הבשורה על-פי לוקס 12 – HHH & CCL

Habrit Hakhadasha/Haderekh

הבשורה על-פי לוקס 12:1-59

1בינתיים הלך וגדל מספר הנוכחים עד שהגיע לאלפים רבים, ומרוב דוחק וצפיפות דרכו אחד על רגלי השני. ישוע פנה תחילה אל תלמידיו ואמר: ”היזהרו מצביעותם של הפרושים! הם מעמידים פני צדיקים תמימים בזמן שמעשיהם והתנהגותם מצביעים על היפוכו של דבר. אולם צביעות כזאת אי־אפשר להסתיר לנצח, 2כי בבוא העת כל מה שמוסתר עכשיו ייגלה, וכל מה שאינו ידוע ייוודע. 3לפיכך, כל מה שאמרתם בחשכה יישמע באור היום, וכל מה שלחשתם בין ארבעה קירות ייקרא בקולי קולות מעל גגות הבתים!

4”ידידים יקרים, אל תפחדו מאלה הרוצים להרוג אתכם, כי הם יכולים להמית אך ורק את הגוף, בעוד שבנפש אין הם מסוגלים לפגוע. 5היודעים אתם ממי עליכם לפחד? מאלוהים! כי הוא מסוגל להמית ואחר כך להשליך לגיהינום!

6”מה מחירן של חמש ציפורי דרור, שניים־שלושה שקלים? אף־על־פי־כן אלוהים אינו שוכח אף אחת מהן. 7אלוהים יודע אפילו את מספר השערות על ראשכם. לכן אל תפחדו; אתם יקרים לאלוהים יותר מציפורים רבות.

8”אני מבטיח לכם שכל המודה שהוא מאמין בי לפני בני־האדם, גם אני אכבד אותו ואודה בו לפני מלאכי אלוהים. 9אולם מי שמתכחש לי לפני בני־אדם, גם אני אתכחש לו לפני מלאכי אלוהים. 10ובכל זאת, מי שידבר נגד בן־האדם ייסלח לו, בעוד שאדם המדבר נגד רוח הקודש לא ייסלח לו לעולם.

11”כאשר יביאו אתכם למשפט בבתי־הכנסת או לפני שליטים וממשלות, אל תדאגו כיצד תגנו על עצמכם וכיצד תעידו, 12כי רוח הקודש יגיד לכם מה לומר בזמן המתאים.“

13איש אחד מהקהל קרא אל ישוע: ”רבי, אמור בבקשה לאחי שייתן לי את חלקי בירושת אבינו.“

14אולם ישוע השיב: ”מי מינה אותי להיות לכם שופט ובורר? 15היזהרו מכל חמדנות, כי חיי האדם והאושר אינם תלויים בעושרו ובנכסיו.“

16ישוע סיפר להם את המשל הבא: ”לעשיר אחד היה שדה פורה שהניב יבול רב. 17אסמיו היו מלאים עד אפס מקום, והאיש לא ידע מה לעשות בתבואה הרבה שכבר לא יכול היה לאחסן. 18’אני יודע מה עלי לעשות!‘ קרא האיש. ’אהרוס את האסמים הקיימים ואבנה לעצמי אסמים גדולים יותר. כך אוכל לאחסן את התבואה הרבה שלי. 19אחר כך אומר לעצמי: יש לך מספיק כסף לשנים רבות. מעתה ואילך אל תעבוד קשה, כי אם אכול, שתה ותהנה‘. 20אבל אלוהים אמר לו: ’שוטה שכמוך! הלילה תמות, ומה תעשה עם כל מה שאגרת לעצמך?‘ 21כך יקרה לכל אדם האוגר לעצמו אוצר על־פני האדמה ולא בשמים.“

22ישוע פנה אל תלמידיו ואמר: ”אל תדאגו למה שתאכלו או תלבשו, 23כי החיים חשובים הרבה יותר מהאוכל, והגוף חשוב הרבה יותר מהלבוש. 24קחו לדוגמה את העורבים – הם אינם זורעים, אינם קוצרים ואין להם מחסן לאגור את מזונם. אף־על־פי־כן לא חסר להם דבר כי אלוהים מאכיל אותם ודואג להם. ואתם הרי יקרים לאלוהים הרבה יותר מן העופות! 25מלבד זאת, מה תועיל דאגתכם? האם יכולה דאגתכם להוסיף עוד יום לחייכם או עוד סנטימטר לקומתכם? 26אם דאגתכם אינה מסוגלת לשנות דברים פעוטים כאלה, מה הטעם לדאוג לדברים גדולים יותר?

