Masalimo 90 – CCL & NIV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 90:1-17

BUKU LACHINAYI

Masalimo 90–106

Salimo 90

Pemphero la Mose munthu wa Mulungu.

1Ambuye, mwakhala muli malo athu okhalamo

pa mibado yonse.

2Mapiri asanabadwe,

musanalenge nʼkomwe dziko lapansi ndi dziko lonse,

kuyambira muyaya mpaka muyaya Inu ndinu Mulungu.

3Inu mumabwezera anthu ku fumbi,

mumati, “Bwerera ku fumbi iwe mwana wa munthu.”

4Pakuti zaka 1,000 pamaso panu

zili ngati tsiku limene lapita

kapena ngati kamphindi ka usiku.

5Inu mumasesa anthu mʼtulo ta imfa,

iwo ali ngati udzu watsopano wa mmawa,

6ngakhale kuti mmawa umaphuka watsopano,

pofika madzulo wauma ndi kufota.

7Ife tathedwa ndi mkwiyo wanu;

ndipo taopsezedwa ndi kuyipidwa kwanu.

8Mwayika mphulupulu zathu pamaso panu,

machimo athu obisika poonekera pamaso panu.

9Masiku athu onse amatha ali pansi pa ukali wanu;

timatsiriza zaka zathu ndi kubuwula.

10Kuchuluka kwa masiku athu ndi 70,

kapena 80 ngati tili ndi mphamvu;

komabe zaka zonsezi ndi za mavuto ndi nkhawa,

zimatha mofulumira ndipo ife timawulukira kutali.

11Kodi ndani amadziwa mphamvu ya mkwiyo wanu?

Pakuti ukali wanu ndi waukulu ngati ulemu umene uyenera Inu.

12Tiphunzitseni kuwerenga masiku athu molondola,

kuti tikhale ndi mtima wanzeru.

13Lezani mtima Inu Yehova! Kodi mudzatikwiyira mpaka liti?

Achitireni chifundo atumiki anu.

14Mutikhutitse mmawa ndi chikondi chanu chosatha,

kuti tiyimbe ndi chimwemwe ndi kukhala okondwa masiku athu onse.

15Tisangalatseni masiku ambiri monga masiku amene mwatisautsa,

kwa zaka zambiri monga momwe tinaonera mavuto.

16Ntchito zanu zionetsedwe kwa atumiki anu,

kukongola kwanu kwa ana awo.

17Kukoma mtima kwa Ambuye Mulungu wathu kukhale pa ife;

tikhazikitsireni ntchito ya manja athu;

inde, khazikitsani ntchito ya manja athu.

New International Version

Psalms 90:1-17

BOOK IV

Psalms 90–106

Psalm 90

A prayer of Moses the man of God.

1Lord, you have been our dwelling place

throughout all generations.

2Before the mountains were born

or you brought forth the whole world,

from everlasting to everlasting you are God.

3You turn people back to dust,

saying, “Return to dust, you mortals.”

4A thousand years in your sight

are like a day that has just gone by,

or like a watch in the night.

5Yet you sweep people away in the sleep of death—

they are like the new grass of the morning:

6In the morning it springs up new,

but by evening it is dry and withered.

7We are consumed by your anger

and terrified by your indignation.

8You have set our iniquities before you,

our secret sins in the light of your presence.

9All our days pass away under your wrath;

we finish our years with a moan.

10Our days may come to seventy years,

or eighty, if our strength endures;

yet the best of them are but trouble and sorrow,

for they quickly pass, and we fly away.

11If only we knew the power of your anger!

Your wrath is as great as the fear that is your due.

12Teach us to number our days,

that we may gain a heart of wisdom.

13Relent, Lord! How long will it be?

Have compassion on your servants.

14Satisfy us in the morning with your unfailing love,

that we may sing for joy and be glad all our days.

15Make us glad for as many days as you have afflicted us,

for as many years as we have seen trouble.

16May your deeds be shown to your servants,

your splendor to their children.

17May the favor90:17 Or beauty of the Lord our God rest on us;

establish the work of our hands for us—

yes, establish the work of our hands.