Numeri 19 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Numeri 19:1-22

Phulusa ndi Madzi Oyeretsera

1Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni: 2“Lamulo limene Yehova wapereka ndi ili: Uzani Aisraeli kuti abweretse ngʼombe yayikazi yofiira yopanda chilema chilichonse imenenso sinakhalepo pa goli. 3Muyipereke kwa Eliezara, wansembe ndipo apite nayo kunja kwa msasa. Iphedwe iye ali pomwepo. 4Ndipo Eliezara wansembe atengeko ena mwa magazi a ngʼombeyo ndi chala chake ndi kuwaza kasanu nʼkawiri ku tsogolo kwa tenti ya msonkhano. 5Wansembeyo akuona, ngʼombeyo ayiwotche chikopa chake, mnofu wake, magazi ake ndi zamʼkati zake. 6Wansembe atenge mtengo wamkungudza, hisope ndi kansalu kofiira ndipo aponye zimenezo pakati pa moto umene akuwotchera ngʼombeyo. 7Zitatha izi, wansembeyo ayenera kuchapa zovala zake ndiponso asambe ndi madzi. Iye angathe kupita ku msasa, komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 8Munthu amene amawotcha ngʼombeyo ayeneranso kuchapa zovala zake ndi kusamba ndi madzi. Iyenso adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.

9“Munthu amene ndi woyeretsedwa achotse phulusa la ngʼombeyo ndi kuliyika pa malo woyeretsedwa kunja kwa msasa. Aisraeli adzasunge phulusalo kuti azikaligwiritsa ntchito polithira mʼmadzi woyeretsera ndi wochotsera tchimo. 10Munthu wochotsa phulusa la ngʼombeyo ayeneranso kuchapa zovala zake. Iyenso adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. Ili likhale lamulo la nthawi zonse kwa Aisraeli ndi alendo okhala pakati pawo.

11“Aliyense wokhudza mtembo wa munthu wina aliyense adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri. 12Adziyeretse yekha ndi madzi pa tsiku lachitatu ndi pa tsiku lachisanu ndi chiwiri ndipo adzayeretsedwa. Koma ngati sadziyeretsa yekha pa tsiku la chitatu ndi lachisanu ndi chiwiri sadzakhala woyeretsedwa. 13Aliyense amene akhudza mtembo wa munthu nʼkulephera kudziyeretsa yekha, ndiye kuti wadetsa Nyumba ya Yehova. Munthu ameneyo achotsedwe pakati pa Aisraeli. Iye ndi wodetsedwa chifukwa sanamuwaze madzi oyeretsa; kudetsedwa kwake kukhalabe pa iyeyo.

14“Pamene munthu wamwalira mu tenti, lamulo lomwe ligwire ntchito ndi ili: Aliyense wolowa mu tentimo ndi amene anali momwemo adzakhala odetsedwa kwa masiku asanu ndi awiri, 15ndiponso chiwiya chilichonse chopanda chivundikiro chidzakhala chodetsedwa.

16“Aliyense wokhudza munthu amene waphedwera kunja ndi lupanga kapena amene wafa ndi imfa ya chilengedwe, kapena aliyense wokhudza fupa la munthu kapena manda, munthu ameneyo adzakhala wodetsedwa kwa masiku asanu ndi awiri.

17“Za munthu wodetsedwayo: ikani phulusa lochokera ku nsembe ya chiyeretso mu mtsuko ndi kuthiramo madzi abwino. 18Tsono munthu woyeretsedwa atenge hisope, amuviyike mʼmadzi ndi kuwaza tentiyo ndi zipangizo zonse, pamodzi ndi anthu anali mʼmenemo. Ayenera kuwazanso aliyense wakhudza fupa kapena, munthu wochita kuphedwa, kapena amene wafa ndi imfa ya chilengedwe kapenanso amene wakhudza manda. 19Munthu woyeretsedwa ndiye awaze munthu wodetsedwayo pa tsiku lachitatu ndi pa tsiku lachisanu ndi chiwiri, ndipo pa tsiku lachisanu ndi chiwiri amuyeretse. Munthu amene akuyeretsedwayo ayenera kuchapa zovala zake ndi kusamba ndi madzi, ndipo madzulo ake adzakhala woyeretsedwa. 20Koma ngati munthu wodetsedwayo sadziyeretsa yekha, ndiye kuti ayenera kuchotsedwa pakati pa gulu chifukwa anadetsa malo wopatulika a Yehova, popeza sanawazidwe madzi oyeretsa ndiye kuti ndi wodetsedwa. 21Ili ndi lamulo lokhazikika kwa iwo.

“Munthu amene amawaza madzi oyeretsawo ayenera kuchapa zovala zake ndipo yense wokhudza madzi oyeretserawo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 22Chilichonse chimene munthu wodetsedwayo achikhudze chidzakhala chodetsedwa ndiponso aliyense wochikhudza adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.”

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

民数记 19:1-22

红母牛的灰

1耶和华对摩西亚伦说: 2“要吩咐以色列人遵行我颁布的以下律法条例。

以色列人要牵来一头毫无残疾、从未负过轭的红母牛。 3你们要把牛交给以利亚撒祭司,然后牵到营外,当着他的面把牛宰了。 4以利亚撒祭司要用指头蘸牛血,向会幕前面弹七次。 5然后,要当着他的面焚烧红母牛,牛的皮、肉、血和粪都要烧掉。 6祭司要把香柏木、牛膝草、朱红色线扔进烧牛的火里。 7之后,祭司要洗衣沐浴,才能回营,但要等到傍晚才能洁净。 8负责烧牛的人也要洗衣、沐浴,并且要等到傍晚才能洁净。 9要由洁净的人把红母牛灰收起来,放在营外洁净的地方,用于给以色列会众制作除秽水,作除罪之用。 10收起牛灰的人也要洗净衣服,等到傍晚才能洁净。以色列人和寄居的外族人都要永远遵行这定例。

11“碰过尸体的人,七天不洁净。 12他要在第三天和第七天用除秽水自洁,才能洁净,否则就不能洁净。 13若有人碰过尸体却不自洁,他就玷污了耶和华的圣幕,要将他从以色列人中铲除,因为除秽水没有洒在他身上,污秽还留在他身上。 14若有人死在帐篷里,当时走进帐篷的或在场的人都七天不洁净。 15帐篷里没有盖的敞口器皿都不洁净。 16人若在野外碰过被杀或自然死亡之人的尸体,或碰过死人的骸骨或坟墓,就七天不洁净。 17要拿些除罪用的红母牛灰,放在器皿里,倒上清水, 18然后由洁净的人拿牛膝草蘸这水洒在帐篷及里面所有的人和器具上,也要洒在碰过骸骨、坟墓、被杀者尸体或自然死亡者尸体的人身上。 19要由洁净的人在第三天和第七天把水洒在不洁净的人身上。到第七天,接受洁净礼的人要洗衣、沐浴,等到傍晚才能洁净。 20若有人沾了污秽却没有用除秽水自洁,他就不洁净,要将他从会众中铲除,因为他玷污了耶和华的圣所。 21你们要永远遵行这定例。洒除秽水的人要洗净衣服。碰过除秽水的人要等到傍晚才能洁净。 22不洁净的人碰过的东西都不洁净,碰过这些东西的人傍晚之前都不洁净。”