27”הביטו בשושנים – הן אינן טוות ואינן אורגות, ואף־על־פי־כן אפילו שלמה המלך בכל תפארתו לא היה לבוש יותר יפה מהן! 28ואם אלוהים מלביש את פרחי השדה הצומחים היום ונובלים מחר, האם אינכם חושבים שילביש גם אתכם, חסרי אמונה שכמותכם? 29אל תדאגו למה שתאכלו ותשתו ואל תדאגו שמא לא יספק לכם אלוהים את מה שאתם צריכים. 30בני־אדם שאינם מאמינים באלוהים דואגים יום־יום למה שיאכלו וישתו, אולם אביכם שבשמים יודע בדיוק מה אתם צריכים. 31דאגו לכל הקשור באלוהים ובמלכותו, והוא יספק לכם יום־יום את כל צרכיכם.

32”אל תפחד, עדר קטן, כי אביכם שבשמים משתוקק להעניק לכם את מלכותו. 33מכרו את רכושכם ותנו כסף לנזקקים. מעשה זה יגדיל את אוצרכם בשמים, ואוצר בשמים לעולם לא ייפגם. כן, אוצרכם לעולם לא ידלדל, גנב לא יוכל לגנבו ועש לא יכרסם בו. 34במקום שבו נמצא אוצרכם שם נמצא גם לבכם ומחשבותיכם.

35”היו מוכנים לכל מה שיקרה – כשאתם לבושים ובידכם נר דולק – 36כמשרתים המצפים לשובו של אדונם מהחתונה. כשיבוא אדונם וידפוק בדלת, יפתחו לו מיד. 37שמחה גדולה מצפה לאלה שיהיו מוכנים לשובו של האדון, כי הוא בעצמו יושיב אותם ליד השולחן וישרת אותם. 38אולי הוא יבוא בלילה, ואולי בבוקר השכם. אך בכל עת שיבוא תהיה שמחה גדולה לכל המשרתים שימצא אותם מוכנים לבואו.

39”אילו ידעו את השעה, היו כולם מתכוננים לבואו, כשם שהיו מתכוננים לבואו של גנב אילו ידעו מתי יבוא. 40גם אתם היו מוכנים תמיד, כי בן־האדם יבוא בשעה בלתי צפויה.“

41”אדון,“ פתח פטרוס בשאלה, ”האם מכוון המשל הזה אלינו בלבד או אל כולם?“

42”משל זה מכוון אל כל אדם נאמן ונבון, אשר אדוניו הפקיד בידו את האחריות להשגיח על עבדיו ולדאוג לכלכלתם“, השיב האדון. 43”ברוך תהיה אם בשובי אמצא אותך ממלא את תפקידך בנאמנות. 44אנשים נאמנים כאלה אני אפקיד על כל רכושי.

45”אולם אם אתה רשע ותאמר לעצמך: ’אה, האדון לא ישוב כל כך מהר‘, – ותתאכזר ליתר העבדים ותבלה את זמנך במסיבות, בזלילה ובשתייה – 46אדונך יופיע בשעה בלתי צפויה, ואז הוא יכה אותך קשות ויקבע את מקומך עם הבלתי־נאמנים. 47הוא גם ייענש בכל חומרת הדין, מאחר שידע את חובתו וסירב למלא אותה.

48”לעומת זאת, אדם שלא ידע את רצון אדוניו ועשה מעשה המחייב עונש, לא ייענש בכל חומרת הדין. מי שקיבל הרבה יידרש ממנו הרבה חזרה, כי אחריותו גדולה משל אחרים.

