Yohane 9 – CCL & HHH

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yohane 9:1-41

Yesu Achiritsa Munthu Wosaona Chibadwire

1Iye akuyendabe, anaona munthu wosaona chibadwire. 2Ophunzira ake anamufunsa Iye kuti, “Rabi anachimwa ndani, munthuyu kapena makolo ake, kuti iye abadwe wosaona?”

3Yesu anayankha kuti, “Sikuti iyeyu anachimwa kapena makolo ake, koma izi zinachitika kuti Mulungu aonetse ntchito zake mwa iyeyu. 4Ife tiyenera kugwira ntchito za Iye amene anandituma kukanali masana. Usiku ukubwera, pamene wina aliyense sadzagwira ntchito. 5Pamene Ine ndili mʼdziko lapansi, Ine ndine kuwunika kwa dziko lapansi.”

6Atanena izi, Iye anathira malovu pansi ndi kukanda dothi, napaka matopewo mʼmaso a munthuyo. 7Yesu anamuwuza iye kuti, “Pita kasambe mʼdziwe la Siloamu” (mawu awa akutanthauza Wotumidwa). Choncho munthuyo anapita ndi kukasamba ndipo anabwerako akupenya.

8Anzake ndi iwo amene anamuona iye poyamba akupempha anafunsa kuti, “Kodi uyu si munthu amene amapemphapempha uja?” 9Ena ananena kuti anali yemweyo.

Ena anati, “Ayi, sakuoneka ngati yemweyo.”

Koma iye mwini ananenetsa kuti, “Munthuyo ndine.”

10Iwo anafunsitsa kuti, “Kodi nanga maso ako anatsekuka bwanji?”

11Iye anayankha kuti, “Munthu wina wotchedwa Yesu anakanda dothi ndi kupaka mʼmaso anga. Iye anandiwuza kuti ndipite ku Siloamu ndi kukasamba. Choncho ndinapita kukasamba, ndipo ndikuona.”

12Iwo anamufunsa iye kuti, “Ali kuti munthu ameneyu?”

Iye anati, “Ine sindikudziwa.”

Afarisi Afufuza za Kuchiritsidwa Kwake

13Iwo anabwera naye munthu amene poyamba anali wosaona kwa Afarisi. 14Tsono linali la Sabata tsiku limene Yesu anakanda dothi ndi kutsekula maso a munthuyu. 15Choncho Afarisi anamufunsanso iye momwe analandirira kuona kwake. Munthuyo anayankha kuti, “Iye anapaka matope mʼmaso anga, ndipo ine ndinakasamba, ndipo ndikuona.”

16Ena a Afarisi anati, “Munthu uyu siwochokera kwa Mulungu, pakuti sasunga Sabata.”

Koma enanso anafunsa kuti, “Kodi munthu wochimwa angachite bwanji zizindikiro zodabwitsa ngati izi?” Choncho iwo anagawanika.

17Pomaliza iwo anatembenukiranso kwa munthu amene anali wosaona uja nati, “Kodi iwe unena chiyani za Iye poti ndi maso ako amene watsekula?”

Munthuyo anayankha kuti, “Iye ndi mneneri.”

18Ayuda sanakhulupirirebe kuti iye anali wosaona ndi kuti anayamba kuona kufikira atayitana makolo ake. 19Iwo anafunsa kuti, “Kodi uyu ndi mwana wanu? Kodi iyeyu ndi amene mukunena kuti anabadwa wosaona? Nanga zikutheka bwanji kuti akuona?”

20Makolo anayankha kuti, “Ife tikudziwa kuti ndi mwana wathu, ndipo tikudziwa kuti anabadwa wosaona. 21Koma sitidziwa zimene zachitika kuti tsopano azipenya. Amenenso wamupenyetsa sitikumudziwa. Mufunseni ndi wamkulu; iye adziyankhira yekha.” 22Makolo ake ananena izi chifukwa amaopa Ayuda, popeza Ayuda anatsimikiza kale kuti aliyense amene adzamuvomereza Yesu kuti anali Khristu adzatulutsidwa mʼsunagoge. 23Ichi ndi chifukwa chake makolo ake anati, “Mufunseni iye ndi wamkulu.”

24Iwo anamuyitanitsa kachiwiri munthu amene anali wosaonayo. Iwo anati, “Lemekeza Mulungu. Ife tikudziwa kuti munthu uyu ndi wochimwa.”

