Yohane 16 – CCL & HHH

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yohane 16:1-33

1“Ine ndakuwuzani zonsezi kuti musadzakhumudwe. 2Iwo adzakuchotsani mʼsunagoge mwawo. Kunena zoona, nthawi ikubwera imene aliyense amene adzakuphani adzaganiza kuti akutumikira Mulungu. 3Iwo adzachita zoterozo chifukwa sanadziwe Atate kapena Inenso. 4Ine ndakuwuzani izi kuti nthawi ikadzafika mudzakumbukire kuti Ine ndinakuchenjezani kale. Ine sindinakuwuzeni izi poyamba paja chifukwa ndinali nanu.”

Ntchito ya Mzimu Woyera

5“Tsopano Ine ndikupita kwa Iye amene anandituma koma palibe wina mwa inu akundifunsa kuti, ‘Kodi mukupita kuti?’ 6Muli ndi chisoni kwambiri chifukwa ndakuwuzani zimene. 7Komatu ndakuwuzani zoona. Ine ndikuti kuli bwino kwa inu kuti ndichoke. Ngati sindichoka, Nkhosweyo sidzabwera kwa inu, koma ngati Ine ndipita, ndidzamutumiza kwa inu. 8Iye akabwera, adzatsutsa dziko lapansi za uchimo, zachilungamo ndi zachiweruzo. 9Za uchimo, chifukwa anthu sakhulupirira Ine. 10Za chilungamo, chifukwa Ine ndi kupita kwa Atate, kumene simudzandionanso. 11Za chiweruzo, chifukwa wolamulira dziko lino lapansi waweruzidwa tsopano.

12“Ine ndili ndi zambiri zoti ndiyankhule nanu, koma simungathe kuzilandira tsopano. 13Koma pamene Iye, Mzimu wachoonadi, abwera, adzakutsogolerani mʼchoonadi chonse. Iye sadzayankhula mwa Iye yekha, adzayankhula zokhazo zimene wamva ndipo Iye adzakuwuzani zimene zikubwera. 14Iye adzalemekeza Ine chifukwa adzatenga za Ine nadzakudziwitsani. 15Zonse za Atate ndi zanga. Ichi nʼchifukwa chake Ine ndanena kuti Mzimu Woyera adzatenga kwa Ine zanga kuti muzidziwe.”

Chisoni cha Ophunzira Chisandulika Chimwemwe

16Yesu anapitiriza kuyankhula kuti, “Mwa kanthawi kochepa, simudzandionanso, ndipo patatha nthawi pangʼono mudzandionanso.”

17Ena a ophunzira ake anati kwa wina ndi mnzake, “Kodi Iye akutanthauza chiyani ponena kuti, ‘Mwa kanthawi kochepa, simudzandionanso,’ ndi ‘ndipo patatha nthawi pangʼono mudzandionanso,’ ndiponso ‘chifukwa ndikupita kwa Atate?’ ” 18Iwo anapitiriza kufunsana kuti, “Kodi akutanthauza chiyani, ‘kanthawi kochepa?’ Ife sitikumvetsetsa chimene Iye akuyankhula.”

19Yesu anadziwa kuti ankafuna kuti amufunse za zimenezi, choncho anawafunsa kuti, “Kodi mukufunsana wina ndi mnzake chimene Ine ndimatanthauza pamene ndinati, ‘Mwa kanthawi kochepa simudzandionanso,’ ndi ‘patatha nthawi pangʼono mudzandionanso?’ 20Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti inu mudzalira ndi kubuma pomwe dziko lapansi lidzakhale likukondwera. Inu mudzamva chisoni, koma chisoni chanu chidzasandulika chimwemwe. 21Mayi akamabereka mwana amamva ululu chifukwa nthawi yake yafika; koma mwana wake akabadwa amayiwala ululu wake chifukwa cha chimwemwe chake chakuti mwana wabadwa mʼdziko lapansi. 22Chimodzimodzinso ndi inu. Tsopano ino ndi nthawi yanu yomva chisoni, koma Ine ndidzakuonaninso ndipo inu mudzasangalala, ndipo palibe amene adzachotsa chimwemwe chanu. 23Tsiku limenelo inu simudzandipemphanso kalikonse. Ine ndikukuwuzani zoona kuti Atate anga adzakupatsani chilichonse chimene mudzapempha mʼdzina langa. 24Mpaka tsopano simunapemphe kalikonse mʼdzina langa. Pemphani ndipo mudzalandira, ndipo chimwemwe chanu chidzakhala chathunthu.

25“Ngakhale ndakhala ndikuyankhula mʼmafanizo, nthawi ikubwera imene Ine sindidzagwiritsanso ntchito mafanizo otere koma ndidzakuwuzani momveka za Atate anga. 26Tsiku limenelo inu mudzapempha mʼdzina langa. Ine sindikunena kuti ndidzapempha Atate mʼmalo mwanu ayi. 27Atate mwini anakukondani chifukwa inu mwandikonda Ine ndipo mwakhulupirira kuti Ine ndinabwera kuchokera kwa Atate. 28Ine ndinabwera kuchokera kwa Atate ndi kulowa mʼdziko lapansi. Tsopano ndikulisiya dziko lapansi kubwerera kwa Atate.”

29Kenaka ophunzira ake anati, “Tsopano mukuyankhula momveka bwino ndi mopanda mafanizo. 30Tsopano ife tikuona kuti Inu mumadziwa zinthu zonse ndi kuti sipafunika wina aliyense kukufunsani. Mwa ichi ife takhulupirira kuti Inu munachokera kwa Mulungu.”

