Yoswa 20 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yoswa 20:1-9

Mizinda Yopulumukiramo

1Pambuyo pake Yehova anati kwa Yoswa: 2“Uza Aisraeli kuti apatule mizinda yopulumukiramo, monga ine ndinakulangizira kudzera mwa Mose, 3kuti aliyense amene wapha munthu mosazindikira osati mwadala azithawirako. Motero adzatetezedwa kwa wolipsira. 4Ngati munthu wathawira ku umodzi mwa mizinda imeneyi, akafike pa malo oweruzira milandu amene ali pa chipata cha mzindawo ndipo akafotokoze mlandu wake pamaso pa akuluakulu a mzindawo. Kenaka iwo adzamulola kulowa mu mzinda wawo ndi kumupatsa malo woti akhale nawo. 5Ngati munthu wolipsirayo amutsatira komweko atsogoleriwo asapereke munthu wakuphayo chifukwa anapha Mwisraeli mnzakeyo mosazindikira, osati mwachiwembu. 6Munthu wakuphayo adzakhalabe mu mzindawo mpaka atayimbidwa mlandu pamaso pa gulu lonse, ndiponso mpaka atamwalira mkulu wa ansembe amene akutumikira pa nthawiyo. Pamenepo munthuyo atha kubwereranso ku mudzi kwawo kumene anachoka mothawa kuja.”

7Choncho iwo anapatula Kedesi mʼdera la Galileya ku mapiri a Nafutali, Sekemu ku mapiri a Efereimu, ndi Kiriati Ariba (ndiye Hebroni) ku mapiri a Yuda. 8Kummawa kwa Yorodani, mʼmapiri a chipululu a kummawa kwa Yeriko, anapatula Bezeri pakati pa dera la fuko la Rubeni. Anapatulanso Ramoti ku Giliyadi mʼdera la fuko la Gadi, ndiponso Golani ku Basani mʼdera la fuko la Manase. 9Imeneyi ndiyo inali mizinda yopulumukiramo ya Aisraeli onse ngakhalenso mlendo wokhala pakati pawo. Munthu aliyense wopha mnzake mwangozi ankathawira ku mizinda imeneyi. Munthu wolipsira sankaloledwa kuti aphe munthu wothawayo ngati mlandu wake sunazengedwe pamaso pa gulu lonse.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

约书亚记 20:1-9

避难城

1耶和华对约书亚说: 2“你吩咐以色列人,照我以前借摩西所吩咐你们的,设立一些城邑作为避难城, 3好让那些误杀了人的可以逃到那里,免遭仇人追杀。 4逃进城的人要先站在城门口,向避难城的长老陈明事情的经过,长老就把他们收容到城里,给他们地方住。 5如果他们的仇人追到,长老们不可把他们交出来,因为他们是无意杀的,跟被杀者无冤无仇。 6这些人要住在城内,直到在会众面前受了审讯,并且还要等到在任的大祭司死后,才可离城回乡。”

7于是,民众便设立拿弗他利山区加利利境内的基低斯以法莲山区的示剑犹大山区的基列·亚巴,即希伯仑作为避难城。 8他们又在约旦河、耶利哥东面空旷的平原上设立吕便支派的比悉迦得支派基列境内的拉末玛拿西支派巴珊境内的哥兰作为避难城。 9这是为以色列人和那些从外地来寄居的人所设立的避难城,误杀了人的可以逃到那里,不致未在会众面前受审便死在报仇的人手里。