Miyambo 25 – CCL & CARST

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Miyambo 25:1-28

Miyambo Ina ya Solomoni

1Iyi ndi miyambo inanso ya Solomoni, imene anthu a Hezekiya mfumu ya ku Yuda analemba.

2Ulemerero wa Mulungu uli pa kubisa zinthu;

ulemerero wa mafumu uli pa kufufuza zinthuzo.

3Monga momwe kwatalikira kumwamba ndi momwe kulili kuzama kwa dziko lapansi,

ndi momwemonso alili maganizo a mfumu kusadziwika kwake.

4Chotsa zoyipa mʼsiliva

ndipo wosula adzapanga naye ziwiya.

5Chotsa munthu woyipa pamaso pa mfumu;

ndipo ufumu wake udzakhazikika mu chilungamo.

6Usamadzikuze ukakhala pamaso pa mfumu,

ndipo usamakhale pamalo pa anthu apamwamba;

7paja ndi bwino kuti mfumu ichite kukuwuza kuti, “Bwera pamwamba pano,”

kulekana ndi kuti ikuchititse manyazi chifukwa cha wina wokuposa.

Chimene wachiona ndi maso ako,

8usafulumire kupita nacho ku bwalo la milandu

nanga udzachita chiyani pa mapeto pake

ngati mnansi wako adzakuchititsa manyazi?

9Kamba mlandu ndi mnansi wako,

koma osawulula chinsinsi cha munthu wina

10kuopa kuti wina akamva mawu ako adzakuchititsa manyazi

ndipo mbiri yako yoyipa sidzatha.

11Mawu amodzi woyankhulidwa moyenera

ali ngati zokongoletsera zagolide mʼzotengera zasiliva.

12Kwa munthu womvetsa bwino, kudzudzula kwa munthu wanzeru kuli ngati ndolo zagolide

kapena chodzikongoletsera china cha golide wabwino kwambiri.

13Wamthenga wodalirika ali ngati madzi ozizira pa nthawi yokolola

kwa anthu amene amutuma;

iye amaziziritsa mtima bwana wake.

14Munthu wonyadira mphatso imene sayipereka

ali ngati mitambo ndi mphepo yopanda mvula.

15Kupirira ndiye kumagonjetsa mfumu,

ndipo kufewa mʼkamwa kutha kumafatsitsa munthu wowuma mtima.

16Ngati upeza uchi, ingodya okukwanira,

kuopa ungakoledwe nawo ndi kuyamba kusanza.

17Uzipita kamodzikamodzi ku nyumba ya mnzako

ukawirikiza kupita, udzadana naye.

18Munthu wochitira mnzake umboni wonama,

ali ngati chibonga kapena lupanga kapena muvi wakuthwa.

19Kudalira munthu wosankhulupirika pa nthawi ya mavuto,

kuli ngati dzino lobowoka kapena phazi lolumala.

20Kuyimbira nyimbo munthu wachisoni

kuli ngati kuvula zovala pa nyengo yozizira

kapena kuthira mchere pa chilonda.

21Ngati mdani wako ali ndi njala, mupatse chakudya kuti adye;

ngati ali ndi ludzu mupatse madzi kuti amwe.

22Pochita izi, udzamusenzetsa makala a moto pa mutu pake,

ndipo Yehova adzakupatsa mphotho.

23Monga momwe mphepo yampoto imabweretsera mvula,

chonchonso mjedu umadzetsa mkwiyo.

24Nʼkwabwino kukhala pa ngodya ya denga

kuposa kukhala mʼnyumba ndi mkazi wolongolola.

25Mthenga wabwino wochokera ku dziko lakutali

ali ngati madzi ozizira kwa munthu waludzu.

26Munthu wolungama amene amagonjera munthu woyipa

ali ngati kasupe wodzaza ndi matope kapena chitsime cha madzi oyipa.

27Sibwino kudya uchi wambiri,

sibwinonso kudzifunira wekha ulemu.

28Munthu amene samatha kudziretsa

ali ngati mzinda umene adani awuthyola ndi kuwusiya wopanda malinga.

Священное Писание (Восточный перевод), версия для Таджикистана

Мудрые изречения 25:1-28

Другие мудрые изречения Сулаймона

1Вот ещё мудрые изречения Сулаймона, собранные людьми Езекии, царя Иудеи25:1 Езекия правил Иудеей с 715 по 686 гг. до н. э. О его правлении см. 4 Цар. 18–20; 2 Лет. 29–32..

2Слава Всевышнего – окутывать дело тайной,

слава царя – исследовать дело.

3Как небеса высотой и земля глубиной,

так и царское сердце непостижимо.

4Удали примесь из серебра,

и у ювелира будет сырьё для сосуда;

5удали нечестивого от царя,

и его престол утвердится праведностью.

6Не заносись пред царём

и не занимай места между великими;

7лучше пусть он тебе скажет: «Сюда поднимись»,

чем унизит тебя перед знатным.

Если ты что-то видел своими глазами,

8не спеши подавать в суд.

Что ты станешь делать в конце,

если ближний твой пристыдит тебя, выиграв дело?

9Если ведёшь с ближним тяжбу,

не открывай чужой тайны,

10иначе люди услышат и пристыдят тебя,

и слава дурная от тебя не отстанет.

11Слово, сказанное уместно,

подобно золотым яблокам в оправе из серебра.

12Что золотая серьга или украшение из чистого золота,

то упрёк мудреца для внимательного уха.

13Что холод снега в жатвенный зной,

то верный посланник для того, кто его посылает:

душу хозяина он бодрит.

14Что облака и ветер без дождя –

тот, кто хвастается подарками, которых не дарил.

15Терпением можно убедить повелителя,

и кроткий язык кость переламывает.

16Нашёл мёд – ешь лишь сколько потребно,

иначе объешься и тебя стошнит.

17Так же с другом: пореже ходи к нему в дом,

иначе, устав от тебя, он тебя возненавидит.

18Что булава, меч или острая стрела –

человек, лжесвидетельствующий против ближнего.

19Что зуб гнилой или хромая нога –

надежда на вероломного в день беды.

20Как снимающий одежду в холодный день

или как уксус на рану25:20 Или: «соду».,

так и поющий печальному сердцу весёлые песни.

21Если враг твой голоден – накорми его;

если он хочет пить – напои его водой.

22Поступая так, ты устыдишь его,

и он будет сгорать со стыда25:22 Букв.: «ты соберёшь ему на голову горящие угли».,

а тебя наградит Вечный.

23Как северный ветер приносит дождь,

так язык клеветника – гневные лица.

24Лучше жить на углу крыши,

чем в доме со сварливой женой.

25Что холодная вода для измученной жаждой души –

то добрые вести из дальнего края.

26Как мутный ключ или загрязнённый родник –

праведник, уступающий нечестивым.

27Нехорошо есть слишком много мёда,

как и постоянно искать себе славы.

28Каков город, чьи стены рухнули,

таков и человек, не владеющий собой.