25Iye anayankha kuti, “Zakuti Iye ndi wochimwa kapena ayi, ine sindikudziwa. Ine ndikudziwa chinthu chimodzi. Ndinali wosaona koma tsopano ndikuona!”

26Kenaka anamufunsa kuti, “Kodi Iye anachita chiyani kwa iwe? Iye anatsekula motani maso ako?”

27Iye anayankha kuti, “Ine ndakuwuzani kale ndipo inu simunamvetsetse. Chifukwa chiyani mukufuna mumvenso? Mukufuna kuti inu mukhale ophunzira akenso?”

28Pamenepo anamunyoza ndipo anati, “Iwe ndiye ophunzira wa munthuyu! Ife ndife ophunzira a Mose! 29Ife tikudziwa kuti Mulungu anayankhula kwa Mose, koma za munthu uyu, ife sitikudziwa ngakhale kumene akuchokera.”

30Munthuyo anayankha kuti, “Tsopano izi ndi zodabwitsa! Inu simukudziwa kumene akuchokera, komabe iye watsekula maso anga. 31Ife tikudziwa kuti Mulungu samvera wochimwa. Iye amamvera munthu woopa Mulungu amene amachita chifuniro chake. 32Palibe amene anamvapo za kutsekula maso a munthu wobadwa wosaona. 33Ngati munthu uyu akanakhala wosachokera kwa Mulungu, palibe chimene Iye akanachita.”

34Pamenepo anayankha kuti, “Iwe unabadwa mu uchimo kotheratu; bwanji ukuyesa kutiphunzitsa ife!” Ndipo anamutulutsa kunja.

Kusaona kwa Uzimu

35Yesu anamva kuti anamutulutsa kunja ndipo pamene anamupeza anati, “Kodi ukukhulupirira Mwana wa Munthu?”

36Munthuyo anafunsa kuti, “Kodi, Ambuye, ameneyo ndi ndani? Ndiwuzeni kuti ndimukhulupirire Iye?”

37Yesu anati, “Iwe wamuona tsopano. Zoonadi ndiye amene akuyankhula nawe.”

38Pamenepo munthuyo anati, “Ambuye, ndikukhulupirira,” ndipo anamulambira Iye.

39Yesu anati, “Ndinabwera pansi pano kudzaweruza kuti osaona aone ndi openya asaone.”

40Afarisi ena amene anali pafupi naye anamva akunena izi ndipo anafunsa kuti, “Chiyani? Kodi ndife osaonanso?”

41Yesu anati, “Mukanakhala osaona, simukanachimwa; koma tsopano popeza mukuti mumaona, ndinu ochimwabe.”

Habrit Hakhadasha/Haderekh

הבשורה על-פי יוחנן 9:1-41

1ישוע עבר בדרך וראה איש שהיה עיוור מלידה.

2”רבי,“ שאלו תלמידיו, ”מדוע נולד האיש עיוור, בגלל חטאיו שלו או של הוריו?“

3”לא בגלל חטאיו ולא בגלל חטאי הוריו“, השיב ישוע. ”אדם זה נולד עיוור על־מנת שאלוהים יוכל לגלות בו את כוחו וגבורתו. 4עלינו למהר לעשות לאור היום את מה שהטיל עלינו שולחי, כי תוך זמן קצר יבוא הלילה, ואז לא יוכל איש לעשות דבר. 5כל עוד אני בעולם, אני אור העולם – אני מעניק לו את אורי.“

6ישוע ירק על הארץ, עשה משחה מהרוק ומרח אותה על עיני העיוור. 7”לך לשטוף את עיניך בבריכת השילוח“, אמר לו ישוע. העיוור הלך לשטוף את עיניו ושב למקום בעיניים פקוחות ובריאות.

8שכנים ואנשים שהכירו אותו כקבצן עיוור שאלו זה את זה: ”האם זהו אותו קבצן עיוור?“ 9אחדים השיבו: ”כן.“ ואחדים אמרו: ”לא. לא ייתכן שזהו אותו אדם“, הרהרו בקול. ”אבל הוא באמת דומה לו כשתי טיפות מים!“

הקבצן בא לעזרתם וקרא ”אני האיש!“

10”כיצד אתה יכול לראות? מה קרה לך?“ שאלו.