49”באתי להצית אש בעולם, ואני מייחל שמשימתי תושלם. 50טבילה נוראה מצפה לי, ועד שאעבור אותה אני שרוי במצוקה גדולה. 51אתם חושבים שבאתי להשכין שלום בארץ? טעות בידיכם; באתי לגרום למחלוקת, 52מעתה ואילך תתפלגנה משפחות; שלושה מבני המשפחה יהיו בעדי ושניים נגדי – או להיפך. 53אב יחלוק על בנו; בן יחלוק על אביו; אם תחלוק על בתה; בת תחלוק על אמה; החמה תחלוק על כלתה; והכלה תחלוק על חמותה.“

54ישוע פנה אל ההמון ואמר: ”כשאתם רואים עננים עולים מן המערב אתם אומרים: ’עומד לרדת גשם‘. ואתם צודקים. 55כשנושבת רוח דרומית אתם אומרים: ’יהיה חמסין‘. ואתם צודקים. 56צבועים! אתם יודעים לפרש את סימני הטבע בשמים ובארץ, אבל אתם מסרבים להבין את משמעות העת שבה אנו חיים. 57מדוע אינכם מסוגלים להחליט בעצמכם מה נכון? 58כשאתה פוגש את יריבך בדרך לבית־המשפט, השתדל להשלים איתו וליישב את הסכסוך לפני שתגיעו לשופט, אחרת השופט עלול להשליך אותך לכלא. 59ואם כך יהיה, לא תצא מהכלא עד שתשלם את מלוא חובתך!“

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Luka 12:1-59

Chenjezo ndi Chilimbikitso

1Nthawi yomweyo, anthu miyandamiyanda atasonkhana, ndi kumapondanapondana, Yesu anayamba kuyankhula poyamba kwa ophunzira ake, nati, “Chenjereni ndi yisiti wa Afarisi, amene ndi chinyengo. 2Palibe chinthu chophimbika chimene sichidzawululika, kapena chobisika chimene sichidzadziwika. 3Chimene mwanena mu mdima chidzamveka dzuwa likuwala, ndipo zimene mwanongʼona mʼkhutu mʼchipinda chamʼkati, zidzayankhulidwa pa denga la nyumba.

4“Ine ndikuwuzani, abwenzi anga, musachite mantha ndi amene amapha thupi chifukwa akatero sangachitenso kanthu. 5Koma Ine ndidzakuonetsani amene muyenera kumuopa: Wopani Iye, amene pambuyo pakupha thupi, ali ndi mphamvu yakukuponyani ku gehena. Inde, Ine ndikuwuzani, muopeni Iye. 6Kodi atimba asanu samagulidwa ndi ndalama ziwiri? Ngakhale zili chomwecho palibe imodzi ya izo imene imayiwalika ndi Mulungu. 7Ndithudi, tsitsi lonse la mʼmutu mwanu ndi lowerengedwa. Musachite mantha; inu ndi oposa kwambiri mpheta zambiri.

8“Ine ndikukuwuza kuti, aliyense amene avomereza Ine pamaso pa anthu, Mwana wa Munthu adzamuvomerezanso pamaso pa angelo a Mulungu. 9Koma iye amene andikana Ine pamaso pa anthu adzakanidwanso pamaso pa angelo a Mulungu. 10Ndipo aliyense amene ayankhulira Mwana wa Munthu mawu oyipa adzakhululukidwa, koma iye wochitira mwano Mzimu Woyera sadzakhululukidwa.

11“Akadzakutengerani ku masunagoge pamaso pa oweruza ndi a maulamuliro, musadere nkhawa mmene mudzadzitchinjirizire nokha kapena chimene mudzayankhule, 12pakuti Mzimu Woyera nthawi imeneyo adzakuphunzitsani zoyenera kunena.”

Fanizo la Munthu Wachuma Wopusa

13Munthu wina mʼgulu la anthu anati kwa Iye, “Aphunzitsi, muwuzeni mʼbale wanga andigawireko chuma chamasiye.”

14Yesu anayankha kuti, “Munthu iwe, ndani anandiyika Ine kukhala woweruza kapena wogawa chuma pakati panu?” 15Kenaka Iye anawawuza kuti, “Chenjerani! Khalani tcheru ndi makhalidwe onse adyera; moyo wa munthu sukhala chifukwa cha kuchuluka kwa zimene ali nazo.”

