Yeremiya 36 – CCL & HOF

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yeremiya 36:1-32

Yehoyakimu Atentha Buku la Yeremiya

1Chaka chachinayi cha Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya Yuda, Yehova anayankhula ndi Yeremiya kuti, 2“Tenga buku ndipo ulembemo mawu onse amene ndayankhula nawe otsutsa Israeli, Yuda ndi mitundu yonse ya anthu, kuyambira nthawi imene ndinayamba kuyankhula nawe pa nthawi ya ulamuliro wa Yosiya mpaka lero lino. 3Mwina mwake anthu a ku Yuda adzamva za zoopsa zonse zimene ndakonza kuti ndiwachitire, ndipo munthu aliyense adzatembenuka ndi kusiya ntchito zake zoyipa. Motero ndidzawakhululukira zoyipa zawo ndi machimo awo.”

4Tsono Yeremiya anayitana Baruki mwana wa Neriya. Baruki analemba mʼbuku mawu onse amene Yeremiya ankamuwuza, mawu amene Yehova anamuwuza Yeremiya. 5Kenaka Yeremiya anawuza Baruki kuti, “Ine andiletsa kupita ku Nyumba ya Mulungu. 6Tsono iwe upite ku Nyumba ya Yehova pa tsiku losala kudya ndipo ukawerenge mawu a Yehova ochokera mʼbukumu amene ndinakulembetsa anthu onse akumva. Ukawawerengere anthu onse a ku Yuda amene amabwera ku Nyumba ya Mulungu kuchokera ku mizinda yawo. 7Mwina mwake adzapempha kwa Yehova ndipo aliyense adzatembenuka ndi kusiya makhalidwe ake oyipa pakuti mkwiyo ndi ukali wa Yehova pa anthu awa ndi woopsa kwambiri.”

8Baruki mwana wa Neriya anachita zonse zimene mneneri Yeremiya anamuwuza kuti achite. Mʼnyumba ya Yehova, iye anawerenga mawu a Yehova ochokera mʼbukulo. 9Pa mwezi wachisanu ndi chinayi wa chaka chachisanu cha Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya Yuda, anthu onse a mu Yerusalemu ndi onse amene anabwera kumeneko kuchokera ku mizinda ya Yuda, anapangana za kusala kudya kuti apepese Yehova. 10Atayima pa chipinda cha Gemariya mwana wa mlembi Safani, chimene chinali mʼbwalo lapamwamba, pafupi ndi Chipata Chatsopano cholowera ku Nyumba ya Yehova, Baruki anawerenga mawu onse a Yeremiya amene anali mʼbuku muja kwa anthu onse amene anali ku Nyumba ya Yehova.

11Mikaya mwana wa Gemariya, mwana wa Safani, atamva mawu onse a Yehova ochokera mʼbukumo, 12anapita ku nyumba ya mfumu nakalowa ku chipinda cha mlembi. Akuluakulu, mlembi Elisama, Delaya mwana wa Semaya, Elinatani mwana wa Akibori, Gemariya mwana wa Safani, Zedekiya mwana wa Hananiya pamodzi ndi akuluakulu ena onse, anali atasonkhana kumeneko. 13Tsono Mikaya anawafotokozera mawu onse amene anamva pamene Baruki ankawerenga buku lija anthu onse akumva. 14Pambuyo pake akuluakulu onsewo anatuma Yehudi mwana wa Netaniya, mwana wa Selemiya, mwana wa Kusi, kwa Baruki kukamuwuza kuti, “Bwera ndi buku limene unawerenga kwa anthu.” Ndipo Baruki mwana wa Neriya anapita nalo bukulo kwa anthuwo. 15Iwo anati, “Khala pansi, ndipo tiwerengere bukuli.”

Ndipo Baruki anawawerengera. 16Atamva mawu onsewo, anayangʼanana mwa mantha ndipo anamuwuza Baruki kuti, “Ndithudi tikafotokozera mfumu mawu onsewa.” 17Tsono anamufunsa Baruki kuti, “Tatiwuze, unalemba bwanji mawu onsewa? Kodi ndi Yeremiya anakulembetsa zimenezi?”

18Baruki anayankha kuti, “Inde, ndi Yeremiya amene anandiwuza mawu onsewa, ndipo ine ndinawalemba ndi utoto mʼbukumu.”

19Kenaka akuluakuluwo anamuwuza Baruki kuti, “Iweyo ndi Yeremiya, pitani mukabisale. Munthu aliyense asadziwe kumene muli.”