31Yesu anawafunsa kuti, “Kodi tsopano mwakhulupirira?” 32Koma nthawi ikubwera ndipo yafika, pamene inu mudzabalalitsidwa, aliyense ku nyumba yake. Inu mudzandisiya ndekhandekha. Koma Ine sindili ndekha, pakuti Atate anga ali nane.

33“Ine ndakuwuzani izi kuti mwa Ine mukhale nawo mtendere. Mʼdziko lapansi mudzakhala nawo mavuto. Koma limbikani mtima! Ine ndaligonjetsa dziko lapansi.”

Habrit Hakhadasha/Haderekh

הבשורה על-פי יוחנן 16:1-33

1”סיפרתי לכם את כל הדברים האלה כדי שתדעו מה מצפה לכם ולא תופתעו או תיבהלו. 2יגרשו אתכם מבתי־הכנסת, ואף יגיע הזמן שהרוצחים אתכם יחשבו שהם עושים את רצון אלוהים! 3הם יעשו כל זאת מפני שאינם מכירים את אבי ואותי. 4אני מספר לכם את כל הדברים האלה כדי שבבוא העת תיזכרו שהזהרתי אתכם. לא סיפרתי לכם זאת מקודם, מפני שעדיין הייתי עמכם.

5”אולם עתה אני חוזר אל שולחי, ואיש מכם אינו מתעניין לדעת לאן אני הולך. 6דברי רק העציבו אתכם. 7האמת היא כי מוטב שאלך, אחרת לא יבוא המנחם. אם אלך הוא יבוא, מפני שאשלח אותו אליכם.

8”כאשר יבוא המנחם הוא ילמד את העולם מהי משמעות החטא, הצדק והמשפט. 9הוא יוציא לאור את חטא העולם, משום שלא האמינו בי. 10הוא יראה להם מהו הצדק האמתי, כי אני חוזר אל אבי ושוב לא תראו אותי. 11הוא ילמד אותם את משמעות המשפט, כי שליט העולם הזה (השטן) כבר נשפט ונדון.

12”הייתי רוצה לומר לכם עוד דברים רבים, אבל אינכם מסוגלים להבינם עדיין. 13כאשר יבוא אליכם רוח האמת הוא יוביל אתכם אל כל האמת, כי אין הוא מדבר על דעת עצמו; הוא יספר לכם את אשר שמע. הוא יספר לכם גם על העתיד. 14הוא יפאר אותי ויביא לי כבוד רב בהראותו לכם את תפארתי. 15כל תפארתו היא תפארתי, ומשום כך אמרתי לכם שהרוח יביא לי כבוד רב בהראותו לכם את תפארתי. 16בעוד זמן מה אלך ושוב לא תראו אותי, אך כעבור זמן מה תראו אותי בשנית, כי אני הולך אל אבי.“

17אחדים מתלמידיו לא הבינו את דבריו. ”למה הוא מתכוון באמרו שבעוד זמן מה נראה אותו בשנית, כי הוא הולך אל אביו?“ שאלו איש את רעהו. 18”למה הוא מתכוון באמרו ’זמן מה‘?“ תמהו.

19ישוע ידע מה הטריד אותם ולכן שאל: ”האם אתם תוהים למה התכוונתי? 20אני אומר לכם באמת וברצינות: העולם ישמח ויגיל על מה שיקרה לי, ואילו אתם תבכו. אבל צערכם יהפוך לשמחה נפלאה, כאשר תראו אותי שנית. 21שמחה זו תדמה לשמחתה של יולדת השוכחת את חבלי הלידה לאחר הולדת תינוקה, כי היא נמלאת שמחה וגיל על כך שאדם נולד לעולם. 22עכשיו אתם עצובים, אולם אשוב לראותכם, ואז תשמחו מאוד ואיש לא יוכל להשבית את שמחתכם. 23ביום ההוא לא יהיה עליכם לבקש ממני דבר, כי תוכלו לבקש את הדבר מאבי, והוא ייתן לכם כל מה שתבקשו ממנו בשמי. 24עד עתה לא ביקשתם דבר בשמי; בקשו ותקבלו, כדי שתימלאו שמחה רבה.

25”דיברתי אליכם במשלים וחידות, אולם יבוא יום שאדבר אליכם על אבי בבירור ולא עוד בחידות ובמשלים. 26ביום ההוא תוכלו לבקש בשמי כל דבר, ולא אצטרך יותר לבקש מאבי שיתן לכם אותו. 27כי אבי אוהב אתכם משום שאתם אוהבים אותי ומאמינים שיצאתי ממנו. 28כן, יצאתי מאבי ובאתי לעולם. כעת אני עוזב את העולם וחוזר לאבי.“

29”סוף סוף אתה מדבר דברים ברורים ולא בחידות ובמשלים“, קראו תלמידיו בהקלה. 30”עתה אנו יודעים שאתה יודע הכל, ואיננו צריכים לשאול אותך יותר שאלות. אנו מאמינים שבאת מאלוהים.“

31”אתם מאמינים לי לבסוף?“ שאל ישוע. 32”אולם יגיע הזמן – למעשה הוא כבר הגיע – שכולכם תתפזרו איש לביתו ותעזבוני לבדי. אך לא אהיה לבדי כי אבי עמדי. 33אמרתי לכם את כל הדברים האלה כדי שלבכם ישקוט ולא תדאגו. כאן בעולם יהיו לכם קשיים וצרות, אולם חיזקו ואימצו, כי אני ניצחתי את העולם!“