Miyambo 19 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Miyambo 19:1-29

1Ndi wabwino munthu wosauka amene amayenda mu ungwiro,

aposa munthu wopusa woyankhula zokhota.

2Si bwino kuti munthu akhale wopanda nzeru;

ndipo munthu woyenda mofulumira amaphonya njira.

3Uchitsiru wa munthu umamubweretsera zovuta,

mtima wake umakwiyira Yehova.

4Chuma chimachulukitsa abwenzi;

koma munthu wosauka bwenzi lake limamuthawa.

5Mboni yonama sidzalephera kulangidwa;

ndipo iye amene amanena mabodza sadzapulumuka.

6Anthu ambiri amafuna munthu wopatsa kuti awakomere mtima,

ndipo munthu amene amapereka mphatso ndi bwenzi la munthu aliyense.

7Ngati munthu wosauka abale ake omwe amadana naye,

nanji abwenzi ake tsono!

Iwo adzamuthawa kupita kutali.

Amayesa kuwatsatira mowapembedza koma iwo samapezeka konse.

8Iye amene amapeza nzeru ndiye kuti amakonda moyo wake.

Wosamalitsa kukhala wanzeru, zinthu zimamuyendera bwino.

9Mboni yonama sidzalephera kulangidwa,

ndipo iye amene amanena mabodza adzawonongeka.

10Nʼkosayenera kuti chitsiru chizikhala ndi moyo wamanyado,

nanjinso kuti kapolo azilamulira akalonga!

11Nzeru zimapangitsa munthu kukhala wosakwiya msanga;

ulemerero wake uli posalabadira kuchitiridwa zoyipa.

12Mkwiyo wa mfumu uli ngati kubangula kwa mkango,

koma kukoma mtima kwake kuli ngati mame pa udzu.

13Mwana wopusa ndiye tsoka la abambo ake

ndipo mkazi wolongolola ndi wotopetsa ngati mvula yamvumbi.

14Nyumba ndi chuma ndiye cholowa chochokera kwa makolo;

koma mkazi wanzeru ndi wochokera kwa Yehova.

15Ulesi umagonetsa tulo tofa nato

ndipo munthu wosatakataka amakhala ndi njala.

16Amene amamvera malangizo amasunga moyo wake,

koma amene sasamala malamulo a Yehova adzafa.

17Amene amakomera mtima osauka amachita ngati wakongoletsa Yehova,

ndipo Yehovayo ndiye adzamubwezere.

18Langa mwana wako, chiyembekezo chikanalipo;

ngati sutero udzawononga moyo wake.

19Munthu waukali woopsa ayenera kulandira chilango;

pakuti akamulekelera ndiye zidzayipa kuposa kale.

20Mvera uphungu ndipo landira malangizo;

pa mapeto pake udzakhala wanzeru.

21Munthu amakonzekera zambiri mu mtima mwake,

koma cholinga cha Yehova ndiye chidzachitike.

22Chimene munthu amafuna ndi chikondi chosatha;

nʼkwabwino kukhala wosauka kusiyana ndi kukhala wabodza.

23Kuopa Yehova kumabweretsa moyo;

wotereyo amakhala mu mtendere; ndiye kuti choyipa sichidzamugwera.

24Munthu waulesi amapisa dzanja lake mʼmbale;

koma sangathe kufikitsa dzanja lakelo pakamwa pake.

25Menya munthu wonyoza, ndipo anthu opanda nzeru adzachenjererapo;

dzudzula munthu wozindikira zinthu, ndipo iye adzapezapo chidziwitso.

26Mwana wochita ndewu ndi abambo ake ndi kuthamangitsa amayi ake,

ndi mwana wochititsa manyazi ndi wonyozetsa.

27Mwana wanga, ukaleka kumvera malangizo,

udzapatukana ndi mawu opatsa nzeru.

28Mboni yopanda pake imanyoza cholungama,

ndipo pakamwa pa anthu oyipa pamameza zoyipa.

29Chilango chakonzedwa kale kuti chigwere anthu oyipa,

ndipo mkwapulo wakonzedwa kale kuti ukwapule misana ya anthu opusa.