20Atayika bukulo mʼchipinda cha mlembi Elisama, analowa mʼbwalo, napita kwa mfumu ndi kukayifotokozera zonse. 21Itamva zimenezi mfumu inatuma Yehudi kuti akatenge bukulo, ndipo Yehudi anakalitenga ku chipinda cha mlembi Elisama ndipo anawerengera mfumu pamodzi ndi akuluakulu ake amene anali naye. 22Unali mwezi wachisanu ndi chinayi ndipo mfumu inali mʼnyumba ya pa nyengo yozizira, ikuwotha moto umene anasonkha. 23Yehudi ankati akawerenga masamba atatu kapena anayi a bukulo, mfumu inkawangʼamba ndi mpeni ndi kuwaponya pa moto ndipo anapitiriza kuchita zimenezi mpaka buku lonse linapsa. 24Mfumu pamodzi ndi omutumikira ake onse amene anamva mawu onsewa sanachite mantha kapena kungʼamba zovala zawo. 25Ngakhale kuti Elinatani, Delaya, ndi Gemariya anapempha mfumu kuti isatenthe bukulo, mfumuyo sinawamvere. 26Mʼmalo mwake, mfumu inalamula Yerahimeeli mwana wake, Seraya mwana wa Azirieli ndi Selemiya mwana wa Abideeli kuti agwire mlembi Baruki ndi mneneri Yeremiya. Koma pamenepo nʼkuti Yehova atawabisa.

27Mfumu itatentha buku limene linali ndi mawu amene Yeremiya anamulembetsa Baruki, Yehova anayankhula ndi Yeremiya kuti, 28“Tenganso buku lina ndipo ulembe mawu onse amene anali mʼbuku loyamba lija, limene Yehoyakimu analitentha. 29Ndiponso akamuwuze Yehoyakimu mfumu ya Yuda kuti, ‘Yehova akuti: Iwe unatentha buku lija ndipo unati: Nʼchifukwa chiyani unalemba kuti mfumu ya ku Babuloni idzabwera ndithu kudzawononga dziko lino ndi kupha anthu pamodzi ndi nyama zomwe?’ 30Nʼchifukwa chake kunena za Yehoyakimu mfumu ya Yuda Yehova akuti sipadzaoneka munthu wina wolowa mʼmalo mwake pa mpando wa Davide. Akadzafa mtembo wake udzaponyedwa kunja ndipo udzakhala pa dzuwa masana, ndi pachisanu chowundana usiku. 31Ndidzamulanga pamodzi ndi ana ake ndiponso omutumikira ake chifukwa cha zoyipa zawo; ndidzagwetsa pa iwo ndi pa onse amene akukhala mu Yerusalemu ndiponso pa anthu a ku Yuda masautso onse amene ndinawanena, chifukwa sanamvere.”

32Choncho Yeremiya anatenga buku lina napatsa mlembi Baruki mwana wa Neriya, ndipo Yeremiya anamulembetsa mawu onse amene anali mʼbuku limene Yehoyakimu mfumu ya Yuda anatentha. Ndipo anawonjezerapo mawu ambiri monga omwewo.

Hoffnung für Alle

Jeremia 36:1-32

Baruch liest Jeremias Schriftrolle im Tempel vor

1Im 4. Regierungsjahr von König Jojakim, dem Sohn von Josia, sprach der Herr zu Jeremia: 2»Nimm eine Schriftrolle und schreib alle Botschaften auf, die ich dir für Israel, Juda und die anderen Völker gegeben habe, von der Regierungszeit Josias an bis zum heutigen Tag! 3Wenn die Bewohner Judas von dem Unheil hören, das ich über sie bringen will, werden sie vielleicht von ihren falschen Wegen umkehren und ihr Leben ändern. Dann will ich ihre Schuld und ihre Sünde vergeben.«

4Da rief Jeremia Baruch, den Sohn von Nerija, zu sich und diktierte ihm alles, was der Herr zu ihm gesprochen hatte. Baruch schrieb es auf eine Schriftrolle. 5Dann gab Jeremia ihm den Auftrag: »Ich darf den Tempel nicht mehr betreten. 6Darum geh du dorthin und lies die Worte des Herrn vor, so wie ich sie dir diktiert habe! Alle Einwohner Jerusalems und der anderen Städte Judas sollen sie hören, wenn sie sich am Fastentag im Tempel versammeln. 7Vielleicht flehen sie dann den Herrn um Gnade an und kehren von ihren falschen Wegen um, denn der Herr ist voller Zorn über sie und hat ihnen großes Unheil angedroht.«

8Baruch befolgte Jeremias Anweisungen und verkündete die Botschaft des Herrn im Tempel. 9Im 9. Monat des 5. Regierungsjahres von Jojakim, dem Sohn von Josia, hatte man nämlich das ganze Volk zum Fasten aufgerufen, um den Herrn um Gnade zu bitten. Viele Menschen aus Jerusalem und den anderen Städten Judas waren dazu in den Tempel gekommen. 10Baruch las Jeremias Worte vor den versammelten Israeliten vor, und alle hörten gespannt zu. Er saß in der Kammer von Gemarja, der ein Sohn des Hofsekretärs Schafan war; die Kammer lag am oberen Vorhof, dicht beim Neuen Tor des Tempels.

