Zekariya 3 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Zekariya 3:1-10

Zovala Zoyera za Mkulu wa Ansembe

1Pamenepo anandionetsa Yoswa, mkulu wa ansembe, atayima pamaso pa mngelo wa Yehova, ndipo Satana anayima ku dzanja lake lamanja kuti atsutsane naye. 2Yehova anawuza Satana kuti, “Yehova akukudzudzula iwe Satana! Yehova amene wasankha Yerusalemu akukudzudzula! Kodi munthu uyu sali ngati chikuni choyaka chofumula pa moto?”

3Tsono Yoswa anali atavala zovala zalitsiro pa nthawi imene anayima pamaso pa mngelo. 4Mngelo uja anawuza anzake amene anali naye kuti, “Muvuleni zovala zake zalitsirizo.”

Kenaka anawuza Yoswa kuti, “Taona, ndachotsa tchimo lako, ndipo ndikuveka zovala zokongola.”

5Ndipo ine ndinati, “Muvekeni nduwira yopatulika pamutu pake.” Choncho anamuveka nduwira yopatulika pamutu pake, namuvekanso zovala zatsopano. Nthawiyi nʼkuti mngelo wa Yehova atayima pambali.

6Mngelo wa Yehova analimbikitsa Yoswa kuti, 7“Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Ngati uyenda mʼnjira zanga ndi kusunga malamulo anga, pamenepo udzalamulira nyumba yanga ndi kuyangʼanira mabwalo anga, ndipo ndidzakulolani kuti mudzakhale pamodzi ndi amene ali panowa.

8“ ‘Mvera tsono, iwe Yoswa mkulu wa ansembe, pamodzi ndi anzako amene wakhala nawowa, amene ndi chizindikiro cha zinthu zimene zikubwera: Ine ndidzabweretsa mtumiki wanga, wotchedwa Nthambi. 9Taona, mwala wokongola umene ndayika patsogolo pa Yoswa! Pa mwala umenewu pali maso asanu ndi awiri, ndipo Ine ndidzalembapo mawu,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse, ‘ndipo ndidzachotsa tchimo la dziko lino tsiku limodzi.

10“ ‘Tsiku limenelo aliyense adzayitana mnzake kuti akhale pansi pa mtengo wamphesa ndi wa mkuyu,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.”

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

撒迦利亚书 3:1-10

约书亚大祭司

1耶和华又让我看见约书亚大祭司站在祂的天使面前,撒旦站在约书亚的右边要控诉他。 2耶和华对撒旦说:“撒旦啊,耶和华斥责你!拣选耶路撒冷的耶和华斥责你!这人岂不像从火中抽出来的一根柴吗?” 3那时,约书亚穿着污秽的衣服站在天使面前。 4天使对侍立在周围的说:“脱掉他污秽的衣服。”他又对约书亚说:“看啊,我已除掉你的罪,我要给你穿上华美的衣服。”

5我说:“要给他戴上洁净的礼冠。”他们便给他戴上洁净的礼冠、穿上华美的衣服。那时,耶和华的天使站在旁边。

6耶和华的天使告诫约书亚7“万军之耶和华说,‘你若遵行我的道,谨守我的吩咐,便可以管理我的家,看守我的院宇。我必让你在这些侍立的天使中间自由出入。 8约书亚大祭司啊,你和坐在你面前的同伴们听着,你们都是将来之事的预兆——我将使我仆人大卫的苗裔兴起。 9看啊,这是我在约书亚面前安置的石头,它有七眼3:9 ”或作“面”。,我要在上面刻上字,并在一天之内除掉这地方的罪。这是万军之耶和华说的。 10到那天,你们将各自邀请邻居坐在葡萄树和无花果树下。这是万军之耶和华说的。’”