Masalimo 44 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 44:1-26

Salimo 44

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya ana a Kora.

1Ife tamva ndi makutu athu, Inu Mulungu;

makolo athu atiwuza

zimene munachita mʼmasiku awo,

masiku akalekalewo.

2Ndi dzanja lanu munathamangitsa mitundu ya anthu ena

ndi kudzala makolo athu;

Inu munakantha mitundu ya anthu,

koma makolo athuwo Inu munawapatsa ufulu.

3Sanalande dziko ndi lupanga lawo,

si mkono wawo umene unawabweretsera chigonjetso,

koma ndi dzanja lanu lamanja, mkono wanu ndi kuwala kwa nkhope yanu,

pakuti munawakonda.

4Inu ndinu Mfumu yanga ndi Mulungu wanga

amene mumalamulira chigonjetso cha Yakobo.

5Kudzera kwa inu ife timabweza adani athu;

kudzera mʼdzina lanu timapondereza otiwukirawo.

6Sindidalira uta wanga,

lupanga langa silindibweretsera chigonjetso;

7koma Inu mumatigonjetsera adani athu,

mumachititsa manyazi amene amadana nafe.

8Timanyadira mwa Mulungu wathu tsiku lonse,

ndipo tidzatamanda dzina lanu kwamuyaya.

9Koma tsopano mwatikana ndi kutichepetsa;

Inu simupitanso ndi ankhondo athu.

10Munachititsa ife kubwerera mʼmbuyo pamaso pa mdani

ndipo amene amadana nafe atilanda katundu.

11Inu munatipereka kuti tiwonongedwe monga nkhosa

ndipo mwatibalalitsa pakati pa anthu a mitundu ina.

12Inu munagulitsa anthu anu pa mtengo wotsika,

osapindulapo kanthu pa malondawo.

13Mwachititsa kuti tikhale chochititsa manyazi kwa anthu a mitundu ina,

chonyozeka ndi chothetsa nzeru kwa iwo amene atizungulira.

14Mwachititsa kuti tikhale onyozeka pakati pa anthu a mitundu ina;

anthu amapukusa mitu yawo akationa.

15Manyazi anga ali pamaso panga tsiku lonse

ndipo nkhope yanga yaphimbidwa ndi manyazi

16chifukwa cha mawu otonza a iwo amene amandinyoza ndi kundichita chipongwe,

chifukwa cha mdani amene watsimikiza kubwezera.

17Zonsezi zinatichitikira

ngakhale kuti ifeyo sitinayiwale Inu

kapena kuonetsa kusakhulupirika pa pangano lanu.

18Mitima yathu sinabwerere mʼmbuyo;

mapazi athu sanatayike pa njira yanu.

19Koma Inu mwatiphwanya ndi kuchititsa kuti tikhale ozunzidwa ndi ankhandwe

ndipo mwatiphimba ndi mdima waukulu.

20Tikanayiwala dzina la Mulungu wathu

kapena kutambasulira manja athu kwa mulungu wachilendo,

21kodi Mulungu wathu sakanazidziwa zimenezi,

pakuti Iye amadziwa zinsinsi zamumtima?

22Komabe chifukwa cha Inu timakumana ndi imfa tsiku lonse,

tili ngati nkhosa zoyenera kuti ziphedwe.

23Dzukani Ambuye! Nʼchifukwa chiyani mukugona!

Dziwutseni nokha! Musatikane kwamuyaya.

24Nʼchifukwa chiyani mukubisa nkhope yanu,

ndi kuyiwala mavuto athu ndi kuponderezedwa kwathu?

25Tatsitsidwa pansi mpaka pa fumbi;

matupi athu amatirira pa dothi.

26Imirirani ndi kutithandiza,

tiwomboleni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

詩篇 44:1-26

第 44 篇

祈求上帝保護

可拉後裔作的訓誨詩,交給樂長。

1上帝啊,

我們親耳聽過祖先講述你在古時,

在我們祖先時代的作為。

2你親手趕出外族,

把我們的祖先安置在那裡;

你擊潰列邦,

使我們的祖先興旺發達。

3他們不是靠自己的刀劍征服那裡,

不是靠自己的臂膀得勝,

而是靠你的權能、力量和恩惠,

因為你愛他們。

4你是我的君王,我的上帝;

你讓雅各得勝。

5我們靠你擊退敵人,

靠你的名踐踏仇敵。

6我不倚靠我的弓,

我的劍不能使我得勝。

7只有你使我們戰勝敵人,

使我們的仇敵蒙羞。

8上帝啊,我們終日以你為榮,

我們永遠讚美你。(細拉)

9現在你卻丟棄我們,

讓我們受辱,

不再幫我們的軍隊作戰。

10你使我們在仇敵面前敗退,

遭敵人擄掠。

11你使我們如被宰殺的羊,

將我們分散在列國。

12你把我們廉價賣掉,

視我們一文不值。

13你使我們遭四鄰辱罵,

被周圍人譏諷、嘲笑。

14你使我們成為列國的笑柄,

人們對我們連連搖頭。

15我終日受辱,滿面羞愧,

16因為咒罵和譭謗我的人譏笑我,仇敵報復我。

17雖然這一切臨到我們身上,

我們卻沒有忘記你,

也沒有違背你的約。

18我們對你沒有異心,

也沒有偏離你的道路。

19你在豺狼出沒的地方壓碎我們,

使死亡的陰影籠罩我們。

20倘若我們忘記我們的上帝,

或舉手向外邦的神明禱告,

21上帝怎會不知道呢?

祂洞悉人心中的秘密。

22為了你,我們終日出生入死,

被視為待宰的羊。

23主啊,求你醒來,

你為何沉睡?

求你起來,不要永遠丟棄我們。

24你為何掩面不理我們,

不理會我們所受的苦難和壓迫?

25我們仆倒在地,橫臥在塵土中。

26求你起來幫助我們,

施慈愛救贖我們。