Masalimo 9 – CCL & BPH

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 9:1-20

Salimo 9

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Monga mwa mayimbidwe a nyimbo ya “Imfa ya Mwana.” Salimo la Davide.

1Ine ndidzakutamandani, Inu Yehova, ndi mtima wanga wonse;

ndidzafotokoza za zodabwitsa zanu zonse.

2Ndidzakondwa ndi kusangalala mwa inu;

Ndidzayimba nyimbo zamatamando pa dzina lanu, Inu Wammwambamwamba.

3Adani anga amathawa,

iwo amapunthwa ndi kuwonongedwa pamaso panu.

4Pakuti Inu mwatsimikiza za kulungama kwanga ndi mlandu wanga;

Inu mwakhala pa mpando wanu waufumu, kuweruza mwachilungamo.

5Mwadzudzula mitundu ya anthu ndipo mwawononga anthu oyipa;

Inu mwafafaniza dzina lawo kwamuyaya.

6Chiwonongeko chosatha chagwera adani,

mwafafaniza mizinda yawo;

ngakhale chikumbutso chawo chawonongedwa.

7Yehova akulamulira kwamuyaya;

wakhazikitsa mpando wake waufumu woweruzira.

8Iye adzaweruza dziko mwachilungamo;

adzalamulira mitundu ya anthu mosakondera.

9Yehova ndiye kothawirako kwa opsinjika mtima,

linga pa nthawi ya mavuto.

10Iwo amene amadziwa dzina lanu adzadalira Inu,

pakuti Inu Yehova, simunawatayepo amene amafunafuna inu.

11Imbani nyimbo zamatamando kwa Yehova, ali pa mpando waufumu mu Ziyoni;

lengezani pakati pa mitundu ya anthu zimene wachita.

12Pakuti Iye amene amabwezera chilango akupha anzawo wakumbukira;

Iye salekerera kulira kwa ozunzika.

13Inu Yehova, onani momwe adani anga akundizunzira!

Chitireni chifundo ndipo ndichotseni pa zipata za imfa,

14kuti ndilengeze za matamando anu

pa zipata za ana aakazi a Ziyoni,

kuti pamenepo ndikondwere ndi chipulumutso chanu.

15Mitundu ya anthu yagwa mʼdzenje limene yakumba;

mapazi awo akodwa mu ukonde umene anawubisa.

16Yehova amadziwika ndi chilungamo chake;

oyipa akodwa ndi ntchito za manja awo.

Higayoni. Sela

17Oyipa amabwerera ku manda,

mitundu yonse imene imayiwala Mulungu.

18Koma osowa sadzayiwalika nthawi zonse,

kapena chiyembekezo cha ozunzika kutayika nthawi zonse.

19Dzukani Inu Yehova, musalole munthu kuti apambane;

mitundu yonse iweruzidwe pamaso panu.

20Akantheni ndi mantha aakulu, Inu Yehova;

mitundu idziwe kuti iwo ndi anthu wamba.

Sela

Bibelen på hverdagsdansk

Salmernes Bog 9:1-21

Herren dømmer de onde og hjælper de undertrykte

1Til korlederen: Synges til melodien „En søns død.” En sang af David.

2Jeg vil prise dig, Herre, af hele mit hjerte,

fortælle om dine undere dag efter dag.

3Jeg fryder mig over dig og synger lovsange til dig,

for du er den almægtige Gud.

4Mine fjender vendte om og flygtede,

du jog dem på flugt og fældede dem.

5Du skaffede mig oprejsning

og afsagde en retfærdig dom.

6Du gik i rette med folkeslagene,

du udryddede de onde mennesker,

så deres navne er glemt for altid.

7Mine fjender blev fuldstændig knust,

deres byer blev lagt i ruiner,

man husker dem ikke mere.

8Herren regerer i evighed,

han sidder som dommer på sin trone.

9Han er fair, når han dømmer folkene,

han regerer verden med retfærdighed.

10De undertrykte søger tilflugt hos Herren,

han hjælper dem i modgang og trængsel.

11De, som kender dig, Herre, stoler på dig,

du skuffer ikke dem, der søger din hjælp.

12Syng af fryd for Herren, som troner på Zion,

lad verden høre om hans store undere.

13Han husker og hævner uret og drab,

han glemmer ikke de svages råb.

14Vær mig nådig, Herre,

for mine fjender er ude efter mig.

Herre, riv mig ud af dødens gab.

15Så vil jeg prise dig på Jerusalems torve,

og fryde mig over, at du frelste mig.

16Fjenderne ender i deres egen faldgrube,

de bliver fanget i deres egne fælder.

17Herren er kendt for sin retfærdighed,

de onde indfanges af deres egen ondskab.

18De ugudelige ender i den evige død,

det gælder alle, som gør oprør mod Gud.

19Men de ydmyge bliver ikke ladt i stikken,

de undertryktes håb bliver ikke gjort til skamme.

20Herre, lad ikke de onde sejre,

men udmål den straf, de fortjener.

21Lad dem frygte og bæve,

så de indser, at de kun er mennesker.