Yobu 21 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yobu 21:1-34

Mawu a Yobu

1Pamenepo Yobu anayankha kuti,

2“Mvetserani bwino mawu anga;

ichi chikhale chitonthozo changa chochokera kwa inu.

3Ndiloleni ndiyankhule

ndipo ndikatha kuyankhula munditonzetonze.

4“Kodi ine ndikudandaulira munthu?

Tsono ndilekerenji kupsa mtima?

5Ndipenyeni ndipo mudabwe;

mugwire dzanja pakamwa.

6Ndikamaganiza zimenezi ndimachita mantha kwambiri;

thupi langa limanjenjemera.

7Chifukwa chiyani anthu oyipa amakhalabe ndi moyo,

amakalamba ndi kusanduka amphamvu?

8Amaona ana awo akukhazikika pamodzi nawo,

zidzukulu zawo zikukula bwino iwo akuona.

9Mabanja awo amakhala pa mtendere ndipo sakhala ndi mantha;

mkwapulo wa Mulungu suwakhudza nʼkomwe.

10Ngʼombe zawo zazimuna sizilephera kubereketsa;

ngʼombe zawo zazikazi sizipoloza.

11Amatulutsa ana awo ngati gulu la nkhosa;

makanda awo amavinavina pabwalo.

12Amayimba nyimbo pogwiritsa ntchito matambolini ndi azeze;

amakondwa pakumva kulira kwa chitoliro.

13Zaka zawo zimatha ali mu ulemerero

ndipo amatsikira ku manda mwamtendere.

14Koma anthuwo amawuza Mulungu kuti, ‘Tichokereni!’

Ife tilibe chikhumbokhumbo chofuna kudziwa njira zanu.

15Kodi Wamphamvuzonseyo ndani kuti timutumikire?

Ife tipindula chiyani tikamapemphera kwa Iyeyo?

16Komatu ulemerero wawo suli mʼmanja mwawo,

koma ine ndimakhala patali ndi uphungu wa anthu oyipa.

17“Koma nʼkangati kamene nyale ya anthu oyipa imazimitsidwa?

Nʼkangati kamene tsoka limawagwera?

Nʼkangati kamene Mulungu amawakwiyira ndi kuwalanga?

18Nʼkangati kamene iwo amakhala ngati phesi lowuluka ndi mphepo,

ngati mungu wowuluzika ndi kamvuluvulu?

19Paja amati, ‘Mulungu amalanga ana chifukwa cha machimo abambo awo.’

Koma Mulungu amabwezera chilango munthuyo, kuti adziwe kuti Mulungu amalangadi.

20Mulole kuti adzionere yekha chilango chake,

kuti alawe ukali wa Wamphamvuzonse.

21Nanga kodi amalabadira chiyani zabanja lake limene walisiya mʼmbuyo,

pamene chiwerengero cha masiku ake chatha?

22“Kodi alipo wina amene angaphunzitse Mulungu nzeru,

poti Iye amaweruza ngakhale anthu apamwamba?

23Munthu wina amamwalira ali ndi mphamvu zonse,

ali pa mtendere ndi pa mpumulo,

24thupi lake lili lonenepa,

mafupa ake ali odzaza ndi mafuta.

25Munthu wina amamwalira ali wowawidwa mtima,

wosalawapo chinthu chabwino chilichonse.

26Olemera ndi osauka omwe amamwalira ndi kuyikidwa mʼmanda

ndipo onse amatuluka mphutsi.

27“Ndikudziwa bwino zimene mukuganiza,

ziwembu zanu zomwe mukuti mundichitire.

28Inu mukuti, ‘Kodi nyumba ya mkulu uja ili kuti,

matenti amene munkakhala anthu oyipa aja ali kuti?’

29Kodi munawafunsapo anthu amene ali pa ulendo?

Kodi munaganizirapo zimene iwo amanena?

30Zakuti munthu woyipa amasungidwa chifukwa cha tsiku la tsoka,

kuti amapulumutsidwa chifukwa cha tsiku la ukali wa Mulungu?

31Kodi ndani amadzudzula munthu wochimwayo?

Ndani amamubwezera zoyipa zimene anachita?

32Iye amanyamulidwa kupita ku manda

ndipo anthu amachezera pa manda ake.

33Dothi la ku chigwa limamukomera;

anthu onse amatsatira mtembo wake,

ndipo anthu osawerengeka amakhala patsogolo pa chitanda chakecho.

34“Nanga inu mudzanditonthoza bwanji ine ndi mawu anu opandapakewo

palibe chimene chatsala kuti muyankhe koma mabodza basi!”