Mateyu 23 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mateyu 23:1-39

Yesu Adzudzula Aphunzitsi Amalamulo ndi Afarisi

1Pamenepo Yesu anati kwa magulu a anthu ndi ophunzira ake: 2“Aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi amakhala pa mpando wa Mose. 3Choncho muziwamvera ndi kuchita chilichonse chimene akuwuzani. Koma musachite zimene amachita, popeza sachita zimene amaphunzitsa. 4Amamanga akatundu olemera nawayika pa mapewa a anthu, koma iwo eni safuna kuwanyamula.

5“Ntchito zawo amachita ndi cholinga chakuti anthu awaone. Amadzimangirira timaphukusi tikulutikulu ta Mawu a Mulungu pa mphumi ndi pa mkono komanso amatalikitsa mphonje za mikanjo yawo. 6Amakonda malo aulemu pa maphwando ndi malo ofunika kwambiri mʼmasunagoge. 7Amakondwera ndi kupatsidwa moni mʼmisika ndi kutchulidwa kuti ‘Aphunzitsi.’

8“Koma inu simuyenera kutchulidwa ‘Aphunzitsi,’ popeza muli naye Mbuye mmodzi ndipo inu nonse ndinu abale. 9Ndipo musamatchule wina aliyense pansi pano kuti ‘Atate,’ pakuti muli ndi Atate mmodzi, ndipo ali kumwamba. 10Komanso musamatchedwenso ‘Mtsogoleri,’ pakuti muli naye Mtsogoleri mmodzi amene ndi Khristu. 11Wamkulu pakati panu adzakhala wokutumikirani. 12Pakuti aliyense amene adzikuza adzachepetsedwa, ndipo aliyense amene adzichepetsa adzakuzidwa.

Tsoka kwa Aphunzitsi Amalamulo ndi Afarisi

13“Tsoka kwa inu aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi achiphamaso! Mumatseka pa khomo la kumwamba kuti anthu asalowemo. Eni akenu simulowamo komanso simulola kuti ena amene akufuna kulowa kuti alowe. 14Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumawadyera akazi amasiye chuma chawo, kwinaku nʼkumanamizira kunena mapemphero ataliatali. Chifukwa cha zimenezi Mulungu adzakulangani koposa.

15“Tsoka kwa inu, aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi, achiphamaso! Mumayenda maulendo ambiri pa mtunda ndi pa nyanja kuti mutembenuze munthu mmodzi, ndipo akatembenuka, mumamusandutsa kukhala mwana wa gehena kawiri kuposa inu.

16“Tsoka kwa inu, atsogoleri akhungu! Mumati, ‘Ngati wina alumbira kutchula Nyumba ya Mulungu, zilibe kanthu; koma ngati wina alumbira kutchula ndalama zagolide za mʼNyumbayo, wotere ayenera kusunga lumbiro lake.’ 17Inu akhungu opusa! Chopambana nʼchiyani: ndalama zagolide, kapena Nyumba imene imayeretsa golideyo? 18Ndiponso mumati, ‘Ngati wina alumbira kutchula guwa lansembe, sizitanthauza kanthu; koma ngati wina alumbira kutchula mphatso ya paguwa lansembe, wotere ayenera kusunga lumbiro lake.’ 19Inu anthu akhungu! Chopambana nʼchiyani: mphatso, kapena guwa limene limayeretsa mphatsoyo? 20Chifukwa chake, iye amene alumbira kutchula guwa alumbira pa ilo ndi pa chilichonse chili pamenepo. 21Ndipo iye wolumbira potchula Nyumba ya Mulungu alumbira pa Nyumbayo ndi pa Iye amene amakhala mʼmenemo. 22Ndipo iye wolumbira kutchula kumwamba alumbira kutchula mpando waufumu wa Mulungu ndi pa Iye wokhalapo.

