Mateyu 2 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mateyu 2:1-23

Anzeru a Kummawa

1Atabadwa Yesu mʼBetelehemu wa ku Yudeya, mʼnthawi ya mfumu Herode, Anzeru a kummawa anabwera ku Yerusalemu 2nafunsa kuti, “Ali kuti amene wabadwa kukhala mfumu ya Ayuda? Chifukwa tinaona nyenyezi yake kummawa ndipo tabwera kudzamupembedza.”

3Mfumu Herode atamva zimenezi, anavutika mu mtima kwambiri pamodzi ndi anthu onse a mu Yerusalemu. 4Ndipo anayitanitsa anthu onse, akulu ansembe ndi aphunzitsi amalamulo nawafunsa kuti, “Kodi Khristu adzabadwira kuti?” 5Ndipo anamuyankha kuti, “Ku Betelehemu wa ku Yudeya chifukwa izi ndi zimene mneneri analemba kuti,

6“ ‘Koma iwe Betelehemu, chigawo cha Yudeya,

sindiwe wamngʼonongʼono mwa olamulira a Yudeya;

pakuti otsogolera adzachokera mwa iwe,

amene adzaweta anthu anga Aisraeli.’ ”

7Pomwepo Herode anawayitanira mseri Anzeruwo nawafunsitsa nthawi yeniyeni yomwe nyenyeziyo inaoneka. 8Ndipo anawatumiza ku Betelehemu nawawuza kuti, “Pitani mukafufuze za mwanayo mosamalitsa. Ndipo mukamupeza mudzandiwuze kuti inenso ndikamupembedze.”

9Atamva mawu a mfumu, ananyamuka ulendo wawo, ndipo taonani nyenyezi anayiona kummawa ija, inawatsogolera mpaka inayima pamwamba pa nyumba yomwe munali mwanayo. 10Pamene iwo anaona nyenyeziyo, anasangalala kwambiri. 11Pofika ku nyumbayo, anaona mwanayo pamodzi ndi amayi ake Mariya, ndipo anagwada namulambira Iye. Pomwepo anamasula chuma chawo ndi kupereka mphatso zawo za ndalama zagolide, lubani ndi mure. 12Ndipo atachenjezedwa mʼmaloto kuti asapitenso kwa Herode, anabwerera ku dziko la kwawo podzera njira ina.

Athawira ku Igupto

13Atachoka, taonani mngelo wa Ambuye anaonekera kwa Yosefe mʼmaloto nati, “Tadzuka, tenga mwanayo pamodzi ndi amayi ake ndipo muthawire ku Igupto. Mukakhale kumeneko mpaka nditakuwuza pakuti Herode adzafunafuna mwanayo kuti amuphe.” 14Atadzuka, Yosefe anatenga mwanayo ndi amayi ake usiku omwewo napita ku Igupto, 15nakhala kumeneko mpaka Herode atamwalira. Ndipo zinakwaniritsidwa zomwe ananena Ambuye mwa mneneri kuti, “Ndinayitana mwana wanga kuti atuluke mu Igupto.”

Kuphedwa kwa Ana mʼBetelehemu

16Herode atazindikira kuti Anzeruwo anamupusitsa, anakwiya kwambiri. Ndipo anatumiza anthu kukapha ana onse aamuna a mʼBetelehemu ndi midzi yozungulira amene anali a zaka ziwiri kapena zocheperapo, molingana ndi nthawi imene Anzeruwo anamuwuza. 17Pamenepo, zimene ananena mneneri Yeremiya zinakwaniritsidwa:

18“Kulira kukumveka ku Rama,

kubuma ndi kulira kwakukulu,

Rakele akulirira ana ake;

sakutonthozeka,

chifukwa ana akewo palibe.”

Abwerera ku Nazareti

19Atamwalira Herode, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa Yosefe mʼmaloto ku Igupto 20nanena kuti, “Nyamuka, tenga mwanayo ndi amayi ake ndipo mupite ku dziko la Israeli, popeza amene anafuna moyo wa mwanayo anamwalira.”

21Tsono Yosefe atadzuka anatenga mwanayo ndi amayi ake kupita ku dziko la Israeli. 22Koma atamva kuti Arikelao akulamulira mu Yudeya mʼmalo mwa abambo ake, Herode, anaopa kupitako. Atachenjezedwa mʼmaloto, anapita ku Galileya, 23ndipo anakakhazikika mu mzinda wa Nazareti. Pamenepo zinakwaniritsidwa zonenedwa ndi aneneri kuti, “Adzatchedwa Mnazareti.”

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

馬太福音 2:1-23

智者來朝拜

1希律王執政期間,耶穌降生在猶太伯利恆城。

當時有幾位智者2·1 智者」或譯「占星家」下同7節和16節。從東方來到耶路撒冷2問道:「那生來做猶太人之王的在哪裡呢?我們在東方看見祂的星,特來朝拜祂。」

3希律王聽後,心裡不安,全城的人都感到不安。 4希律王就召來祭司長和律法教師,問他們:「基督在哪裡降生呢?」

5他們回答說:「在猶太伯利恆,因為先知這樣記載,

6猶大地區的伯利恆啊!

你在猶大各城中並不是最小的,

因為有一位君王要從你那裡出來,

牧養我的以色列子民。』」

7於是,希律暗中召見那幾位智者,仔細查問那星出現的準確時間, 8然後派他們去伯利恆,並吩咐道:「你們去仔細尋訪那個小孩,找到了,就回來報信,我也好去朝拜祂。」

9他們聽了王的吩咐,就去了。忽然,那顆曾在東方出現的星又出現在他們前面,引領他們來到小孩耶穌所在的地方,便停下來。 10他們看見那顆星,喜出望外。

11他們進了屋子,看見孩子和祂母親瑪麗亞,就俯伏在地上拜祂,並打開盛寶物的盒子獻上黃金、乳香和沒藥作禮物。 12他們在夢中得到指示不可回希律那裡,便改道返回了家鄉。

逃往埃及

13他們離開之後,主的天使在夢中向約瑟顯現,說:「起來,帶著小孩子和祂母親逃往埃及,住在那裡等候我的通知,因為希律要尋找這孩子,殺害祂。」 14於是,約瑟起來帶著孩子和祂母親連夜逃往埃及15並在那裡一直住到希律死了。這就應驗了主藉著先知所說的話:「我把兒子從埃及召出來。」

16希律見自己被智者愚弄,大為惱怒,便照著智者所說的時間推算,下令把伯利恆附近兩歲以下的男孩殺光。 17這正應驗了耶利米先知的話:

18「在拉瑪有痛哭哀號的聲音,

拉結在為兒女哀慟,

不肯接受安慰,

因為他們都死了!」

定居拿撒勒

19希律死後,主的天使在夢中向在埃及約瑟顯現,說: 20「起來,帶著孩子和祂母親回以色列去吧!因為要殺害孩子的人已經死了。」 21約瑟就起來,帶著孩子和祂母親返回以色列

22約瑟聽聞亞基勞繼承父親希律的王位統治猶太,就不敢回猶太。這時,他在夢中得到主的指示,便前往加利利地區, 23定居在拿撒勒鎮。這應驗了先知的話:「祂將被稱為拿撒勒人。」