16Ndipo Iye anawawuza fanizo ili, “Munda wa munthu wina wachuma unabereka kwambiri. 17Iye anaganiza kuti, ‘Ndichite chiyani? Ndilibe malo osungiramo mbewu zanga.’

18“Ndipo Iye anati, ichi ndi chimene ndidzachite: Ndidzaphwasula nkhokwe zanga zonse ndi kumanga zokulirapo, ndipo ndidzasungira mʼmenemo mbewu ndi katundu. 19Ndipo ndidzawuza moyo wanga kuti, ‘Uli nazo zinthu zabwino zambiri zimene zikhalepo zaka zambiri, usapupulume; idya, imwa ndi kukondwera.’ ”

20“Koma Mulungu anati kwa iye, ‘Iwe wopusa! Usiku womwe uno moyo wako udzachotsedwa kwa iwe, ndipo ndi ndani amene adzatenge zimene iwe wadzikonzera?’

21“Umu ndi mmene zidzakhalire ndi aliyense amene amadziwunjikira chuma, koma si wachuma pamaso pa Mulungu.”

Musadere Nkhawa

22Kenaka Yesu anati kwa ophunzira ake, “Choncho Ine ndikuwuzani kuti musadere nkhawa za moyo wanu, zimene mudzadya; kapena za thupi lanu, zimene mudzavala. 23Moyo uposa chakudya, ndi thupi liposa chovala. 24Taonani makwangwala: iwo safesa kapena kukolola, alibe nyumba zosungamo zinthu kapena nkhokwe; komabe, Mulungu amawadyetsa. Koposa kotani inu amene ndi ofunikira kuposa mbalame. 25Ndi ndani wa inu akhoza kuwonjeza ora pa moyo wake chifukwa cha kudandaula? 26Popeza simungathe kuchita kanthu kakangʼono aka, nʼchifukwa chiyani mumadandaula ndi zinazi?

27“Taonani mmene maluwa amakulira. Iwo sagwira ntchito kapena kusoka zovala. Koma Ine ndikuwuzani kuti, ngakhale Solomoni muulemelero wake wonse sanavalepo ngati limodzi la awa. 28Ngati umu ndi mmene Mulungu amavekera udzu wakuthengo, umene lero ulipo ndipo mawa uponyedwa pa moto, nanga Iye adzakuvekani inu motani. Haa! Inu achikhulupiriro chochepa! 29Ndipo musayike mtima wanu pa zimene mudzadye kapena kumwa; musade nazo nkhawa. 30Pakuti anthu akunja amathamanga kufunafuna zinthu zotere, ndipo Atate amadziwa kuti mumazifuna zimenezi. 31Koma funafunani ufumu wake, ndipo mudzapatsidwa zonsezi.

Chuma cha Kumwamba

32“Musachite mantha, inu kagulu kankhosa, pakuti zinakondweretsa Atate anu kuti akupatseni ufumu. 33Gulitsani zonse zimene muli nazo, ndipo ndalama zake mupereke kwa osauka. Dzipezereni zikwama zandalama zimene sizidzatha, ndi kudzikundikira chuma chomwe sichidzatha kumwamba, kumene mbala sizingafikeko, ndipo dzimbiri silingawononge. 34Popeza kumene kuli chuma chanu, mtima wanunso udzakhala komweko.”

Kukhala a Atcheru

35“Khalani okonzekeratu ndipo nyale zanu ziziyaka, 36ngati anthu oyembekezera kubwera kwa mbuye wawo kuchokera kuphwando la ukwati, kuti pamene afika ndi kugogoda akhoza nthawi yomweyo kumutsekulira chitseko. 37Zidzakhala bwino kwa antchitowo amene mbuye wawo pobwera adzawapeze akudikira. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti adzakonzekera kuwatumikira, adzakhala nawo pa tebulo ndipo adzabwera ndi kuwatumikira. 38Zidzakhala bwino kwa antchitowo amene mbuye wawo adzawapeze ali okonzeka, ngakhale iye atabwera pa ora lachiwiri kapena lachitatu usiku. 39Koma zindikirani izi: Ngati mwini nyumba akanadziwa ora limene mbala ibwera, sakanalola kuti nyumba yake ithyoledwe. 40Inunso muyenera kukhala okonzeka, chifukwa Mwana wa Munthu adzabwera pa ora limene simukumuyembekezera Iye.”

