Job 29 – CST & CCL

Nueva Versión Internacional (Castilian)

Job 29:1-25

Soliloquio de Job

1Job, retomando la palabra, dijo:

2«¡Cómo añoro los meses que se han ido,

los días en que Dios me cuidaba!

3Su lámpara alumbraba sobre mi cabeza,

y por su luz podía andar entre tinieblas.

4¡Qué días aquellos, cuando yo estaba en mi apogeo

y Dios bendecía mi casa con su íntima amistad!

5»Cuando aún estaba conmigo el Todopoderoso,

y mis hijos me rodeaban;

6cuando ante mí corrían ríos de crema,

y de las rocas fluían arroyos de aceite;

7cuando ocupaba mi puesto en el concejo de la ciudad,29:7 cuando ocupaba … ciudad. Lit. cuando salía yo a las puertas de la ciudad.

y en la plaza pública tomaba asiento,

8los jóvenes al verme se hacían a un lado,

y los ancianos se ponían de pie;

9los jefes se abstenían de hablar

y se tapaban la boca con las manos;

10los nobles bajaban la voz,

y la lengua se les pegaba al paladar.

11Los que me oían, hablaban bien de mí;

los que me veían, me alababan.

12Si el pobre recurría a mí, yo lo ponía a salvo,

y también al huérfano si no tenía quien lo ayudara.

13Me bendecían los desahuciados;

¡por mí gritaba de alegría

el corazón de las viudas!

14De justicia y rectitud me revestía;

ellas eran mi manto y mi turbante.

15Para los ciegos fui sus ojos;

para los tullidos, sus pies.

16Fui padre de los necesitados

y defensor de los extranjeros.

17A los malvados destroné;

¡de sus fauces les arrebaté la presa!

18»Llegué a pensar: “Moriré en mi propia casa;

mis días serán incontables como la arena del mar.

19Mis raíces llegarán hasta las aguas;

el rocío de la noche se quedará en mis ramas.

20Mi gloria mantendrá en mí su lozanía,

y el arco en mi mano se mantendrá firme”.

21»La gente me escuchaba expectante,

y en silencio aguardaba mi consejo.

22Hablaba yo, y nadie replicaba;

mis palabras hallaban cabida29:22 hallaban cabida. Lit. caían como gotas. en sus oídos.

23Expectantes, absorbían mis palabras

como quien espera las lluvias tardías.

24Si yo les sonreía, no podían creerlo;

mi rostro sonriente los reanimaba.29:24 mi rostro … reanimaba. Lit. la luz de mi rostro no los hacía caer.

25Yo les indicaba el camino a seguir;

me sentaba a la cabecera;

habitaba entre ellos como un rey entre su tropa,

como quien consuela a los que están de luto.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yobu 29:1-25

1Yobu anapitiriza kuyankhula kwake:

2“Aa! Ndikanakhala momwe ndinalili miyezi yapitayi,

masiku amene Mulungu ankandiyangʼanira,

3pamene nyale yake inkandiwunikira

ndipo ndi kuwunika kwakeko ine ndinkatha kuyenda mu mdima!

4Ndithu, masiku amene ndinali pabwino kwambiri,

pamene ubwenzi wa Mulungu unkabweretsa madalitso pa nyumba yanga,

5nthawi imene Wamphamvuzonse anali nane,

ndipo ana anga anali atandizungulira mʼmbalimu,

6pamene popondapo ine panali patakhathamira mafuta a mkaka,

ndipo pa thanthwe pamatuluka mitsinje ya mafuta a olivi.

7“Pamene ndinkapita pa chipata cha mzinda

ndi kukhala pa mpando wanga pabwalo,

8anyamata amati akandiona ankapatuka

ndipo anthu akuluakulu ankayimirira;

9atsogoleri ankakhala chete

ndipo ankagwira pakamwa pawo;

10anthu otchuka ankangoti duu,

ndipo malilime awo anali atamatirira ku nkhama zawo.

11Aliyense amene anamva za ine anayankhula zabwino zanga,

ndipo iwo amene anandiona ankandiyamikira,

12chifukwa ndinkapulumutsa mʼmphawi wofuna chithandizo,

ndiponso mwana wamasiye amene analibe aliyense womuthandiza.

13Munthu amene anali pafupi kufa ankandidalitsa;

ndinkasangalatsanso mkazi wamasiye.

14Chilungamo chinali ngati chovala changa;

chiweruzo cholungama ndiye chinali mkanjo ndi nduwira yanga.

15Ndinali ngati maso kwa anthu osapenya;

ndinali ngati mapazi kwa anthu olumala.

16Ndinali ngati abambo kwa anthu aumphawi;

ndinkayimira mlendo pa mlandu wake.

17Ndinkawononga mphamvu za anthu oyipa

ndi kulanditsa amene anali atagwidwa.

18“Ndinkaganiza kuti, ‘Ndidzafera mʼnyumba yanga,

masiku a moyo wanga ali ochuluka ngati mchenga.

19Mizu yanga idzatambalalira ku madzi,

ndipo mame adzakhala pa nthambi zanga usiku wonse.

20Ulemerero wanga udzakhala wosaguga mwa ine,

ndipo uta wanga udzakhala watsopano nthawi zonse mʼdzanja langa.’

21“Anthu ankamvetsera zimene ndinkanena mwachidwi,

ankadikira atakhala chete kuti amve malangizo anga.

22Ndikayankhula, iwo sankayankhulanso;

mawu anga ankawagwira mtima.

23Ankayembekezera ine monga momwe amayembekezera mvula

ndipo ankalandira mawu anga ngati mvula ya mʼmalimwe.

24Ndikawasekerera, iwo sankatha kukhulupirira;

kuwala kwa nkhope yanga chinali chinthu chamtengowapatali kwa iwowo.

25Ndinkawasankhira njira yawo ndipo ndinkawatsogolera ngati mfumu;

ndinkakhala ngati mfumu pakati pa gulu lake lankhondo;

ndinali ngati msangalatsi pakati pa anthu olira.”