Yeremiya 18 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yeremiya 18:1-23

Ku Nyumba ya Wowumba Mbiya

1Yehova anawuza Yeremiya kuti, 2“Pita ku nyumba ya munthu wowumba mbiya, ndipo kumeneko ndikakuwuza mawu anga.” 3Choncho ndinatsikira ku nyumba ya wowumba mbiya, ndipo ndinamuona akuwumba mbiya pa mkombero. 4Tsono amati ngati mbiya imene waumba ikhala yosawumbika bwino ankayiphwanya nʼkuwumbanso ina monga mmene afunira ndi dothi lake lomwe lija.

5Kenaka Yehova anandiwuza kuti, 6“Inu Aisraeli, kodi Ine sindingathe kuchita nanu monga amachitira wowumba mbiya?” akutero Yehova. “Inu muli mʼmanja mwanga ngati mtapo mʼmanja mwa wowumba mbiya. 7Ngati nditalengeza kuti mtundu wina wa anthu kapena ufumu wina ndiwuzula, kuwugwetsa ndi kuwuwononga, 8ndipo ngati mtundu wa anthu umene ndawuchenjezawo ulapa zoyipa zawo, ndiye kuti Ine ndidzaleka ndipo sindidzabweretsa pa anthuwo mavuto amene ndinakonzekera kuwachitira. 9Ndipo ngati ndilengeza kuti ndikufuna kumanga ndi kukhazikitsa mtundu wa anthu kapena ufumu. 10Koma mtunduwo ukachita choyipa pamaso panga nʼkusandimvera, ndiye kuti sindidzawuchitiranso zabwino zimene ndimafuna ndiwuchitire.

11“Ndipo tsopano kawawuze anthu a ku Yuda ndi amene akukhala mu Yerusalemu kuti, ‘Yehova akuti, Taonani! Ndikukukonzerani mavuto, ndi kuganizira zoti ndikulangeni. Kotero siyani makhalidwe anu oyipa aliyense wa inu, ndipo mukonzenso makhalidwe anu ndi zochita zanu.’ 12Koma iwo adzayankha kuti, ‘Zimenezo nʼzosathandiza. Ife tidzapitiriza kuchita zomwe takonzekera; aliyense wa ife adzatsatira zoyipa za mtima wake wokanika.’ ”

13Yehova akuti,

“Uwafunse anthu a mitundu ina kuti:

Kodi ndani anamvapo zinthu zofanana ndi zimenezi?

Israeli amene anali ngati namwali wanga wachita

chinthu choopsa kwambiri.

14Kodi chisanu chimatha pa matanthwe

otsetsereka a phiri la Lebanoni?

Kodi madzi ozizira amitsinje ochokera

ku phiri la Lebanoni adzamphwa?

15Komatu anthu anga andiyiwala;

akufukiza lubani kwa mafano achabechabe.

Amapunthwa mʼnjira

zawo zakale.

Amayenda mʼnjira zachidule

ndi kusiya njira zabwino.

16Dziko lawo amalisandutsa chipululu,

chinthu chochititsa manyazi nthawi zonse;

onse odutsapo adzadabwa kwambiri

ndipo adzapukusa mitu yawo.

17Ngati mphepo yochokera kummawa,

ndidzawabalalitsa pamaso pa adani awo;

ndidzawafulatira osawathandiza

pa tsiku la mavuto awo.”

18Anthuwo anati, “Tiyeni, tipangane zoti timuchitire Yeremiya; pakuti ansembe otiphunzitsa malamulo tidzakhala nawobe. Anthu anzeru otilangiza tidzakhala nawo, ndiponso aneneri otilalikira mawu. Choncho tiyeni timupezere chifukwa ndipo tisamvere chilichonse chimene akunena.”

19Ndipo ndinapemphera kwa Yehova kuti, “Inu Yehova, ndimvereni;

imvani zimene adani anga akunena za ine!

20Kodi chinthu choyipa nʼkukhala dipo la chinthu chabwino?

Komabe iwo andikumbira dzenje.

Kumbukirani kuti ndinadzayima pamaso panu

kudzawapempherera

kuti muwachotsere mkwiyo wanu.

21Choncho langani ana awo ndi njala;

aperekeni kuti aphedwe ndi lupanga.

Akazi awo asanduke opanda ana ndi amasiye;

amuna awo aphedwe ndi mliri,

anyamata awo aphedwe ndi lupanga ku nkhondo.

22Kulira kumveke kuchokera mʼnyumba zawo

mutawatumizira gulu lankhondo mwadzidzidzi kuti liwakanthe.

Iwo andikumbira dzenje kuti ndigweremo

ndipo atchera msampha mapazi anga.

23Koma Inu Yehova, mukudziwa

ziwembu zawo zonse zofuna kundipha.

Musawakhululukire zolakwa zawo

kapena kufafaniza machimo awo pamaso panu.

Agonjetsedwe pamaso panu;

muwalange muli wokwiya.”