Numeri 21 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Numeri 21:1-35

Kuwonongedwa kwa Aradi

1Mfumu ya Akanaani ya ku Aradi, imene inkakhala ku Negevi, itamva kuti Aisraeli akubwera kudzera msewu wopita ku Atarimu, inachita nkhondo ndi Aisraeli nigwira ena mwa iwo. 2Ndipo Israeli anachita lonjezo ili kwa Yehova: “Mukapereka anthu awa mʼdzanja lathu ife tidzawonongeratu mizinda yawo.” 3Yehova anamva pempho la Aisraeli ndipo anapereka Akanaaniwo kwa iwo. Anawawononga pamodzi ndi mizinda yawo. Kotero malowo anatchedwa Horima.

Njoka Yamkuwa

4Aisraeli anayenda kuchokera ku phiri la Hori kudzera njira ya ku Nyanja Yofiira kuzungulira dziko la Edomu. Koma anthu anataya mtima mʼnjiramo 5ndipo anayankhula motsutsana ndi Mulungu ndi Mose, nati, “Chifukwa chiyani munatitulutsa kuchoka mʼdziko la Igupto kuti tidzafere mʼchipululu muno? Kuno kulibe chakudya, kulibe madzi ndipo chakudya cha chabechabechi tatopa nacho.”

6Choncho Yehova anatumiza njoka zaululu pakati pawo. Zinaluma anthu ndipo Aisraeli ambiri anafa. 7Anthuwo anabwera kwa Mose ndi kunena kuti, “Tachimwa chifukwa tayankhula motsutsana ndi Yehova komanso inu. Pempherani kwa Yehova kuti atichotsere njokazi.” Tsono Mose anapempherera anthuwo.

8Yehova anati kwa Mose, “Upange njoka yaululu ndipo uyipachike pa mtengo. Aliyense amene walumidwa akangoyangʼana njokayo adzakhala ndi moyo.” 9Pamenepo Mose anapanga njoka yamkuwa ndi kuyipachika pa mtengo. Ndipo aliyense wolumidwa akayangʼana njoka yamkuwayo ankakhala ndi moyo.

Ulendo wa ku Mowabu

10Aisraeli anayendabe nakamanga misasa yawo ku Oboti. 11Kenaka anasamuka ku Oboti nakamanga misasa yawo ku Iye-Abarimu, mʼchipululu chimene chili kummawa kwa Mowabu, kotulukira dzuwa. 12Kuchoka kumeneko anayendabe nakamanga misasa yawo mʼchigwa cha Zeredi. 13Anasamukanso kumeneko nakamanga moyandikana ndi Arinoni mʼdera limene lili mʼchipululu chimene chimafika mʼdziko la Aamori. Arinoni ndiwo malire a Mowabu ndi Aamori. 14Nʼchifukwa chake Buku la Nkhondo za Yehova limati,

“Mzinda wa Wahebu uli mu Sufa,

mu zigwa za Arinoni, 15ku matsitso a zigwa

amene afika mpaka ku Ari

nakhudza malire a dziko la Mowabu.”

16Kuchokera kumeneko anapitirira mpaka ku Beeri, pa chitsime chomwe Yehova anawuza Mose kuti, “Sonkhanitsa anthu pamodzi ndipo ndidzawapatsa madzi.”

17Pamenepo Aisraeli anayimba nyimbo iyi:

“Tulutsa madzi, chitsime iwe!

Chiyimbireni nyimbo,

18chitsime chomwe anakumba mafumu,

chomwe anakumba anthu omveka,

ndi ndodo zawo zaufumu ndi ndodo zawo zoyendera.”

Kenaka anachoka ku chipululu ndi kupita ku Matana. 19Kuchoka ku Matana anapita ku Nahalieli, kuchoka ku Nahalieli anapita ku Bamoti, 20ndipo atachoka ku Bamoti anapita ku chigwa cha dziko la Mowabu kudzera njira ya pamwamba pa phiri la Pisiga, moyangʼanana ndi Yesimoni.

Kugonjetsedwa kwa Sihoni ndi Ogi

21Aisraeli anatumiza amithenga kwa Sihoni mfumu ya Aamori, kuti,

22“Tiloleni kuti tidutse mʼdziko mwanu. Sitidzapatukira mʼminda mwanu kapena mu mpesa wanu kapena kumwa madzi mʼchitsime chili chonse. Tidzayenda mu msewu waukulu wa mfumu mpaka titadutsa malire a dziko lanu.”

23Koma Sihoni sanalole kuti Aisraeli adutse mʼdziko mwake. Iye anasonkhanitsa pamodzi ankhondo ake onse kuti akamenyane ndi Aisraeli mʼchipululu. Atafika pa Yahazi anamenyana ndi Aisraeli. 24Koma Aisraeli anamupha ndi kulanda dziko lake kuchokera ku Arinoni mpaka ku Yaboki, kulekezera mʼmalire a dziko la Aamoni, chifukwa malire a dziko la Aamoni anali otetezedwa. 25Ndipo Aisraeli analanda mizinda yonse ya Aamori, nakhalamo kuphatikizapo Hesiboni ndi midzi yake yozungulira. 26Hesiboni unali mzinda wa Sihoni mfumu ya Aamori, yemwe anamenyana ndi mfumu yakale ya dziko la Mowabu. Lonselo linakhala dziko lake mpaka ku Arinoni.

27Nʼchifukwa chake alakatuli amati:

“Bwerani ku Hesiboni, mzindawo umangidwenso;

mzinda wa Sihoni ukhazikike.

28“Moto unabuka ku Hesiboni,

malawi a moto kuchokera mu mzinda wa Sihoni.

Unanyeketsa Ari mzinda wa ku Mowabu,

nzika za ku malo okwera a Arinoni.

