Numeri 23 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Numeri 23:1-30

Uthenga Woyamba wa Balaamu

1Balaamu anati kwa Balaki, “Mundimangire maguwa ansembe asanu ndi awiri pano, ndipo mukonzenso ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri ndi nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri.” 2Balaki anachita monga Balaamu ananenera ndipo awiriwo anapereka ngʼombe imodzi ndi nkhosa yayimuna imodzi pa guwa lansembe lililonse.

3Kenaka Balaamu anati kwa Balaki, “Khalani pano pafupi ndi nsembe yanu ineyo ndipite pambali. Mwina Yehova adzabwera kuti akumane nane. Chilichonse chimene akandionetse ndidzakuwuzani” Choncho anapita ku malo okwera a chipululu.

4Mulungu anakumana naye ndipo Balaamu anati, “Ndakonza maguwa asanu ndi awiri ndipo pa guwa lililonse ndaperekapo nsembe ya ngʼombe yayimuna imodzi ndi nkhosa yayimuna imodzinso.”

5Yehova anawuza Balaamu kuti, “Bwerera kwa Balaki ndipo ukamuwuze uthenga uwu.”

6Ndipo anabwerera kwa iye namupeza atayima pafupi ndi nsembe yake pamodzi ndi akuluakulu onse a Mowabu. 7Ndipo Balaamu ananena uthenga wake:

“Balaki ananditenga kuchoka ku Aramu,

mfumu ya ku Mowabu kuchokera ku mapiri a kummawa.

Iye anati, ‘Bwera, temberera Yakobo mʼmalo mwanga,

pita nyoza Israeli.’

8Ndingatemberere bwanji

amene Mulungu sanawatemberere?

Ndinganyoze bwanji

amene Yehova sanawanyoze?

9Kuchokera pamwamba pa mapiri ndikuona anthu,

ndikuwaona kuchokera pa zitunda.

Ndikuona anthu okhala pawokha,

osakhala mʼgulu limodzi ndi mitundu ina.

10Ndani angawerenge zidzukulu za Yakobo zochuluka ngati fumbi,

kapena chimodzi mwa zigawo zinayi za Israeli?

Lekeni ndife imfa ya oyera mtima,

ndi chimaliziro changa chikhale ngati chawo!”

11Balaki anati kwa Balaamu, “Wandichitira chiyani? Ndinakuyitana kuti utemberere adani anga, ndipo taona, sunachite chilichonse koma kuwadalitsa!”

12Iye anayankha kuti, “Kodi sindinayenera kuyankhula zimene Yehova anandiwuza?”

Uthenga Wachiwiri wa Balaamu

13Kenaka Balaki anawuza Balaamu kuti, “Tiye tipite limodzi ku malo ena komwe ungawaone. Udzangoona gulu limodzi osati onsewo. Ndipo pamenepo, ukawatemberere mʼmalo mwanga.” 14Tsono anamutengera ku munda wa Zofimu pamwamba pa phiri la Pisiga ndipo kumeneko anamanga maguwa ansembe asanu ndi awiri ndipo anapereka nsembe ngʼombe yayimuna imodzi ndi nkhosa yayimuna imodzi pa guwa lansembe lililonse.

15Balaamu anawuza Balaki kuti, “Khalani pano pafupi ndi nsembe yanu pamene ine ndikukakumana ndi Mulungu cha uko.”

16Yehova anakumana ndi Balaamu ndipo anamuyankhula kuti, “Bwerera kwa Balaki ndipo ukamuwuze uthenga uwu.”

17Ndipo anapita kwa iye ndipo anamupeza atayimirira pafupi ndi nsembe yake pamodzi ndi akuluakulu a ku Mowabu. Balaki anafunsa Balaamu kuti, “Yehova wayankhula chiyani?”

18Pamenepo Balaamu ananena uthenga wake:

“Nyamuka Balaki ndipo tamvera;

Undimvere iwe mwana wa Zipori.

19Mulungu si munthu kuti aname,

kapena mwana wa munthu kuti asinthe maganizo ake.

Kodi amayankhula koma osachita?

Kodi amalonjeza koma osakwaniritsa?

20Wandilamula kuti ndidalitse,

Iyeyo wadalitsa ndipo sindingasinthe.

21“Palibe kuwukira kulikonse kumene wakuona mwa Yakobo,

sanaone chovuta mu Israeli.

Yehova Mulungu wawo ali nawo:

mfuwu wa mfumu uli pakati pawo.

22Mulungu wowatulutsa mʼdziko la Igupto,

ali ndi mphamvu ngati za njati.

23Palibe matsenga amene angalimbane ndi Yakobo,

palibe mawula amene angalimbane ndi Israeli.

Tsopano za Yakobo ndi Israeli adzanena kuti,

‘Onani zimene Mulungu wachita!’

