Yesaya 27 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 27:1-13

Za Munda Wamphesa wa Yehova

1Tsiku limenelo,

Yehova ndi lupanga lake

lakuthwa, lalikulu ndi lamphamvu,

adzalanga Leviyatani chinjoka chothawa chija,

Leviyatani chinjoka chodzikulunga;

adzapha chirombo choopsa cha mʼnyanja.

2Tsiku limenelo Yehova adzati,

“Tidzayimba nyimbo ya munda wamphesa wobereka bwino:

3Ine, Yehova, ndimawuyangʼanira;

ndimawuthirira nthawi zonse.

Ndimawulondera usana ndi usiku

kuti wina angawononge.

4Ine sindinakwiye.

Ngati mkandankhuku ndi minga zikanaoneka ndikanalimbana nazo!

Ndikachita nazo nkhondo;

ndikanazitentha zonse ndi moto.

5Koma ngati apo ayi, abweretu kwa Ine adani angawo kuti ndidzawateteze;

apangane nane za mtendere,

ndithu, apangane nane za mtendere.”

6Masiku akubwerawo Yakobo adzazika mizu,

Israeli adzaphukira ndi kuchita maluwa,

ndipo adzadzaza dziko lonse lapansi ndi zipatso.

7Kodi Yehova anakantha Israeli

ngati momwe anakanthira anthu amene anazunza Israeli?

Kapena kodi Yehova anapha Israeli

ngati mmene anthu ena anaphera Israeli?

8Yehova mwawalanga powapirikitsa ndi kuwatumiza ku ukapolo,

mwawachotsa ndi mpweya wanu woopsa,

monga zimachitikira pa tsiku la mkuntho wochokera kummawa.

9Yehova adzakhululuka kulakwa kwa Yakobo.

Iwo adzaonetsa kuti alapadi pamene adzaphwanya miyala yonse ya guwa lachikunja,

ngati mmene anthu amaphwanyira miyala yanjereza

mpaka kukhala ngati fumbi lokhalokha.

Sipadzapezekanso mafano a Asera

kapena maguwa ofukiza lubani.

10Mzinda wamalinga uja wasanduka bwinja,

wasanduka malo osiyidwa, ndi kutayidwa ngati chipululu;

kumeneko amadyetselako ana angʼombe

kumeneko zimapumulako ziweto

ndi kumwetula nthambi za mitengo kotheratu.

11Pamene nthambi za mitengoyo zauma, zimathyoka

ndipo amayi amabwera nazitola ndi kuzisandutsa nkhuni.

Pakuti awa ndi anthu opanda nzeru;

kotero Mulungu amene anawapanga sadzachitira chisoni,

ndipo Mlengi wawo sawakomera mtima.

12Tsiku limenelo Yehova adzasonkhanitsa pamodzi anthu ake mmodzimmodzi kumalo opunthira tirigu, kuchokera ku mtsinje wa Yufurate mpaka ku mtsinje wa ku Igupto. 13Ndipo tsiku limenelo lipenga lalikulu lidzalira. Amene akuzunzika ku Asiriya iwo amene ali ku ukapolo ku Igupto adzabwera ndi kudzalambira Yehova pa phiri lopatulika mu Yerusalemu.