Mlaliki 7 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mlaliki 7:1-29

Nzeru

1Mbiri yabwino ndi yopambana mafuta onunkhira bwino,

ndipo tsiku lomwalira ndi lopambana tsiku lobadwa.

2Kuli bwino kupita ku nyumba yamaliro

kusiyana ndi kupita ku nyumba yamadyerero:

Pakuti imfa ndiye mathero a munthu aliyense;

anthu amoyo azichisunga chimenechi mʼmitima mwawo.

3Chisoni nʼchabwino kusiyana ndi kuseka,

pakuti nkhope yakugwa ndi yabwino chifukwa imakonza mtima.

4Mtima wa munthu wanzeru nthawi zonse umalingalira za imfa,

koma mitima ya zitsiru imalingalira za chisangalalo.

5Kuli bwino kumva kudzudzula kwa munthu wanzeru

kusiyana ndi kumvera mayamiko a zitsiru.

6Kuseka kwa zitsiru kuli ngati

kuthetheka kwa moto kunsi kwa mʼphika,

izinso ndi zopandapake.

7Kuzunza ena kumasandutsa munthu wanzeru kukhala chitsiru,

ndipo chiphuphu chimawononga mtima.

8Mathero ake a chinthu ndi abwino kupambana chiyambi chake,

ndipo kufatsa nʼkwabwino kupambana kudzikuza.

9Usamafulumire kukwiya mu mtima mwako,

pakuti mkwiyo ndi bwenzi la zitsiru.

10Usamafunse kuti, “Nʼchifukwa chiyani masiku amakedzana anali abwino kupambana masiku ano?”

pakuti si chinthu chanzeru kufunsa mafunso oterewa.

11Nzeru ngati cholowa, ndi chinthu chabwino

ndipo imapindulitsa wamoyo aliyense pansi pano.

12Nzeru ndi chitetezo,

monganso ndalama zili chitetezo,

koma phindu la chidziwitso ndi ili:

kuti nzeru zimasunga moyo wa munthu amene ali nazo nzeruzo.

13Taganizirani zimene Mulungu wazichita:

ndani angathe kuwongola chinthu

chimene Iye anachipanga chokhota?

14Pamene zinthu zili bwino, sangalala;

koma pamene zinthu sizili bwino, ganizira bwino:

Mulungu ndiye anapanga nthawi yabwinoyo,

ndiponso nthawi imene si yabwinoyo.

Choncho munthu sangathe kuzindikira

chilichonse cha mʼtsogolo mwake.

15Pa moyo wanga wopanda phinduwu ndaona zinthu ziwiri izi:

munthu wolungama akuwonongeka mʼchilungamo chake,

ndipo munthu woyipa akukhala moyo wautali mʼzoyipa zake.

16Usakhale wolungama kwambiri

kapena wanzeru kwambiri,

udziwonongerenji wekha?

17Usakhale woyipa kwambiri,

ndipo usakhale chitsiru,

uferenji nthawi yako isanakwane?

18Nʼkwabwino kuti utsate njira imodzi,

ndipo usataye njira inayo.

Munthu amene amaopa Mulungu adzapewa zinthu ziwiri zonsezi.

19Nzeru zimapereka mphamvu zambiri kwa munthu wanzeru

kupambana olamulira khumi a mu mzinda.

20Palibe munthu wolungama pa dziko lapansi

amene amachita zabwino zokhazokha ndipo sachimwa.

21Usamamvetsere mawu onse amene anthu amayankhula,

mwina udzamva wantchito wako akukutukwana,

22pakuti iwe ukudziwa mu mtima mwako

kuti nthawi zambiri iwenso unatukwanapo ena.

23Zonsezi ndinaziyesa ndi nzeru zanga ndipo ndinati,

“Ine ndatsimikiza mu mtima mwanga kuti ndikhale wanzeru,”

koma nzeruyo inanditalikira.

