Yakobo 4 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yakobo 4:1-17

Kugonjera Mulungu

1Nʼchiyani chimene chimayambitsa ndewu ndi mapokoso pakati panu? Kodi sizichokera ku zilakolako zimene zimalimbana mʼkati mwanu? 2Mumalakalaka zinthu koma simuzipeza, choncho mumapha. Mumasirira zinthu koma simutha kuzipeza zimene mukufuna, choncho mumakangana ndi kumenyana. Mulibe zinthuzo chifukwa simupempha kwa Mulungu. 3Koma ngakhale mumapempha simulandira, chifukwa mumapempha ndi zolinga zoyipa. Mumapempha kuti muzigwiritse ntchito pa zokusangalatsani nokha.

4Inu anthu achigololo, kodi simukudziwa kuti kuchita ubwenzi ndi dziko lapansi ndi kudana ndi Mulungu? Choncho, aliyense wosankha kukhala bwenzi la dziko lapansi amasanduka mdani wa Mulungu. 5Kapena mukuganiza kuti Malemba amanena popanda chifukwa kuti Mulungu amafunitsitsa mwansanje mzimu umene Iye anayika kuti uzikhala mwa ife? 6Koma amatipatsa chisomo chochuluka. Nʼchifukwa chake Malemba amati,

“Mulungu amatsutsa odzikuza,

koma apereka chisomo kwa odzichepetsa.”

7Dziperekeni nokha kwa Mulungu. Mukaneni Mdierekezi ndipo adzakuthawani. 8Sendezani kufupi ndi Mulungu ndipo Iye adzasendeza kwa inu. Sambani mʼmanja mwanu, inu anthu ochimwa. Yeretsani mitima yanu, inu anthu okayikira. 9Chitani chisoni chifukwa cha zimene mwachita, lirani misozi. Kuseka kwanu kusanduke kulira, ndipo chimwemwe chanu chisanduke chisoni. 10Dzichepetseni pamaso pa Ambuye ndipo Iye adzakukwezani.

11Abale musamanenane. Aliyense wonenera zoyipa mʼbale wake kapena kumuweruza, akusinjirira ndi kuweruza Malamulo. Pamene muweruza malamulo, ndiye kuti simukusunga malamulowo, koma mukuwaweruza. 12Pali mmodzi yekha Wopereka Malamulo ndi Woweruza. Ndiye amene akhoza kupulumutsa ndi kuwononga. Kodi ndiwe yani kuti uziweruza mnzako?

Kunyadira za Mawa

13Tsono tamverani, inu amene mumati, “Lero kapena mawa tipita ku mzinda wakutiwakuti, tikatha chaka chimodzi tikuchita malonda ndi kupanga ndalama.” 14Chifukwa chiyani mukutero? Inu simukudziwa zimene ziti zichitike mawa. Kodi moyo wanu ndi wotani? Inu muli ngati nkhungu imene imangooneka kwa kanthawi kochepa ndipo kenaka ndikuzimirira. 15Koma inuyo muyenera kunena kuti, “Ambuye akalola, tikadzakhala ndi moyo, tidzachita zakutizakuti.” 16Koma mmene zililimu mumangodzitama ndi kudzikuza. Kudzitama konse kotereku ndi koyipa. 17Aliyense amene amadziwa zabwino zimene amayenera kuchita koma osazichita, ndiye kuti wachimwa.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

雅各書 4:1-17

不要與世俗為友

1你們彼此衝突、互相鬥毆的起因是什麼呢?不就是你們身體中不斷交戰的慾望嗎? 2你們貪心,得不到就去殺人。你們嫉妒,得不到就爭吵、打鬥。你們得不到是因為你們不向上帝祈求。 3你們求也得不到是因為你們動機不純,只求享樂和滿足自己的慾望。 4你們這些對主不忠的人啊,難道還不明白與世俗為友就是與上帝爲敵嗎?所以,凡是與世俗為友的,都是上帝的敵人。 5聖經上說:「上帝所賜、住在我們心裡的聖靈深願我們完全屬於祂。」你們以為這是空談嗎? 6但上帝賜給我們更大的恩典,所以聖經上說:「上帝阻擋驕傲的人,恩待謙卑的人。」

7因此,你們要服從上帝,抵擋魔鬼,魔鬼必逃離你們。 8你們親近上帝,上帝就必親近你們。有罪的人啊,洗淨你們的手吧!三心二意的人啊,潔淨你們的心吧! 9你們要悲傷、憂愁、痛哭,轉歡笑為悲哀,變歡樂為愁苦。 10你們要在主面前謙卑,祂必擢升你們。

不要論斷

11弟兄姊妹,不要彼此批評。批評、論斷弟兄姊妹就等於是批評、論斷律法。如果你論斷律法,你就不是遵行律法的人,而是以審判者自居。 12設立律法和審判人的只有一位,就是能拯救人也能毀滅人的上帝。你是誰,竟然論斷別人呢?

警戒自誇

13你們有些人說:「今天或是明天,我們要往某某城去,在那裡逗留一年半載,做生意賺錢。」 14其實你們根本不知道明天會發生什麼事。你們的生命是什麼呢?你們只不過像一陣霧氣,出現片刻,就無影無蹤了。 15你們只當說:「如果主許可,我們就可以活著,可以做這事或做那事。」 16現在,你們竟敢傲慢自誇,這實屬邪惡。 17所以人若知道善而不去行,就是犯罪。