24Taonani, anthu anyamuka ngati mkango waukazi;

adzuka okha ngati mkango waumuna

umene supuma mpaka utadya nyama imene wagwira

ndi kumwa magazi a nyama yogwidwayo.”

25Ndipo Balaki anati kwa Balaamu, “Usawatemberere ndi pangʼono pomwe kapena kuwadalitsa!

26“Balaamu anayankha Balaki kuti, ‘Kodi sindinakuwuzeni kuti ndiyenera kuchita zimene Yehova wanena?’ ”

Uthenga Wachitatu wa Balaamu

27Kenaka Balaki anati kwa Balaamu, “Bwera ndikutengere ku malo ena. Mwina chidzamukondweretsa Mulungu kuti uwatemberere kumeneko mʼmalo mwanga.” 28Ndipo Balaki anamutengera Balaamu pamwamba pa Peori, poyangʼanana ndi chipululu.

29Balaamu anati kwa Balaki, “Mundimangire maguwa ansembe asanu ndi awiri pano ndipo mundikonzere ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri.” 30Balaki anachita monga Balaamu ananenera ndipo anapereka nsembe ngʼombe imodzi yayimuna ndi nkhosa imodzi yayimuna pa guwa lililonse.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

民数记 23:1-30

巴兰的预言

1巴兰巴勒说:“你在这里为我筑七座祭坛,预备七头公牛和七只公绵羊。” 2巴勒就照巴兰的话做了。他们二人在每座坛上献上一头公牛和一只公绵羊, 3巴兰巴勒说:“你留在燔祭旁边,我到前面去,也许耶和华会来见我。无论祂有什么指示,我必告诉你。” 4上帝果然向巴兰显现。巴兰对上帝说:“我已经预备了七座祭坛,每座祭坛上献了一头公牛和一只公绵羊。” 5耶和华告诉他当说的话,命他回去转告巴勒6巴兰就回到巴勒那里,看见他和摩押的臣仆们都站在燔祭旁边。 7巴兰吟诗预言说:

巴勒引我出亚兰

摩押王请我出东山,

说,‘来为我咒诅雅各

来斥责以色列!’

8上帝没有咒诅的,

我怎能咒诅?

耶和华没有斥责的,

我怎能斥责?

9我从峰顶观看他们,

从高岗眺望他们,

这独居一方之民,

不与万国同列。

10雅各的子孙多如尘土,

谁能数得清?

谁能数清以色列人的四分之一?

我愿像义人一样死去,

如义人般终此一生。”

11巴勒巴兰说:“你这是做什么?我请你来咒诅我的仇敌,你竟祝福他们!” 12巴兰说:“耶和华让我说的话,我岂能不说?”

巴兰第二次预言

13巴勒说:“请你跟我去另一个地方,那里看不见全部以色列人,只能看见一部分,你要在那里为我咒诅他们。” 14他领巴兰上到毗斯迦山顶的琐腓田,在那里筑了七座祭坛,每座坛上都献了一头公牛和一只公绵羊。 15巴兰巴勒说:“你留在这些燔祭旁边,我到那边去见耶和华。” 16耶和华向巴兰显现,告诉他当说的话,让他转告巴勒17巴兰回到巴勒那里,看见他和摩押的臣仆们都站在燔祭旁边。巴勒问道:“耶和华说了什么?” 18巴兰吟诗预言说:

巴勒啊,要留心听!

西拨的儿子啊,请听我言。

19上帝并非世人,祂不撒谎;

上帝不是凡人,祂不反悔。

祂言出必行,信守承诺。

20我奉命祝福,祂已赐福,

我不能改变。

21雅各的子孙中未见有罪恶,

以色列人中看不见有祸患。

他们的上帝耶和华与他们同在,

他们向自己的君王欢呼。

22上帝把他们带出埃及

23:22 ”有古卷作“他们”。的力量如野牛之角。

23没有邪术能害雅各

没有咒语可伤以色列

时候一到,人们必谈论雅各

谈论以色列,说,‘看啊,

上帝的作为何等伟大!’

24看啊,这民族挺身如母狮,

又像雄狮一跃而起,

不吞掉猎物不罢休,

不喝饱猎物的血不躺卧。”

25巴勒巴兰说:“你可以不咒诅他们,但也不该为他们祝福啊!” 26巴兰回答说:“我不是说过,我必须按耶和华的指示做吗?”

27巴勒说:“来吧,我带你去另一个地方,也许上帝会同意你在那里为我咒诅他们。” 28他领着巴兰登上俯瞰旷野的毗珥山顶。 29巴兰巴勒说:“你在这里为我筑七座祭坛,预备七头公牛和七只公绵羊。” 30巴勒就照巴兰的话在每座祭坛上献了一头公牛和一只公绵羊。