11והקבצן סיפר להם: ”אדם בשם ישוע מרח משחה על עיני, ואמר לי לשטוף אותן בבריכת השילוח. עשיתי כדבריו ואני יכול לראות!“

12”היכן האיש הזה עכשיו?“ שאלו האנשים.

”איני יודע“, השיב הקבצן.

13ואז הם לקחו את הקבצן אל הפרושים 14(כל זה התרחש בשבת).

15”כיצד נפקחו עיניך?“ שאלו הפרושים. והקבצן סיפר להם כיצד ישוע מרח משחה על עיניו ושלחו לשטוף אותן בבריכת השילוח. 16אחדים מהפרושים החליטו: ”האיש הזה, ישוע, אינו יכול לבוא מן האלוהים, מאחר שאין הוא שומר את השבת.“

אחרים טענו: ”אבל כיצד יכול אדם חוטא לחולל ניסים כאלה?“ מחלוקת קשה התפתחה ביניהם.

17הפרושים פנו אל הקבצן ושאלו: ”מה דעתך על האיש שריפא אותך?“ ”אני חושב שהוא נביא שנשלח על־ידי אלוהים“, השיב הקבצן.

18מנהיגי היהודים לא האמינו שהקבצן היה באמת עיוור ושעתה נרפא, ומשום כך הלכו לברר את הדבר אצל הוריו.

19”האם זהו בנכם?“ שאלו. ”האם הוא באמת נולד עיוור? אם כן, כיצד הוא יכול לראות עתה?“ 20אולם ההורים השיבו: ”אנחנו יודעים כי זהו בננו וכי נולד עיוור, 21אך איננו יודעים כיצד הוא יכול לראות, או מי ריפא אותו. הוא אדם מבוגר ויכול לדבר בעד עצמו“, שאלו אותו. 22‏-23ההורים ענו כך כי חששו ממנהיגי היהודים, אשר איימו לגרש מקהל ישראל את כל המודה שישוע הוא המשיח.

24שוב קראו היהודים לקבצן שהיה עיוור ואמרו: ”עליך להודות לאלוהים ולא לישוע, כי כולנו יודעים שהוא איש חוטא.“

25”איני יודע אם הוא חוטא או לא,“ השיב הקבצן, ”אבל דבר אחד אני יודע: הייתי עיוור ועכשיו אני רואה!“

26”מה הוא עשה? כיצד ריפא אותך?“ דרשו.

27”כבר סיפרתי לכם. האם לא שמעתם? מדוע אתם מבקשים שאספר לכם בשנית, האם גם אתם רוצים להיות תלמידיו?“ שאל הקבצן.

28הם קללו אותו ואמרו: ”אתה תלמידו! אנחנו תלמידיו של משה רבנו! 29אנחנו יודעים שאלוהים דיבר אל משה, אבל איננו יודעים דבר על האיש הזה.“

30”מוזר מאוד שאינכם יודעים דבר על אודות האיש שריפא את עיני“, השיב הקבצן. 31”אנחנו יודעים כי אלוהים אינו שומע לקול הרשעים, אך הוא מקשיב ברצון לאלה שאוהבים אותו ושומעים בקולו. 32מאז בריאת העולם לא שמענו על אדם שריפא עיוורון מלידה. 33אילו אדם זה לא בא מאלוהים, הוא לא היה מסוגל לעשות מאומה!“

34”ממזר שכמוך!“ קראו לעברו בזעם. ”אתה מתיימר ללמד אותנו?“ והם גרשוהו החוצה.

35כאשר שמע ישוע את הדבר, הוא פגש בקבצן ושאל אותו: ”האם אתה מאמין בבן האדם?“

36”מיהו?“ שאל האיש. ”אני רוצה להאמין בו.“

37”ראית אותו, והוא מדבר אליך כרגע“ השיב ישוע.

38”כן, אדוני,“ קרא האיש, ”אני מאמין!“ והוא השתחווה לישוע.

39”אני באתי לעולם לשם משפט – להעניק ראייה לעיוורים, ולהוכיח לאלה שחושבים את עצמם לפיקחים שהם למעשה עיוורים“, אמר ישוע.

40הפרושים שעמדו שם שאלו: ”האם אתה כולל אותנו בין העיוורים?“

41”אילו הייתם עיוורים לא הייתם אשמים“, הסביר ישוע. ”אולם אתם טוענים שאתם רואים, ולכן אתם אשמים.“