23“Tsoka kwa inu, aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi, achiphamaso! Mumapereka chakhumi cha timbewu tonunkhira ndi cha timbewu tokometsera chakudya. Koma mwasiya zofunikira kwambiri za mʼmalamulo monga chilungamo, chifundo ndi kukhulupirika. Muyenera kuchita zomalizirazi komanso osasiya zoyambazo. 24Atsogoleri akhungu inu! Mumachotsa kantchentche mu chakumwa chanu koma mumameza ngamira.

25“Tsoka kwa inu, aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi achiphamaso! Mumayeretsa kunja kwa chikho ndi mbale, koma mʼkatimo mwadzaza ndi dyera ndi kusadziretsa. 26Afarisi akhungu! Poyamba tsukani mʼkati mwa chikho ndi mbale, ndipo kunja kwake kudzakhalanso koyera.

27“Tsoka kwa inu, aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi, achiphamaso! Muli ngati ziliza pa manda zowala kunja zimene zimaoneka zokongola koma mʼkatimo mwadzaza mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zina zonse. 28Chimodzimodzinso, kunja mumaoneka kwa anthu kuti ndinu olungama koma mʼkatimo ndinu odzaza ndi chinyengo ndi zoyipa zina.

29“Tsoka kwa inu, aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi, achiphamaso! Mumamanga ziliza za aneneri ndi kukongoletsa manda a olungama. 30Ndipo mumati, ‘Ngati tikanakhala mʼmasiku a makolo athu sitikanakhetsa nawo magazi a aneneri.’ 31Potero mukutsimikiza kuti muli ana a iwo amene anapha aneneri. 32Dzazani inu muyeso wa uchimo wa makolo anu!

33“Njoka inu! Ana amamba! Mudzachithawa bwanji chilango cha gehena? 34Choncho ndi kutumizirani aneneri ndi anthu anzeru ndi aphunzitsi. Ena a iwo mudzawapha ndi kuwapachika; ena mudzawakwapula mʼmasunagoge anu ndi kuwafunafuna kuchokera mudzi wina kufikira wina. 35Ndipo magazi onse a olungama amene anakhetsedwa pansi pano, kuyambira magazi a Abele, olungama kufikira Zakariya mwana wa Barakiya, amene munamupha pakati pa Nyumba ya Mulungu ndi guwa lansembe, adzakhala pa inu. 36Zoonadi, ndikuwuzani kuti zonsezi zidzafika pa mʼbado uno.

37“Haa! Yerusalemu, Yerusalemu, iwe amene umapha aneneri ndi kugenda miyala amene atumidwa kwa iwe, kawirikawiri ndimafuna kusonkhanitsa ana ako, monga nkhuku imasonkhanitsira ana ake pansi pa mapiko ake, koma iwe sunafune. 38Taona, nyumba yako yasiyidwa ya bwinja. 39Chifukwa chake ndikuwuza kuti simudzandionanso kufikira pamene mudzati, ‘Wodala Iye amene akudza mʼdzina la Ambuye.’ ”

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

馬太福音 23:1-39

譴責律法教師和法利賽人

1隨後,耶穌對百姓和門徒說: 2「律法教師和法利賽人坐在摩西的位子上講授律法。 3你們要遵行他們的教導,但不要效法他們的行為,因為他們言行不一。 4他們捆好重擔放在別人肩上,而自己連一根指頭也不肯動!

5「他們的所作所為是為了給人看的,他們把額上佩戴的經文盒子加寬了,又將衣裳的穗邊加長了。 6他們喜歡宴席中的上座和會堂裡的首位。 7他們喜歡別人在街市上問候他們,稱呼他們為老師23·7 老師」希臘文是「拉比」,特指猶太教的老師。8但你們不要讓別人稱呼你們為老師,因為你們只有一位老師,你們彼此都是弟兄。 9不要稱呼地上的人為父親,因為你們只有一位父親,祂在天上。 10不要讓人稱你們為導師,因為你們只有一位導師——基督。 11你們當中誰最偉大,誰就要作你們的僕人。 12自高的人必遭貶抑,謙卑的人必得尊榮。

