Yoswa 13 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yoswa 13:1-33

Mayiko Otsala Oyenera Kulandidwa

1Yoswa atakalamba Yehova anamuwuza kuti, Iwe tsopano wakalamba kwambiri, koma dziko losalandidwa lilipobe lalikulu.

2“Madera amene atsala ndi awa: chigawo chonse cha Afilisti ndi Agesuri 3kuchokera ku mtsinje wa Sihori kummawa kwa Igupto mpaka kumpoto kwa dziko la Ekroni. Madera onse amawerengedwa kuti ndi a Akanaani ngakhale amalamulidwa ndi mafumu asanu a Afilisti a ku Gaza, Asidodi, Asikeloni, Gati, Ekroni ndi Agiti, komanso ku Avimu ku chigawo cha kumpoto. 4Dziko lina la Akanaani ndi Ameara limene lili mʼmanja mwa Asidoni mpaka ku Afeki, dziko limene linachitana malire ndi dziko la Aamori. 5Palinso dziko lonse la Gebala ndi Lebanoni cha kummawa kuyambira ku Baala-Gadi pa tsinde pa phiri la Herimoni mpaka ku Lebo Hamati.

6“Palinso anthu okhala mʼchigawo cha ku mapiri kuchokera ku Lebanoni mpaka ku Misirefoti-Maimu, Ine ndidzawapirikitsa pamene Aisraeli azidzalowa. Tsono uwagawire Aisraeli dziko limeneli kuti likhale cholowa chawo monga momwe ndakulamulira. 7Tsopano ugawire dziko limeneli mafuko asanu ndi anayi ndiponso theka la fuko la Manase, kuti likhale cholowa chawo.”

Kugawidwa kwa Dziko la Kummawa kwa Yorodani

8Anthu a fuko la Rubeni ndi fuko la Gadi pamodzi ndi theka lina la fuko la Manase analandira kale cholowa chawo chimene Mose mtumiki wa Yehova anawapatsa. Cholowa chawocho chinali kummawa kwa mtsinje wa Yorodani.

9Dziko lawolo linayambira ku Aroeri mzinda umene uli pafupi ndi chigwa cha Arinoni, ndiponso mzinda umene uli pakati pa chigwacho. Dzikolo linkaphatikizanso dera lonse lokwera kuyambira ku Medeba mpaka ku Diboni. 10Linkaphatikizanso mizinda yonse ya mfumu Sihoni ya Aamori, imene inkalamulira mu Hesiboni, mpaka ku malire a Aamoni. 11Dzikoli linaphatikizanso Giliyadi, dziko la anthu a ku Gesuri ndi Maaka, phiri lonse la Herimoni ndi dziko lonse la Basani mpaka ku Saleka. 12Linaphatikizanso dziko la mfumu Ogi ya ku Basani imene imalamulira kuchokera ku Asiteroti ndi Ederi. Iye yekha ndiye anali mfumu ya Arefaimu amene anapulumuka. Mose anali atawagonjetsa anthu amenewa ndi kuwathamangitsira kutali. 13Koma Aisraeli sanathamangitse anthu a ku Gesuri ndi Maaka, kotero iwowa amakhalabe pakati pawo mpaka lero.

14Koma Mose sanapereke dziko kwa fuko la Alevi popeza zopereka zopatulika zimene anthu ankapereka kwa Yehova, Mulungu wa Israeli, ndizo zinali cholowa chawo monga Yehova anawalonjezera.

15Mose anapereka gawo lina la dziko kwa mabanja a fuko la Rubeni.

16Dziko lawo linayambira ku Aroeri mzinda umene uli pafupi ndi chigwa cha Arinoni, mʼmudzi wa pakati pa chigwa, ndiponso dera lonse lokwera mpaka ku Medeba. 17Dzikolo linaphatikizanso Hesiboni ndi mizinda yake yonse, komanso mizinda monga Diboni, Bamoti Baala, Beti-Baala-Meoni, 18Yahaza, Kedemoti, Mefaati. 19Kiriataimu, Sibima, Zereti-Sahari, pa phiri limene lili mʼchigwa, 20Beti-Peori, ku matsitso a Pisiga, ndiponso Beti-Yesimoti. 21Dzikolo linaphatikizanso mizinda yonse ya ku madera okwera ndiponso dziko lonse la mfumu Sihoni ya Aamori amene ankalamulira kuchokera ku Hesiboni. Mose anamugonjetsa iye pamodzi ndi mafumu a Amidiyani awa: Evi, Rekemu, Zuri, Huri ndi Reba, mafumu amene anagwirizana ndi Sihoni. Onsewa analamulira dzikolo ngati nduna za Sihoni. 22Kuwonjezera pa amene anaphedwa ndi nkhondo, Aisraeli anapha ndi lupanga Balaamu mwana wa Beori, amene amachita za matsenga. 23Malire a fuko la Rubeni anali mtsinje wa Yorodani. Mizinda imeneyi pamodzi ndi midzi yake zinapatsidwa kwa mabanja a fuko la Rubeni kuti akhale cholowa chawo.

