Mlaliki 6 – CCL & NSP

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mlaliki 6:1-12

1Ine ndinaona choyipa china pansi pano, ndipo chimasautsa anthu kwambiri: 2Mulungu amapereka chuma, zinthu ndi ulemu kwa munthu, kotero kuti munthuyo sasowa kanthu kalikonse kamene akukalakalaka, koma Mulungu samulola kuti adyerere zinthuzo, ndipo mʼmalo mwake amadyerera ndi mlendo. Izi ndi zopandapake, ndi zoyipa kwambiri.

3Ngakhale munthu atabereka ana 100 ndi kukhala ndi moyo zaka zambiri; komatu ngakhale atakhala zaka zambiri chotani, ngati iye sangadyerere chuma chake ndi kuyikidwa mʼmanda mwaulemu, ine ndikuti mtayo umamuposa iyeyo. 4Mtayo umangopita pachabe ndipo umapita mu mdima, ndipo mu mdimamo dzina lake limayiwalika. 5Ngakhale kuti mtayowo sunaone dzuwa kapena kudziwa kanthu kalikonse, koma umapumula kuposa munthu uja, 6ngakhale munthuyo atakhala ndi moyo zaka 2,000, koma ndi kulephera kudyerera chuma chake. Kodi onsewa sapita malo amodzi?

7Ntchito yonse ya munthu imathera pakamwa pake,

komatu iye sakhutitsidwa ndi pangʼono pomwe.

8Kodi munthu wanzeru

amaposa motani chitsiru?

Kodi munthu wosauka amapindula chiyani

podziwa kukhala bwino pamaso pa anthu ena?

9Kuli bwino kumangoona zinthu ndi maso

kusiyana ndi kumangozilakalaka mu mtima.

Izinso ndi zopandapake,

nʼkungodzivuta chabe.

10Chilichonse chimene chilipo anachitchula kale dzina,

za mmene munthu alili nʼzodziwika;

sangathe kutsutsana ndi munthu

amene ali wamphamvu kupambana iyeyo.

11Mawu akachuluka

zopandapake zimachulukanso,

nanga munthu zimamupindulira chiyani?

12Pakuti ndani amene amadziwa chomwe ndi chabwino pa moyo wa munthu, pakuti moyo wake ndi wa masiku ochepa ndi opandapake, umangopitira ngati mthunzi. Ndani amene angamufotokozere zimene zidzachitika pansi pano iye atapita?

New Serbian Translation

Књига проповедникова 6:1-12

1Постоји за људе још једно велико зло које сам видео под капом небеском: 2Некоме Бог да иметак, богатство, част, па му души ништа не мањка што пожели. Али му Бог не даје да ужива, да једе од тога, већ туђинац једе. То је пролазно и тешка је болест.

3Да неко има стотину синова, да живи многе године, да је много дана његових година – чак и гроба не имао, а душа му се није наситила благостања – онда тврдим да је и мртворођенче боље од њега. 4Јер, оно је узалуд рођено, у таму је отишло и тама му име покрива. 5Није видело сунца и не зна за њега, а почива боље него онај други; 6који, све да живи и двапут по хиљаду година, не ужива у своме иметку. Најзад, не иду ли сви на исто место?

7Сав је човеков труд за његова уста,

али му опет душа није сита.

8По чему је мудром боље од безумног,

и шта има сиромашак

који уме да се влада пред људима?

9Боље је оно што очи гледају

него оно за чим душа жуди,

јер је и то пролазно

и јурење ветра.

10Оно што се збило одређено је и било,

и зна се шта је човек:

не може да се спори

са јачим од себе.

11Тамо где је много речи

бесмисао бива већи,

и каква је од тога човекова корист?

12Јер ко зна шта је добро за човека у мало дана његовог пролазног живота који му ишчезну као сена? Ко ће да каже човеку шта ће се збити након њега под капом небеском?