13「虛偽的律法教師和法利賽人啊,你們有禍了!因為你們當著人們的面關閉天國之門,自己不進去,也不讓別人進去。

14「虛偽的律法教師和法利賽人啊,你們有禍了!因為你們侵吞寡婦的財產,還假意做冗長的禱告。因此,你們會受到更嚴厲的刑罰。23·14 有些古卷無:「虛偽的律法教師和法利賽人啊,你們有禍了!因為你們侵吞寡婦的財產,還假意做冗長的禱告。因此,你們會受到更嚴厲的刑罰。」

15「虛偽的律法教師和法利賽人啊,你們有禍了!因為你們走遍海洋和陸地去引人入教,等人入了教,卻使他淪為地獄之子,比你們還壞兩倍。

16「瞎眼的嚮導啊,你們有禍了!你們說,『指著聖殿發誓,不算數;但是指著聖殿裡的金子發誓,就要遵守誓言。』 17無知的瞎子啊!金子重要呢?還是使金子神聖的聖殿重要呢? 18你們又說,『指著祭壇發誓不算數,但是指著壇上的供物發誓,就要遵守誓言。』 19瞎眼的人啊!供物重要呢?還是使供物神聖的祭壇重要呢? 20其實指著祭壇發誓,就是指著祭壇和壇上的一切東西發誓。 21指著聖殿發誓,就是指著聖殿和住在裡面的上帝發誓。 22指著天發誓,就是指著上帝的寶座和坐在寶座上的那位發誓。

23「虛偽的律法教師和法利賽人啊,你們有禍了!你們把薄荷、茴香、芹菜獻上十分之一,卻忽略了律法中更重要的事——公正、憐憫、信實。後者是你們本該做的,前者也不可忽略。 24瞎眼的嚮導啊!你們濾出蚊蟲,卻吞下駱駝。

25「虛偽的律法教師和法利賽人啊,你們有禍了!你們洗淨杯盤的外面,裡頭卻盛滿了貪婪和放縱。 26瞎眼的法利賽人啊!要先洗淨杯盤的裡面,好讓外面也乾淨。23·26 意思是:「裡面的思想先乾淨了,外在的言行才會真正乾淨。」

27「虛偽的律法教師和法利賽人啊,你們有禍了!你們好像粉飾的墳墓,外表好看,裡面卻裝滿了死人的骨頭和各樣污穢之物。 28你們虛有公義的外表,內心卻充滿了各種的虛偽和罪惡。

29「虛偽的律法教師和法利賽人啊,你們有禍了!你們為先知建墓,為義人修碑,並且說, 30『如果我們活在我們祖先的時代,絕不會和他們一起去殺害先知。』 31這樣,你們自己證明自己是殺害先知之人的後代。 32去填滿你們祖先的罪惡吧! 33你們這些蛇,這些毒蛇的後代啊,你們怎能逃脫地獄的刑罰呢?

34「看啊,我派先知、智者和律法教師到你們當中,有的會遭到你們的殺害,被你們釘在十字架上;有的會在會堂裡被你們鞭打,被你們從這城追到那城。 35因此,所有義人在地上所流的血,就是從義人亞伯的血,直到你們在聖所和祭壇之間所殺的巴拉加的兒子撒加利亞的血,都要歸到你們身上。 36我實在告訴你們,這一切的罪責都要歸到這個世代。

為耶路撒冷哀歎

37耶路撒冷啊!耶路撒冷啊!你常殺害先知,又用石頭打死派到你那裡的使者。我多次想要招聚你的兒女,像母雞將小雞聚集在翅膀底下,可是你們卻不肯。 38看啊!你們的家園將一片荒涼。 39我告訴你們,從現在起,直到你們說『奉主名來的當受稱頌』那天之前,你們再也見不到我了。」