Yobu 8 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yobu 8:1-22

Mawu a Bilidadi

1Pamenepo Bilidadi wa ku Suki anayankha kuti,

2“Kodi udzakhala ukuyankhula zoterezi mpaka liti?

Mawu ako ali ngati mphepo yamkuntho.

3Kodi Mulungu amapotoza chiweruzo cholungama?

Kodi Wamphamvuzonse amalephera kuchita zachilungamo?

4Pamene ana ako anamuchimwira Mulungu,

Iye anawapereka kuti alangidwe chifukwa cha tchimo lawo.

5Koma utayangʼana kwa Mulungu,

ndi kudandaulira Wamphamvuzonse,

6ngati uli wangwiro ndi wolungama mtima

ngakhale tsopano Iye adzachitapo kanthu mʼmalo mwako

ndipo adzakubwezeretsa pa malo ako oyenera.

7Chiyambi chako chidzaoneka ngati chochepa

koma chimaliziro chako chidzakhala chopambana.

8“Funsa kwa anthu amvulazakale

ndipo upeze zimene makolo awo anaziphunzira

9pakuti ife ndife ana adzulodzuloli ndipo sitidziwa chilichonse,

ndipo moyo wathu pa dziko lapansi uli ngati chithunzithunzi.

10Kodi iwo sadzakulangiza ndi kukufotokozera?

Kodi sadzakuwuza mawu ochokera pa zimene amazidziwa?

11Kodi bango nʼkumera pa nthaka yopanda chinyontho?

Nanga mawango nʼkukula bwino popanda madzi?

12Popanda madzi, zimenezi zimafota zikanali zaziwisi ndi zosadula;

zimawuma msangamsanga kuposa bango.

13Ndimo mmene amachitira anthu onse amene amayiwala Mulungu;

ndi mmene chiyembekezo cha munthu wosapembedza Mulungu chimathera.

14Kulimba mtima kwake kumafowoka;

zimene iye amadalira zili ngati ukonde wa kangawude.

15Iye amatsamira ukonde wake, koma umaduka;

amawugwiritsitsa koma sulimba.

16Munthu woyipayo ali ngati chomera chothiriridwa bwino chimene chili pa dzuwa,

nthambi zake zimatambalala pa munda wake;

17mizu yake imayanga pa mulu wa miyala

ndi kufunafuna malo woti izikike pa miyalapo.

18Koma pamene yachotsedwa pamalo pakepo,

pamalopo pamakana chomeracho ndi kuti, ‘Ine sindinakuonepo.’

19Ndithudi chomeracho chimafota,

ndipo pa nthakapo pamatuluka zomera zina.

20“Ndithudi, Mulungu sakana munthu amene alibe cholakwa

kapena kulimbikitsa anthu ochita zoyipa.

21Iye adzadzaza mʼkamwa mwako ndi phwete

ndipo milomo yako idzafuwula ndi chimwemwe.

22Adani ako adzachita manyazi,

ndipo malo okhalamo anthu oyipa sadzaonekanso.”