Salmo 48 – CST & CCL

Nueva Versión Internacional (Castilian)

Salmo 48:1-14

Salmo 48

Canción. Salmo de los hijos de Coré.

1Grande es el Señor, y digno de suprema alabanza

en la ciudad de nuestro Dios.

Su monte santo, 2bella colina,

es la alegría de toda la tierra.

El monte Sión, en la parte norte,

es la ciudad del gran Rey.

3En las fortificaciones de Sión

Dios se ha dado a conocer como refugio seguro.

4Hubo reyes que unieron sus fuerzas

y que juntos avanzaron contra la ciudad;

5pero al verla quedaron pasmados,

y asustados emprendieron la retirada.

6Allí el miedo se apoderó de ellos,

y un dolor de parturienta les sobrevino.

7¡Con un viento huracanado

destruiste las naves de Tarsis!

8Tal como lo habíamos oído,

ahora lo hemos visto

en la ciudad del Señor Todopoderoso,

en la ciudad de nuestro Dios:

¡Él la hará permanecer para siempre! Selah

9Dentro de tu templo, oh Dios,

meditamos en tu gran amor.

10Tu alabanza, oh Dios, como tu nombre,

llega a los confines de la tierra;

tu derecha está llena de justicia.

11A causa de tus justas decisiones

el monte Sión se alegra

y las aldeas de Judá se regocijan.

12Caminad alrededor de Sión,

caminad en torno a él

y contad sus torres.

13Observad bien sus murallas

y examinad sus fortificaciones,

para que se lo cuenten a las generaciones futuras.

14¡Este Dios es nuestro Dios eterno!

¡Él nos guiará para siempre!48:14 para siempre (LXX); sobre muerte (TM).

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 48:1-14

Salimo 48

Nyimbo. Salimo la ana a Kora.

1Wamkulu ndi Yehova, ndi woyenera kwambiri matamando

mu mzinda wa Mulungu wathu, phiri lake loyera.

2Lokongola mu utali mwake,

chimwemwe cha dziko lonse lapansi.

Malo aatali kwambiri a Zafoni ndiye Phiri la Ziyoni,

mzinda wa Mfumu yayikulu.

3Mulungu ali mu malinga ake;

Iye wadzionetsa yekha kuti ndiye malinga akewo.

4Pamene mafumu anasonkhana pamodzi,

pamene anayendera pamodzi kudzalimbana nafe,

5iwo anaona mzindawo ndipo anadabwa kwambiri;

anathawa ndi mantha aakulu.

6Pomwepo anagwidwa nako kunjenjemera,

ululu wonga wa mkazi woyembekezera pa nthawi yochira.

7Inu munawawononga monga sitima zapamadzi za ku Tarisisi

zitawonongeka ndi mphepo ya kummawa.

8Monga momwe tinamvera,

kotero ife tinaona

mu mzinda wa Yehova Wamphamvuzonse,

mu mzinda wa Mulungu wathu.

Mulungu adzawuteteza kwamuyaya.

9Mʼkati mwa Nyumba yanu Mulungu,

ife timalingaliramo zachikondi chanu chosasinthika.

10Monga dzina lanu, Inu Mulungu,

matamando anu amafika ku malekezero a dziko lapansi

dzanja lanu lamanja ladzaza ndi chilungamo.

11Phiri la Ziyoni likukondwera,

midzi ya Yuda ndi yosangalala

chifukwa cha maweruzo anu.

12Yendayendani mu Ziyoni, uzungulireni mzindawo,

werengani nsanja zake.

13Yangʼanitsitsani bwino mipanda yake,

penyetsetsani malinga ake,

kuti mudzafotokoze za izo ku mʼbado wotsatira.

14Pakuti Mulungu uyu ndi Mulungu wathu ku nthawi zosatha;

Iye adzakhala mtsogoleri wathu mpaka ku mapeto.