11Als Michaja, ein Sohn von Gemarja und Enkel von Schafan, die Worte des Herrn hörte, 12lief er zum Königspalast und ging in den Raum des Hofsekretärs. Dort saßen alle führenden Männer beieinander: der Hofsekretär Elischama, Delaja, der Sohn von Schemaja, Elnatan, der Sohn von Achbor, Gemarja, der Sohn von Schafan, Zedekia, der Sohn von Hananja, und die übrigen hohen Würdenträger. 13Michaja berichtete ihnen, was Baruch vor allen Leuten aus der Schriftrolle vorgelesen hatte. 14Da schickten die führenden Männer einen Mann namens Jehudi, den Sohn von Netanja, Enkel von Schelemja und Urenkel von Kuschi, zu Baruch und ließen ihm sagen: »Komm zu uns und bring die Schriftrolle mit!« Baruch nahm sie und ging zu ihnen.

15»Setz dich und lies uns daraus vor«, baten sie ihn. Und so las Baruch ihnen alles vor. 16Als die Männer die Weissagungen hörten, schauten sie sich entsetzt an und sagten zu Baruch: »Wir müssen das unbedingt dem König melden! 17Wie bist du dazu gekommen, dies alles aufzuschreiben? Hat Jeremia dir das gesagt?« 18»Jeremia hat mir jedes Wort diktiert«, antwortete Baruch, »und ich habe alles mit Tinte auf dieser Schriftrolle niedergeschrieben.«

19»Ihr müsst euch verstecken, du und Jeremia«, rieten die Männer. »Niemand darf wissen, wo ihr seid!«

Jojakim verbrennt die Schriftrolle

20Sie bewahrten die Rolle im Raum des Hofsekretärs Elischama auf, gingen in den inneren Hof des Palasts und erstatteten dem König Bericht. 21Jojakim ließ Jehudi die Schriftrolle aus dem Raum von Elischama holen. Dann las Jehudi sie dem König und den führenden Männern vor, die sich um ihn versammelt hatten.

22Weil es der 9. Monat des Jahres war, saß der König im Winterhaus, und vor ihm stand ein Kohlenbecken, in dem ein Feuer brannte. 23Sobald Jehudi drei oder vier Spalten vorgelesen hatte, schnitt der König sie mit einem Federmesser ab und warf sie ins Feuer, bis er die ganze Schriftrolle verbrannt hatte.

24Weder der König noch seine Würdenträger waren entsetzt über das, was sie gehört hatten; niemand zerriss in Trauer sein Gewand. 25Nur Elnatan, Delaja und Gemarja flehten den König an, die Schriftrolle nicht zu verbrennen, aber er hörte nicht auf sie. 26Er befahl dem Prinzen Jerachmeel sowie Seraja, dem Sohn von Asriël, und Schelemja, dem Sohn von Abdeel, sie sollten den Schreiber Baruch und den Propheten Jeremia gefangen nehmen. Aber der Herr sorgte dafür, dass man die beiden nicht fand.

Baruch schreibt Gottes Botschaft noch einmal auf

27Nachdem der König die Schriftrolle verbrannt hatte, die Jeremia Baruch diktiert hatte, gab der Herr Jeremia den Auftrag:

28»Nimm eine andere Rolle und schreib noch einmal alle Botschaften nieder, die auf der ersten standen! 29Richte Jojakim aus:

So spricht der Herr: Du hast die erste Rolle verbrannt und Jeremia gefragt: ›Warum kündigst du an, dass der König von Babylonien unser Land ganz bestimmt angreifen und zu einer Wüste machen wird, in der es keine Menschen und Tiere mehr gibt?‹ 30Höre nun, König von Juda, was ich, der Herr, über dich sage:

In Zukunft wird niemand aus deiner Familie mehr als Nachfolger von David über Juda regieren. Deine Leiche wird man draußen liegen lassen, tagsüber ist sie der Hitze und nachts der Kälte ausgesetzt. 31Ich bestrafe dich, deine Nachkommen und deine Würdenträger wegen eurer Schuld. Ja, über euch, über die Einwohner Jerusalems und alle Judäer lasse ich das Unheil hereinbrechen, das ich euch angedroht habe, denn ihr wolltet nicht auf mich hören!«

32Jeremia nahm eine andere Schriftrolle und gab sie dem Schreiber Baruch, dem Sohn von Nerija. Baruch schrieb nach Jeremias Anweisung alle Botschaften der alten Rolle nieder, die König Jojakim von Juda verbrannt hatte. Außerdem wurden noch viele ähnliche Weissagungen hinzugefügt.