Numeri 10 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Numeri 10:1-36

Malipenga Asiliva

1Yehova anawuza Mose kuti, 2“Sula malipenga awiri a siliva, ndipo uziwagwiritsa ntchito posonkhanitsa anthu pamodzi ndiponso powasamutsa mʼmisasa. 3Pamene akuliza malipenga onse awiri, anthu onse asonkhane kwa iwe pa khomo la tenti ya msonkhano. 4Akaliza limodzi lokha, atsogoleri, akulu a mafuko a Aisraeli, asonkhane kwa iwe. 5Akaliza lipenga lochenjeza, misasa yomwe ili kummawa iyambe kusamuka. 6Akaliza lipenga lochenjeza lachiwiri, misasa yakummwera iyambe kusamuka. Kuliza kwa lipenga lochenjeza kudzakhala chizindikiro choyamba ulendo. 7Pofuna kusonkhanitsa anthu, muziliza malipenga, koma mosiyana ndi mmene malipenga ochenjeza amalizidwira.

8“Ana a Aaroni, ansembe aja, ndiwo aziliza malipengawo. Zimenezi zikhale zokhazikika kwa inu ndi ku mibado yanu yonse. 9Pamene mukupita ku nkhondo mʼdziko lanu lomwe, kulimbana ndi mdani amene akukuzunzani, muziliza malipenga ochenjeza ndipo Yehova Mulungu wanu adzakukumbukirani ndi kukulanditsani mʼmanja mwa adani anu. 10Komanso pa nthawi yanu ya chisangalalo, pa maphwando anu oyikika ndi maphwando a mwezi watsopano, muziliza malipenga pa nsembe zanu zopsereza ndi nsembe zanu za chiyanjano, ndipo zidzakhala chikumbutso chanu pamaso pa Mulungu. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.”

Aisraeli Achoka ku Sinai

11Pa chaka chachiwiri, mwezi wachiwiri, tsiku la 20, mtambo unachoka pamwamba pa chihema cha umboni. 12Ndipo Aisraeli ananyamuka kuchoka mʼchipululu cha Sinai ndipo anayenda malo osiyanasiyana mpaka pamene mtambo unayima mʼchipululu cha Parani. 13Kameneka kanali koyamba kuti Aisraeli anyamuke monga momwe Yehova analamulira Mose.

14Magulu a msasa wa Yuda ndiwo anayamba kunyamuka potsata mbendera yawo. Mtsogoleri wa gulu lawo anali Naasoni mwana wa Aminadabu. 15Mtsogoleri wa gulu la fuko la Isakara anali Netanieli mwana wa Zuwara, 16Eliabu mwana wa Heloni ndiye anali mtsogoleri wa fuko la Zebuloni. 17Kenaka anagwetsa chihema, ndipo Ageresoni ndi Amerari amene ananyamula chihemacho, ananyamuka.

18Kenaka magulu a msasa wa fuko la Rubeni ananyamuka potsatira mbendera yawo. Mtsogoleri wawo anali Elizuri mwana wa Sedeuri. 19Mtsogoleri wa fuko la Simeoni anali Selumieli mwana wa Zurisadai, 20ndipo Eliyasafu mwana wa Deuweli ndiye ankatsogolera fuko la Gadi. 21Kenaka Akohati ananyamuka atanyamula zinthu zopatulika. Chihema chinkayenera kuyimikidwa iwo asanafike.

22Magulu a msasa wa Aefereimu anatsatira potsatira mbendera yawo. Elisama mwana wa Amihudi ndiye anali mtsogoleri wawo. 23Gamalieli mwana wa Pedazuri ndiye anali mtsogoleri wa fuko la Manase. 24Abidani mwana wa Gideoni ndiye anali mtsogoleri wa mtundu wa Benjamini.

25Pambuyo pa magulu onse panali magulu a msasa wa Dani, omwe ankateteza magulu onsewa ndipo ananyamuka potsatira mbendera yawo. Mtsogoleri wawo anali Ahiyezeri mwana wa Amisadai. 26Pagieli mwana wa Okirani ndiye anali mtsogoleri wa fuko la Aseri, 27ndipo mtsogoleri wa mtundu wa Nafutali anali Ahira mwana wa Enani. 28Umenewu ndiwo unali mndandanda wa kayendedwe ka magulu a Aisraeli pamene ankanyamuka ulendo wawo mʼmagulumagulu.

29Ndipo Mose anawuza Hobabu mwana wa Reueli Mmidiyani, mpongozi wa Mose kuti, “Tikunyamuka kupita ku malo amene Yehova anati, ‘Ndidzakupatsani.’ Tiye upite nafe ndipo tidzakusamalira bwino, pakuti Yehova analonjeza zinthu zabwino kwa Israeli.”

30Hobabu anayankha kuti, “Ayi, sindipita nanu, ndibwerera ku dziko la kwathu ndi kwa abale anga.”

31Ndipo Mose anati, “Pepa usatisiye popeza ukudziwa kumene tingamange misasa mʼchipululu muno ndipo udzakhala maso athu. 32Iweyo ukapita nafe, tidzagawana nawe zinthu zabwino zomwe Yehova adzatipatsa.”

33Motero ananyamuka ku Phiri la Yehova nayenda ulendo wa masiku atatu. Bokosi la Chipangano cha Yehova linkayenda patsogolo pawo pa masiku atatuwo kuti apeze malo woti apumulepo. 34Mtambo wa Yehova unkawaphimba masana pamene ankasamuka pa misasa yawo.

35Nthawi iliyonse imene Bokosi la Chipangano likunyamuka, Mose ankanena kuti,

“Dzukani, Inu Yehova!

Adani anu abalalike;

Odana nanu athawe pamaso panu.

36“Pamene likupumula, ankanena kuti,

“Bwererani, Inu Yehova,

ku chinamtindi cha Aisraeli.”