Yeremiya 8 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yeremiya 8:1-22

1Yehova akuti, “ ‘Pa nthawi imeneyo, mafupa a mafumu ndi a akuluakulu a ku Yuda, mafupa a ansembe ndi a aneneri, ndiponso mafupa a anthu a ku Yerusalemu adzafukulidwa. 2Adzawamwaza pa nthaka kuyangʼana dzuwa, mwezi ndi nyenyezi zonse zamlengalenga, zimene ankazikonda, kuzitumikira ndi kuzitsatira, kupemphako nzeru ndiponso kuzilambira. Mafupawo sadzawasonkhanitsa kapena kuwakwirira, koma adzakhala ngati ndowe pamwamba pa nthaka. 3Otsala onse a mtundu woyipawu adzafuna imfa kopambana moyo kulikonse kumene ndidzawapirikitsirako, akutero Yehova Wamphamvuzonse.’ ”

Tchimo ndi Chilango Chake

4“Tsono awuze anthuwa, ‘Yehova akuti:

“ ‘Kodi anthu akagwa sangadzukenso?

Munthu akasochera kodi sangathe kubwereranso?

5Chifukwa chiyani nanga anthu awa akupitirirabe kuchimwa, osabwerera?

Chifukwa chiyani Yerusalemu akubwerera mʼmbuyo?

Iwo akangamira chinyengo;

akukana kubwerera.

6Ine ndinatchera khutu kumvetsera

koma iwo sanayankhulepo zoona.

Palibe woyipa amene analapapo zoyipa zake,

nʼkumati, ‘Ine ndachita chiyani?’

Aliyense akutsatira njira yake

ngati kavalo wothamangira nkhondo.

7Mbalame yotchedwa kakowa ija imadziwa

nthawi yake mlengalenga.

Koma nkhunda, namzeze ndi chingalu

zimadziwa nthawi yonyamukira ulendo,

koma anthu anga sadziwa

malamulo a Yehova.

8“ ‘Inu mukunena bwanji kuti,

‘Ndife anzeru ndipo timasunga malamulo a Yehova?’

Koma ndi alembi anu

amene akulemba zabodza.

9Anthu anzeru achita manyazi;

athedwa nzeru ndipo agwidwa.

Iwo anakana mawu a Yehova.

Nanga tsono nzeru zawo ziwapinduliranji?

10Nʼchifukwa chake akazi awo ndidzawapereka kwa amuna ena

ndipo minda yawo ndidzayipereka kwa amene adzawagonjetse.

Kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu,

onse ali ndi khalidwe lofuna kupeza chuma mwakuba.

Aneneri pamodzi ndi ansembe omwe,

onse amachita zachinyengo.

11Iwo amapoletsa zilonda za anthu anga

pamwamba chabe

nʼkumati, ‘Mtendere, mtendere,’

pamene palibe mtendere.

12Kodi amachita manyazi akamachita zonyansazi?

Ayi, alibe manyazi ndi pangʼono pomwe;

iwo sadziwa nʼkugwetsa nkhope komwe.

Choncho iwo adzagwera pakati pa anzawo amene agwa kale;

adzagwa pansi tsiku limene ndidzawalanga,

akutero Yehova.

13“ ‘Ndidzatenga zokolola zawo,

Sipadzakhalanso mphesa pa mpesa

kapena nkhuyu pa mkuyu,

ndipo masamba ake adzawuma.

Zinthu zimene ndinawapatsa

ndidzawachotsera.’ ”

14Koma amati, “Tikukhala pano chifukwa chiyani?

Tiyeni tonse pamodzi

tithawire ku mizinda yotetezedwa

ndi kukafera kumeneko.

Pakuti Yehova Mulungu wathu watsimikiza kuti tiyenera kufa.

Watipatsa madzi aululu kuti timwe,

chifukwa tamuchimwira.

15Tinkayembekezera mtendere

koma palibe chabwino chomwe chinachitika,

tinkayembekezera kuchira

koma tinakumana ndi zoopsa zokhazokha.

16Kulira kwa ngʼombe zazimuna za mdani

kukumveka kuchokera ku Dani;

dziko lonse likunjenjemera

chifukwa cha kulira kwa akavalowo.