29Tsoka kwa iwe Mowabu!

Mwawonongedwa inu anthu a ku Kemosi!

Ana ake aamuna wawasandutsa ngati anthu othawathawa

ndipo ana ake aakazi ngati akapolo,

akapolo a Sihoni, mfumu ya Aamori.

30“Koma ife tawagonjetsa;

Hesiboni wawonongedwa mʼnjira monse mpaka kufika ku Diboni.

Tawaphwasula mpaka ku mzinda wa Nofa,

mzinda womwe umafika ku Medeba.

31“Choncho Aisraeli anakhala mʼdziko la Aamori.”

32Mose atatumiza azondi ku Yazeri, Aisraeliwo analanda midzi yozungulira ndi kuthamangitsa Aamori omwe ankakhala kumeneko. 33Kenaka anabwerera, nadzera njira ya ku Basani. Choncho Ogi mfumu ya ku Basani ndi gulu lake lonse lankhondo anatuluka kukakumana nawo ndipo anamenyana nawo ku Ederi.

34Yehova anati kwa Mose, “Usachite naye mantha pakuti ndamupereka mʼmanja mwako pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo ndi dziko lake lomwe. Ndipo uchite kwa iye zimene unachita Sihoni mfumu ya Aamori, amene ankalamulira ku Hesiboni.”

35Choncho Aisraeli anapha Ogi pamodzi ndi ana ake aamuna ndi gulu lake lonse la nkhondo. Palibe ndi mmodzi yemwe amene anatsala wamoyo, ndipo analanda dziko lakelo.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

民数记 21:1-35

击败迦南人

1住在南地的迦南亚拉得王听说以色列人取道亚他林而来,就攻打他们,俘虏了一些人。 2以色列人向耶和华许愿说:“要是你将这些人交在我们手中,我们必彻底摧毁21:2 摧毁”希伯来文有“销毁,以示奉献给耶和华”之意。他们的城邑。” 3耶和华答应了他们的祈求,把迦南人交在他们手中,使他们彻底毁灭了迦南人及其城邑。从此,那地方叫何珥玛21:3 何珥玛”意思是“毁灭”。

铜蛇

4以色列人为了绕过以东,便从何珥山出发,沿通往红海的路行进。途中,民众心里烦躁, 5埋怨上帝和摩西说:“你们为什么把我们从埃及带出来,叫我们死在旷野呢?这里无粮无水,我们厌恶这难吃的东西!”

6于是,耶和华派毒蛇进入以色列人中,咬死了许多人。 7他们来找摩西,说:“我们埋怨耶和华和你,犯了罪,求你向耶和华祷告,好叫这些蛇离开我们。”摩西就为他们祷告。 8耶和华对摩西说:“你去造一条蛇挂在杆子上,凡被咬的一望这蛇,就可活命。” 9摩西就造了一条铜蛇,挂在杆子上。被蛇咬的人一望铜蛇,就保住了性命。

前往摩押

10以色列人继续前行,在阿伯安营; 11又从阿伯动身,走到摩押东边的旷野,在以耶·亚巴琳安营; 12又从那里前行,走到撒烈谷安营; 13又从那里出发,走到亚嫩河北岸的旷野安营。那里毗邻亚摩利人的边境,亚嫩河是摩押亚摩利之间的疆界。 14因此,耶和华的战记上说:“苏法哇哈伯亚嫩河谷, 15以及河谷的斜坡——靠近摩押边界并延伸到亚珥城。”

16以色列人又往前走,来到比珥21:16 比珥”意思是“井”。。耶和华曾在那里对摩西说:“把民众招聚起来,我要给他们水喝。” 17当时,以色列人唱了这首歌:

“井啊,涌出水来!

你们要歌颂这口井,

18它是首领挖的,

是民中的贵族掘的,

用令牌和权杖挖掘的。”

他们从旷野前往玛他拿19玛他拿前往拿哈列,从拿哈列前往巴末20巴末前往摩押的谷地,从那里的毗斯迦山顶可以俯视旷野。

击败亚摩利王和巴珊王

21以色列人派使者去见亚摩利西宏,说: 22“请允许我们从贵国经过,我们只走大路,不会踏入田地和葡萄园,也不会喝井里的水,直到走出贵国的土地。” 23西宏拒绝了他们的请求,并招聚军队到旷野攻击他们。两军在雅杂交锋。 24以色列人杀了西宏,占领了他的土地——从亚嫩河到雅博河,远至防守严密的亚扪人边界。 25以色列人攻占了亚摩利人的所有城邑,包括希实本及其周围的村庄,住在其中。 26希实本亚摩利西宏的都城。西宏曾与摩押的先王交战,占领了他所有的领土,远至亚嫩河。 27因此有人作诗说:

“来希实本吧!

重建西宏的城。

28希实本烈焰熊熊,

西宏的城火光冲天,

烧毁摩押亚珥

吞噬亚嫩河的高岗。

29摩押啊,你大祸临头了!

基抹神明的人啊,

你们要灭亡了!

基抹任由自己的儿子逃亡、

女儿被亚摩利西宏掳走。

30但我们击溃了亚摩利人,

希实本一直到底本都被摧毁,

挪法米底巴都沦为废墟。”

31于是,以色列人住在亚摩利境内。 32摩西派人去雅谢打探,然后出兵攻占了雅谢及其周围的村庄,赶走那里的亚摩利人。 33以色列人回师前往巴珊巴珊率全军出动,在以得来迎战以色列人。 34耶和华对摩西说:“不要怕他,因为我已把他及其众民和土地交在你手中。你要像从前对付希实本亚摩利西宏一样对付他。” 35于是,以色列人杀了及其儿子和人民,一个不留,并夺取了他的国土。