24Nzeru zimene zilipo,

zili kutali ndipo ndi zozama kwambiri,

ndani angathe kuzidziwa?

25Kotero ndinayikapo mtima wanga kuti ndidziwe,

ndifufuze ndi kumafunafuna nzeru ndi mmene zinthu zimakhalira

ndipo ndinafunanso kudziwa kuyipa kwa uchitsiru

ndiponso kupusa kwake kwa misala.

26Ndinapeza kanthu kowawa kupambana imfa,

mkazi amene ali ngati khoka,

amene mtima wake uli ngati khwekhwe,

ndipo manja ake ali ngati maunyolo.

Munthu amene amakondweretsa Mulungu adzathawa mkaziyo,

koma mkaziyo adzakola munthu wochimwa.

27Mlaliki akunena kuti, “Taonani, chimene ndinachipeza ndi ichi:

“Kuwonjezera chinthu china pa china kuti ndidziwe mmene zinthu zimachitikira,

28pamene ine ndinali kufufuzabe

koma osapeza kanthu,

ndinapeza munthu mmodzi wolungama pakati pa anthu 1,000,

koma pakati pawo panalibepo mkazi mmodzi wolungama.

29Chokhacho chimene ndinachipeza ndi ichi:

Mulungu analenga munthu, anamupatsa mtima wolungama,

koma anthu anatsatira njira zawozawo zambirimbiri.”

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

傳道書 7:1-29

1美好的名聲勝過珍貴的膏油,

人死之日勝過出生之時。

2探望喪家勝過參加宴席,

因為死亡是每個人的結局,

活著的人要把這事銘記在心。

3哀傷勝過歡笑,

因為哀傷磨煉人的心靈。

4智者的心思考生死大事,

愚人的心只顧作樂。

5聽智者的責備,

勝過聽愚人的頌歌。

6愚人的笑聲像鍋底下燒荊棘的噼啪聲。

這也是虛空。

7欺壓使智者變愚昧,

賄賂敗壞人心。

8事情的結局勝過事情的開端;

恆久忍耐勝過心驕氣傲。

9不要輕易發怒,

因為愚人心懷怒氣。

10不要問為什麼過去比現在好,

因為這樣問不明智。

11智慧如同產業一樣美好,

有益於得見日光的世人。

12智慧如同金錢,

是一種保障,

能保全智者的生命。

這就是知識的好處。

13你應當思想上帝的作為,

因為上帝弄彎的,

誰能使它變直呢?

14順境時要快樂,

逆境時要思想:

兩者都是上帝的安排,

好叫人不能預知將來。

15在我虛空的一生中,我見過義人行義,反而滅亡;惡人行惡,卻享長壽。 16為人不要過分正直,也不要過於聰明,何必自取毀滅呢? 17不要過分邪惡,也不要做愚人,何必時候未到就死呢? 18最好是持守這個教訓也不放鬆那個教訓,因為敬畏上帝的人必避免兩個極端。 19智慧使一個智者比城裡十個官長更有能力。 20誠然,在地上無法找到一個一生行善、從未犯罪的義人。 21你不要斤斤計較別人所說的每一句話,免得聽見你的僕人咒詛你, 22因為你心裡知道自己也曾多次咒詛別人。 23我用智慧試驗過這一切。我說:「我要做智者」,誰知智慧卻離我甚遠。 24智慧如此遙不可及、深不可測,誰能找得到呢? 25我用心去認識、探究、追尋智慧和事物的原委,並去認識邪惡帶來的愚昧和無知帶來的狂妄。 26我發現有的婦人比死亡更苦毒,她是個陷阱,心如網羅,手像鎖鏈。敬畏上帝的人避開她,罪人卻被她俘虜。 27-28傳道者說:「看啊,我事事反復探索,要查明萬事之理,卻沒有尋獲。但我發現在一千個男子中還可以找到一位正直人,在眾女子中卻未找到一位。 29我只發現一件事,上帝造的人本來正直,人卻找出各種詭計。」