Zekariya 5 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Zekariya 5:1-11

Chikalata Chowuluka

1Ndinayangʼananso ndipo taonani ndinaona chikalata chimene chimawuluka.

2Mngelo uja anandifunsa kuti, “Kodi ukuona chiyani?”

Ndinayankha kuti, “Ndikuona chikalata chikuwuluka, mulitali mwake mamita asanu ndi anayi ndipo mulifupi mwake mamita anayi ndi theka.”

3Ndipo mngeloyo anandiwuza kuti, “Awa ndi matemberero amene akupita pa dziko lonse lapansi; potsata zimene zalembedwa mʼkati mwa chikalatamo, aliyense wakuba adzachotsedwa, ndipo potsata zomwe zalembedwa kunja kwake, aliyense wolumbira zabodza adzachotsedwanso. 4Yehova Wamphamvuzonse akunena kuti, ‘Temberero limeneli ndidzalitumiza, ndipo lidzalowa mʼnyumba ya munthu wakuba ndi munthu wolumbira zabodza mʼdzina langa. Lidzakhala mʼnyumbamo mpaka kuyiwonongeratu, matabwa ake ndi miyala yake yomwe.’ ”

Mkazi mu Dengu

5Kenaka mngelo amene amayankhula nane uja anabwera patsogolo panga ndipo anandiwuza kuti, “Kweza maso ako tsopano kuti uwone kuti ndi chiyani chikubwerachi.”

6Ndinafunsa kuti, “Kodi chimenechi nʼchiyani?”

Mngeloyo anayankha kuti, “Limeneli ndi dengu loyezera.” Ndipo anawonjezera kunena kuti, “Umenewu ndi uchimo wa anthu mʼdziko lonse.”

7Pamenepo chovundikira chake chamtovu chinatukulidwa, ndipo mʼdengumo munali mutakhala mkazi. 8Mngeloyo anati, “Chimenechi ndi choyipa,” ndipo anamukankhira mkaziyo mʼdengu muja, nabwezera chovundikira chamtovu chija pamwamba pake.

9Kenaka ndinayangʼananso, ndipo ndinaona akazi awiri akuwuluka kubwera kumene kunali ine; akuwuluzika ndi mphepo. Iwo anali ndi mapiko ngati a kakowa, ndipo ananyamula dengu lija, kupita nalo pakati pa mlengalenga ndi dziko lapansi.

10Ine ndinafunsa mngelo amene amayankhula nane kuti, “Dengulo akupita nalo kuti?”

11Iye anayankha kuti, “Ku dziko la Babuloni kuti akalimangire nyumba. Nyumbayo ikadzatha, adzayikamo dengulo.”

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

撒迦利亚书 5:1-11

飞行的书卷

1我又举目观看,见有书卷在飞。 2天使问我:“你看见什么?”我说:“我看见飞行的书卷,长十米,宽五米。” 3他说:“这是临到全天下的咒诅,因为书卷一面写着‘凡偷盗的必被清除’,另一面写着‘凡起假誓的必被清除’。” 4万军之耶和华说:“我要使这咒诅进入盗贼和奉我的名起假誓者的家,住在他们家里,毁灭他们的家,不留一木一石。”

量器中的女子

5与我说话的天使又来对我说:“你举目观看,看看出现了什么?” 6我问道:“这是什么?”他说:“这是一个量器。”接着他又说:“里面盛着世人的罪。” 7只见量器的铅盖打开了,里面坐着一个女子。 8天使说:“这是罪恶。”他把女子推回量器中,盖上铅盖。 9我又举目观看,见有两个女子展翅飞来,她们的翅膀像鹳鸟的翅膀。她们把量器提到空中。 10我问与我说话的天使:“她们要把量器带到哪里?” 11他说:“要带到示拿5:11 示拿”巴比伦的别名。,在那里为它建造房屋,建好后就把它安置在底座上。”