Akubwera kudzawononga dziko

ndi zonse zimene zili mʼmenemo.

Adzawononga mzinda ndi onse okhalamo.”

17Yehova akuti, “Onani, ndikukutumizirani njoka zaululu,

mphiri zimene munthu sangathe kuzilodza,

ndipo zidzakulumani,”

18Ndadzazidwa ndi chisoni kwambiri,

mtima wanga walefukiratu.

19Imvani kulira kwa anthu anga

kuchokera ku dziko lakutali:

akuti, “Kodi Yehova sali ku Ziyoni?

Kodi mfumu yake sili kumeneko?”

“Chifukwa chiyani akundiputa ndi mafano awo osema,

ndi milungu yawo yachilendo?”

20“Nthawi yokolola yapita,

chilimwe chapita,

koma sitinapulumuke.”

21Chifukwa cha mavuto a anthu anga, ine ndikumva kuwawa;

ndikungolira ndipo mantha aakulu andigwira.

22Kodi ku Giliyadi kulibe mankhwala ochiritsa?

Kodi kumeneko kulibe singʼanga?

Nanga chifukwa chiyani mabala

a anthu anga sanapole?

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

耶利米书 8:1-22

1耶和华说:“那时,犹大王、首领、祭司、先知及耶路撒冷居民的骸骨都要从坟墓中被挖出来, 2抛散在他们昔日恋慕、供奉、追随、求问、祭拜的日月星辰之下,无人收殓和埋葬,他们好像地上的粪便。 3我要把这邪恶民族的余民流放异地,他们在那里必痛不欲生。这是万军之耶和华说的。”

4耶和华吩咐我对犹大人说:

“人跌倒后难道不站起来吗?

人走错了路难道不回头吗?

5为什么耶路撒冷的居民一味地背叛我?

他们诡诈成性,不肯回头。

6我仔细听,没有人说实话,

没有人为自己的恶行后悔,说,

‘我做了可怕的事!’

人人一意孤行,

像战马直奔战场。

7天空的鹳鸟尚且知道来去的季节,

斑鸠、燕子和白鹤也遵守迁徙的时间,

但我的子民却不认识耶和华的法则。

8“你们怎能说,‘我们有智慧,

因为我们有耶和华的律法’?

事实上,律法教师撒谎的笔把律法篡改了。

9智者必蒙羞辱,受惊吓,

被捉拿。

看啊,他们既弃掉耶和华的话,

哪里还有智慧可言呢?

10因此,我要把他们的妻子和田地交给别人,

因为他们无论贵贱,

个个贪图不义之财;

无论是先知还是祭司,

都行为诡诈。

11他们敷衍了事地医治我子民的伤痛,说,

‘没事了,没事了!’

其实情况很糟。

12他们做可憎的事会羞愧吗?

不!他们不知廉耻,

毫不脸红。

因此,他们要与其他人一样灭亡,

死在我的惩罚下。

这是耶和华说的。

13我要彻底灭绝他们。

葡萄树必没有葡萄,

无花果树必没有果子,

树叶也要枯干,

我所赐给他们的都要被夺走。

这是耶和华说的。”

14他们说:“我们为什么还坐在这里?

大家一起进入坚城,死在那里吧!

我们的上帝耶和华要毁灭我们,

给我们毒药喝,

因为我们得罪了祂。

15我们期待平安,

却没有平安;

渴望得到医治,

却饱受惊吓。

16“从传来敌人战马的嘶鸣,

声音震动大地。

他们要来吞灭我们的土地和作物、城邑和居民。

17“看啊,我要派毒蛇去咬你们,

法术无法制服它们。”

这是耶和华说的。

18我有无限忧愁,伤心欲绝。

19听啊!远处传来我同胞的哀鸣:

“难道耶和华不在锡安了吗?

难道她的王不在她那里了吗?”

耶和华说:“他们为什么供奉雕刻的神像和外族无用的偶像,惹我发怒?”

20他们说:“麦收已完,

夏季已过,

但我们还未得救。”

21同胞的创伤令我伤心欲绝,

痛苦万分,

惊慌失措。

22难道基列没有药物、

没有医生吗?

为什么我同胞的创伤至今未愈?