Yeremiya 21 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yeremiya 21:1-14

Mulungu Akana Pempho la Zedekiya

1Mfumu Zedekiya inatuma Pasuri mwana wa Malikiya ndi wansembe Zefaniya mwana wa Maseya kwa Yeremiya. 2Iwo amati akanene kwa Yeremiya mawu akuti, “Tinenere kwa Yehova chifukwa Nebukadinezara mfumu ya Babuloni akutithira nkhondo. Mwina mwake Yehova nʼkutichitira zodabwitsa kuti Nebukadinezarayo achoke kwathu kuno.”

3Koma Yehova anawuza Yeremiya kuti ayankhe Pasuri ndi Zefaniya kuti, “Kamuwuzeni Zedekiya kuti, 4‘Yehova, Mulungu wa Israeli akuti ndikulandeni zida zimene zili mʼmanja mwanu zimene mukugwiritsa ntchito polimbana ndi mfumu ya ku Babuloni ndi ankhondo ake amene akuzingani kunja kwa lingali. Ndipo ndidzasonkhanitsa zidazo mʼkati mwa mzindawu. 5Ineyo mwini wakene ndi mkono wotambasula ndi dzanja lamphamvu, ndidzachita nanu nkhondo ndili wokwiya, wokalipa ndi waukali. 6Ndidzakantha amene amakhala mu mzinda muno, anthu pamodzi ndi zirombo, ndipo zidzafa ndi mliri woopsa. 7Pambuyo pake, ndidzapereka Zedekiya mfumu ya ku Yuda, nduna zake pamodzi ndi anthu a mu mzinda muno amene adzapulumuke pa nthawi ya mliri, lupanga ndi njala kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni ndi kwa adani awo amene ankafuna kuwapha. Iye adzawapha ndi lupanga. Sadzawachitira chifundo kapena kuwamvera chisoni kapenanso kuwakomera mtima.’

8“Yehova anati ndiwawuzenso anthu amenewa kuti asankhe pakati pa moyo ndi imfa. 9Aliyense amene akhale mu mzinda muno adzaphedwa ndi lupanga, njala kapena mliri. Koma aliyense amene apite kukadzipereka kwa Ababuloni amene akuzinganiwa adzakhala ndi moyo, adzapulumuka. 10Ine ndatsimikiza kuchitira mzinda uno choyipa osati chabwino, akutero Yehova. Udzaperekedwa mʼdzanja la mfumu ya ku Babuloni, ndipo iyeyo adzawutentha ndi moto.

11“Komanso, uwuze banja laufumu la Yuda kuti, ‘Imva mawu a Yehova; 12inu a mʼbanja la Davide, Yehova akuti,

“ ‘Weruzani mwachilungamo mmawa uliwonse;

pulumutsani mʼdzanja la wozunza

aliyense amene walandidwa katundu wake,

kuopa kuti ukali wanga ungabuke

ndi kuyaka ngati moto wosazimitsika

chifukwa cha zoyipa zimene mwachita.

13Ndidzalimbana nanu,

inu amene mukukhala pamwamba pa chigwa,

inu okhala ngati thanthwe lapachidikha,

akutero Yehova.

Inu amene mumanena kuti, ‘Ndani amene angabwere kudzalimbana nafe?

Ndani amene angathe kulowa mʼmalinga mwathu?’

14Ndidzakulangani molingana ndi ntchito zanu,

akutero Yehova.

Ndidzatentha nkhalango zanu;

moto udzapsereza zonse zimene zakuzungulirani.’ ”