Zekariya 2 – CCL & AKCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Zekariya 2:1-13

Munthu ndi Chingwe Choyezera

1Kenaka ndinayangʼananso, ndipo ndinaona munthu atanyamula chingwe choyezera mʼmanja mwake. 2Ndipo ndinafunsa kuti, “Kodi ukupita kuti?”

Anandiyankha kuti, “Akukayeza Yerusalemu kuti ndidziwe mulifupi mwake ndi mulitali mwake.”

3Taonani, mngelo amene amayankhula nane uja akuchoka, mngelo wina anabwera kudzakumana naye 4ndipo anamuwuza kuti, “Thamanga, kamuwuze mnyamatayo kuti, ‘Yerusalemu udzakhala mzinda wopanda malinga chifukwa mudzakhala anthu ambiri ndiponso ziweto zochuluka. 5Ndipo Ine mwini ndidzakhala linga lamoto kuteteza mzindawo,’ akutero Yehova, ‘ndipo ndidzakhala ulemerero mʼkati mwake.’

6“Tulukani! Tulukani! Thawaniko ku dziko la kumpoto,” akutero Yehova, “pakuti ndinakumwazirani ku mphepo zinayi zamlengalenga,” akutero Yehova.

7“Tuluka, iwe Ziyoni! Thawa, iwe amene umakhala mʼdziko la mwana wamkazi wa Babuloni!” 8Pakuti Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Atatha kundilemekeza wanditumiza kwa anthu a mitundu ina amene anakufunkhani; pakuti aliyense wokhudza inu wakhudza mwanadiso wanga. 9Ndithu Ine ndidzawamenya anthuwo ndi dzanja langa ndipo amene anali akapolo awo ndiye adzawalande zinthu. Pamenepo mudzadziwa kuti Yehova Wamphamvuzonse ndiye wandituma.

10“Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni, fuwula ndipo sangalala. Pakuti taona ndikubwera, ndipo ndidzakhala pakati pako,” akutero Yehova. 11“Nthawi imeneyo anthu a mitundu yambiri adzabwera kwa Yehova ndipo adzasanduka anthu anga. Ndidzakhala pakati pako ndipo iwe udzadziwa kuti Yehova Wamphamvuzonse wandituma kwa iwe. 12Yehova adzachititsa kuti Yuda akhale chuma chake mʼdziko lopatulika ndipo adzasankhanso Yerusalemu. 13Khalani chete pamaso pa Yehova anthu nonse, chifukwa Iye wavumbuluka kuchoka ku malo ake opatulika.”

Akuapem Twi Contemporary Bible

Sakaria 2:1-13

Onipa A Okura Susuhama No

1Afei memaa mʼani so, na mihuu ɔbarima bi a okura susuhama sɛ ogyina mʼanim! 2Mibisaa no se, “Ɛhe na worekɔ?” Obuae se, “Merekosusuw Yerusalem, ahu ne trɛw ne ne tenten.”

3Na ɔbɔfo a na ɔne me rekasa na kɔe, na ɔbɔfo foforo behyiaa no 4na ɔka kyerɛɛ no se, “Tu mmirika, ka kyerɛ saa aberante no se, ‘Yerusalem bɛyɛ kuropɔn a enni afasu esiane nnipa ne mmoa dodow a wɔwɔ mu nti. 5Na mʼankasa mɛyɛ ogya fasu, atwa ho ahyia,’ sɛnea Awurade se ni, ‘na mayɛ ne mu anuonyam.’

6“Mommra! Mommra! Munguan mfi atifi asase no so,” sɛ Awurade se ni, “Na mahwete mo mu ama ɔsoro mframa anan no,” sɛnea Awurade se ni.

7“Mommra, Sion! Munguan, mo a mote Ɔbabea Babilonia!” 8Efisɛ sɛɛ na Asafo Awurade se, “Onuonyamfo no asoma me akotia aman a wɔafow mo nneɛma no akyi no, nea ɔde ne nsa bɛka mo biara no de nsa aka AWURADE aniwa nkesua. 9Nokware, mɛma me nsa so de atia wɔn sɛnea ɛbɛyɛ a wɔn nkoa bɛfom wɔn nneɛma. Na ɛbɛma moahu sɛ Asafo Awurade na wasoma me.

10“Teɛ mu na ma wʼani nnye, Ɔbabea Sion. Efisɛ, mereba, na mene mo bɛtena,” sɛnea Awurade se ni. 11“Aman bebree bɛka Awurade ho saa da no na wɔabɛyɛ me nkurɔfo. Me ne mo bɛtena, na mubehu sɛ, Asafo Awurade na wasoma me mo nkyɛn. 12Awurade bɛfa Yuda sɛ nʼagyapade wɔ asase kronkron no so, na ɔbɛfa Yerusalem bio. 13Monyɛ komm wɔ Awurade anim, adesamma nyinaa, efisɛ wakanyan ne ho wɔ ne tenabea kronkron hɔ.”