Yesaya 58 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 58:1-14

Kusala Kwenikweni

1“Fuwula kwambiri, usaleke.

Mawu ako amveke ngati lipenga.

Uwawuze anthu anga za kulakwa kwawo;

uwuze nyumba ya Yakobo za machimo awo.

2Pakuti tsiku ndi tsiku amafunafuna Ine;

amaoneka ngati a chidwi chofuna kudziwa zimene ndimafuna,

kukhala ngati kuti ndi dziko limene limachita zolondola

ndipo silinasiye zolamulira za Mulungu wake.

Amandipempha kuti ndigamule mlandu wawo mwachilungamo

ndipo amaonetsa chidwi chofuna kukhala pafupi ndi Mulungu.

3Anthu akufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani ife tasala

kudya pamene Inu simukulabadirapo?

Kodi ife tavutikiranji nʼkudzichepetsa

pamene Inu simunasamalepo?’ ”

Yehova akuti, “Komatu tsiku lanu losala kudya, mumachita zinthu zokukondweretsani,

ndipo mumazunza antchito anu onse.

4Mumati uku mukusala kudya, uku mukukangana ndi kumenyana,

mpaka kumenyana ndi nkhonya zopweteka.

Kusala kudya mukuchitiramu musayembekezere kuti mawu anu amveka kumwamba.

5Kodi kusala kudya kumene ndimakufuna Ine nʼkumeneku,

kungokhala tsiku loti munthu adzichepetse basi?

Kodi ndi tsiku loti munthu angowerama pansi ngati bango

ndi kumayala ziguduli nʼkuthirapo phulusa nʼkugonapo?

Kodi ndiye mumati kusala kudya kumeneko,

tsiku lokondweretsa Yehova?

6“Kodi si uku kusala kudya kumene Ine ndimakufuna:

Kumasula maunyolo ozunzizira anthu

ndi kumasula zingwe za goli,

kupereka ufulu kwa oponderezedwa

ndi kuphwanya goli lililonse?

7Anthu anjala kodi mwawagawira chakudya chanu?

Osowa ndi ongoyendayenda,

kodi mwawapatsa malo ogona?

Munthu wausiwa kodi mwamupatsa chovala?

8Mukatero chipulumutso chanu chidzabwera ngati mʼbandakucha,

ndipo mabala anu adzachira msangamsanga;

chilungamo chanu chidzakutsogolerani

ndipo ulemerero wa Yehova udzakhala chokutchinjirizani kumbuyo kwanu.

9Mukamadzapemphera Yehova adzakuyankhani;

mukadzapempha thandizo, Iye adzati: Ine ndili pano.

“Ngati muleka kuzunza anzanu,

ngati musiya kuloza chala ndiponso kunena zoyipa za anzanu.

10Ndipo ngati mudyetsa anthu anjala,

ndi kuthandiza anthu oponderezedwa,

pamenepo kuwala kwanu kudzaonekera mu mdima,

ndipo usiku wanu udzakhala ngati usana.

11Yehova adzakutsogolerani nthawi zonse;

adzakwaniritsa zosowa zanu mʼdziko longʼalukangʼaluka dzuwa

ndipo adzalimbitsa matupi anu.

Mudzakhala ngati dimba la madzi ambiri,

ngati kasupe amene madzi ake saphwa.

12Anthu ako adzamanganso nyumba zimene zakhala mabwinja nthawi yayitali,

ndipo adzamanganso pa maziko akalekale;

inu mudzatchedwa okonza makoma opasuka.

Anthu okonza misewu ndi nyumba zake.

13“Muzisunga osaphwanya Sabata;

musamachite zimene mukufuna pa masiku anga opatulika,

tsiku la Sabata lizikhala tsiku lachisangalalo.

Tsiku lopatulika la Yehova muzililemekeza

posayenda mʼnjira zanu,

kapena kuchita zimene mukufuna ndi kuyankhula zopandapake,

14mukatero mudzapeza chimwemwe mwa Yehova,

ndipo ndidzakukwezani ndi kukupambanitsani pa dziko lonse lapansi.

Mudzadyerera dziko limene ndinapatsa Yakobo kholo lanu.”

Yehova wayankhula ndi pakamwa pake.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

以赛亚书 58:1-14

真正的虔诚

1“你要高声呼喊,不要停止;

要放声高呼,像响亮的号角。

要向我的子民宣告他们的过犯,

雅各家宣告他们的罪恶。

2他们天天寻求我,

好像渴慕认识我的律法,

俨然像没有丢弃他们上帝法令的正义之邦。

他们向我求公义的判决,

似乎渴慕到我面前。

3他们说,‘我们禁食,你为什么不看呢?

我们刻苦己身,你为什么不理睬呢?’

我说,‘看啊,禁食之日你们仍然随心所欲,

压榨你们的工人。

4你们一面禁食,一面争闹打斗,

彼此恶拳相向。

不要指望这样的禁食会使你们的祷告在天上蒙垂听。

5难道这是我要的禁食吗?

难道刻苦己身、

像芦苇一样垂着头、

躺在麻布和炉灰上就是禁食吗?

这就是你们所谓的禁食,

所谓的蒙耶和华悦纳的日子吗?

6“‘我要的禁食是,

除去罪恶的锁链,

解开轭上的绳索,

折断一切的轭,

使受欺压的人得到自由,

7把你们的食物分给饥饿的人,

接待无家可归的穷人,

送衣服给赤身露体的人,

不躲避求助的亲人。

8如果你们这样做,你们的光必如晨光照耀,

你们的创伤必迅速痊愈,

你们的公义必在前方为你们开路,

耶和华的荣耀必在后面保护你们。

9你们求告,我必应允;

你们呼求,我必回应。

如果你们不再欺压、指责、毁谤,

10如果你们给饥饿的人食物,

扶助困苦的人,

你们的光必照亮黑暗,

你们的黑夜必变成正午。

11耶和华必不断地引导你们,

使你们在干旱之地也能得到供应,筋骨强健。

你们必像灌溉充足的园子,

又像涌流不息的泉源。

12你们当中必有人重修古老的荒场,

重建远古的根基。

你们必被称为修补断垣、

重建街道的人。

13“‘如果你们遵守安息日,

在我的圣日不做私事,

以安息日为乐,

尊崇我的圣日,

不随意而行,

不妄自说话,

14就必以耶和华为乐,

耶和华必使你们在地上受尊崇,

并享用你们先祖雅各的产业。’”

这是耶和华亲口说的。