa malamulo kuti aphunzire mawu a malamulowo. 14Tsono anapeza kuti zinalembedwa mʼbuku la malamulo kuti Yehova analamula kudzera mwa Mose kuti Aisraeli azikhala mʼzithando pa nthawi yonse ya chikondwerero cha mwezi wachisanu ndi chiwiri. 15Choncho analengeza ndi kufalitsa mʼmizinda yawo yonse ndi mu Yerusalemu kuti, “Pitani ku phiri mukadule nthambi za mtengo wa olivi, za mtengo wa olivi wa kutchire, za mtengo wa mchisu, za mtengo wa mgwalangwa ndiponso za mitengo ina ya masamba, zomangira zithando monga zalembedweramu ndi kubwera nazo.”

16Choncho anthu anapita kukatenga nthambi ndipo aliyense anadzimangira misasa pa denga ya nyumba yake, mʼmabwalo awo, mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu, mʼbwalo la pa Chipata cha Madzi ndiponso mʼbwalo la pa Chipata cha Efereimu. 17Gulu lonse la anthu limene linabwera ku ukapolo linamanga misasa ndipo linakhala mʼmenemo. Kuyambira nthawi ya Yoswa mwana wa Nuni mpaka tsiku limenelo nʼkuti Aisraeli asanachitepo zimenezi. Choncho panali chimwemwe chachikulu.

18Tsiku ndi tsiku, kuyambira tsiku loyamba mpaka lomaliza, Ezara ankawerenga buku la malamulo a Mulungu. Anthu anachita chikondwerero masiku asanu ndi awiri. Pa tsiku lachisanu ndi chitatu panachitika msonkhano potsata buku la malamulo lija.