24Dera limene Mose anapereka kwa mabanja a fuko la Gadi ndi ili:

25Dziko la Yazeri, mizinda yonse ya mu Giliyadi ndiponso theka la dziko la Amori kukalekezera ku Aroeri, kufupi ndi Raba; 26ndiponso kuyambira ku Hesiboni mpaka ku Ramati-Mizipa, ndi Betonimu; ndiponso kuyambira ku Mahanaimu mpaka ku dziko la Debri. 27Mu chigwa cha Yorodani analandiramo Beti-Haramu, Beti-Nimira, Sukoti ndi Zafoni pamodzi ndi dziko lonse la mfumu Sihoni ya ku Hesiboni. Malire ake a ku madzulo anali mtsinje wa Yorodani kufikira ku Nyanja ya Kinereti, kumpoto. 28Mizinda ndi midzi imeneyi inali cholowa cha mabanja a fuko la Gadi.

29Mose anali atapereka kale gawo lina la dziko limeneli kwa theka la mabanja a fuko la Manase kuti likhale cholowa chawo.

30Derali linayambira ku Mahanaimu kuphatikizapo dziko lonse la mfumu Ogi, Mfumu ya ku Basani, pamodzi ndi mizinda 60 ya ku Yairi, ku Basaniko. 31Derali linaphatikizanso theka la Giliyadi pamodzi ndi Asiteroti ndi Ederi, mizinda yayikulu ya mfumu Ogi wa Basani. Mizinda imeneyi inapatsidwa kwa mabanja a Makiri, mwana wa Manase kuti ikhale cholowa cha theka la ana a Makiri, malinga ndi mabanja awo.

32Umu ndi mmene Mose anagawira malo a mʼchigwa cha Yorodani, kummawa kwa Yeriko, ku tsidya kwa Yorodani. 33Komatu Mose sanapereke malo kwa fuko la Levi. Mose anawawuza kuti zopereka zimene anthu ankapereka kwa Yehova ndizo cholowa chawo.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

约书亚记 13:1-33

尚未攻取之地

1约书亚年事已高,耶和华对他说:“你年纪大了,但还有许多地方有待征服, 2就是非利士人和基述人的全境, 3即从埃及东面的西曷河直到北面以革伦的边境,这一带都算是迦南,是统治迦萨人、亚实突人、亚实基伦人、迦特人、以革伦人的五个非利士王的地方;南方亚卫人的地方; 4整个迦南人的地方,从西顿人的米亚拉直到亚摩利人边境的亚弗5迦巴勒人的地方;以及东从黑门山山麓的巴力·迦得直到哈马口的整个黎巴嫩6我必为以色列人赶走从黎巴嫩米斯利弗·玛音一带山区的西顿人。你只管照我的吩咐,把这些土地分给以色列人作产业, 7分给其他九个支派和玛拿西半个支派作产业。”

约旦河东土地的分配

8玛拿西半个支派和吕便迦得两支派已经得到耶和华的仆人摩西约旦河东分给他们的产业: 9亚嫩谷旁的亚罗珥起,包括谷中的城,直到底本的整个米底巴平原, 10以及希实本亚摩利西宏统治的各城,直到亚扪的边境。 11此外,还包括基列基述人和玛迦人的疆域、整个黑门山和直到撒迦的整个巴珊地, 12以及巴珊的国土。曾经在亚斯她录以得来做王,是仅存的利乏音人。摩西打败了这些人,赶走了他们。 13以色列人却没有赶走基述人和玛迦人,他们到今天还住在以色列人当中。

14摩西并没有把土地分给利未支派作产业,因为献给以色列的上帝耶和华的火祭就是他们的产业,正如耶和华对他们的应许。

15以下是摩西按宗族分给吕便支派的产业: 16亚嫩谷的城、谷旁的亚罗珥米底巴附近的整个平原, 17希实本城和希实本平原的所有城邑,即底本巴末·巴力伯·巴力·勉18雅杂基底莫米法押19基列亭西比玛、谷中山丘上的细列哈·沙辖20伯毗珥毗斯迦山坡和伯·耶西末21平原的各城邑和亚摩利西宏的国土。西宏曾在希实本做王,摩西打败了他和他的米甸首领以未利金苏珥户珥利巴22以色列人所杀的人中有比珥的儿子术士巴兰23吕便支派的土地以约旦河为界。以上是吕便支派按宗族分到的城邑和村庄。

24以下是摩西按宗族分给迦得支派的土地: 25雅谢基列境内所有的城邑;亚扪人的一半领土,直到拉巴附近的亚罗珥26希实本直到拉抹·米斯巴比多宁,从玛哈念底璧的边境; 27还有谷中的伯亚兰伯·宁拉疏割撒分,就是希实本西宏国中其余的土地,以约旦河为界,沿东岸直到加利利海的顶端。 28以上这些城邑、村庄便是迦得支派按宗族所分到的产业。

29以下是摩西按宗族分给玛拿西半个支派的土地: 30玛哈念开始,包括整个巴珊,就是巴珊的国土及其境内雅珥的六十座城邑, 31还有基列的一半和巴珊的两座城——亚斯她录以得来玛拿西的儿子玛吉的一半子孙按宗族分到这些土地。

32以上是摩西耶利哥对面约旦河东的摩押平原分给以色列人的产业。 33摩西并没有分给利未支派任何产业,因为以色列的上帝耶和华就是他们的产业,正如耶和华对他们的应许。