Wantchito Wokhulupirika ndi Wosakhulupirika

41Petro anafunsa kuti, “Kodi mukunena fanizoli kwa ife, kapena kwa aliyense?”

42Ambuye anayankha kuti, “Kodi tsono woyangʼanira wokhulupirika ndi wanzeru ndani? Kodi ndi amene mbuye wake wamuyika kukhala oyangʼanira antchito ake kuti aziwapatsa ndalama yachakudya pa nthawi yake yoyenera? 43Zidzamukhalira bwino wantchito amene mbuye wake adzamupeza akuchita zimene pamene iye abwera. 44Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti adzamuyika kukhala woyangʼanira katundu wake yense. 45Koma tiyerekeze kuti wantchitoyo aziganiza mu mtima mwake kuti, ‘Bwana wanga akuchedwa kwambiri kubwera,’ ndipo kenaka ndi kuyamba kumenya antchito aamuna ndi aakazi ndi kudya, kumwa ndi kuledzera. 46Mbuye wake adzabwera tsiku limene iye sakumuyembekezera ndi ora limene iye sakudziwa. Iye adzamulanga ndi kumusiya kumalo kumene kuli osakhulupirira.

47“Wantchito amene amadziwa chifuniro cha mbuye wake koma wosakonzeka kapena wosachita chimene mbuye wake akufuna adzakwapulidwa zikwapu zambiri. 48Koma wantchito amene sadziwa koma nʼkuchita zinthu zoyenera chilango, adzakwapulidwa zikwapu zochepa. Aliyense amene anapatsidwa zambiri, adzayenera kubwezanso zambiri; ndipo amene anamusungitsa zambiri, adzamulamula kuti abweze zambirinso.”

Za Kugawikana

49“Ine ndabwera kudzayatsa moto pa dziko lapansi, ndipo ndikanakonda ukanayaka kale. 50Koma Ine ndiyenera kubatizidwa, ndipo ndikusautsika mu mtima mpaka utachitika! 51Kodi mukuganiza kuti Ine ndinabwera kudzabweretsa mtendere pa dziko lapansi? Ayi, Ine ndikukuwuzani kuti, ndinabweretsa kugawikana. 52Kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo mʼbanja limodzi mudzakhala anthu asanu ndipo adzawukirana wina ndi mnzake, atatu kuwukira awiri, ndipo awiri kuwukira atatu. 53Anthu adzawukirana. Abambo kudzawukira mwana wawo wamwamuna, mwana wawoyo adzawukira abambo ake. Amayi adzawukira mwana wawo wamkazi, mwana wawoyo adzawukira amayi ake. Amayi adzawukira mpongozi wawo wamkazi, mpongoziyo adzawukira amayiwo.”

Kumasulira Nthawi

54Iye anati kwa gulu la anthu, “Pamene mukuona mtambo ukukwera kummawa, nthawi yomweyo inu mumati, ‘kugwa mvula,’ ndipo imagwadi. 55Ndipo pamene mphepo yakummwera ikuwomba, inu mumati ‘kutentha’ ndipo kumaterodi. 56Achiphamaso inu! Inu mumadziwa kutanthauzira maonekedwe a dziko lapansi ndi thambo. Zikutheka bwanji kuti simukudziwa kumasulira kwa nthawi ino?

57“Bwanji simukuzindikira nokha zoyenera kuchita? 58Pamene mukupita kwa woweruza ndi amene munalakwirana naye, yesetsani kwambiri kuti muyanjane naye mʼnjiramo, chifukwa mukapanda kutero akhoza kukutengerani ku bwalo la milandu ndipo woweruzayo adzakuperekani kwa woyangʼanira ndende, ndipo woyangʼanira ndendeyo adzakuponyani mʼndende. 59Ine ndikuwuzani kuti, simudzatulukamo mpaka mutalipira ndalama zonse.”