Masalimo 42 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 42:1-11

BUKU LACHIWIRI

Masalimo 42–72

Salimo 42

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya ana a Kora.

1Monga mbawala ipuma wefuwefu kufunafuna mitsinje yamadzi,

kotero moyo wanga upuma wefuwefu kufunafuna Inu Mulungu.

2Moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Mulungu, lofuna Mulungu wamoyo.

Kodi ndipite liti kukakumana ndi Mulungu?

3Misozi yanga yakhala chakudya changa

usana ndi usiku,

pamene anthu akunena kwa ine tsiku lonse kuti,

“Mulungu wako ali kuti?”

4Zinthu izi ndimazikumbukira

pamene ndikukhuthula moyo wanga:

momwe ndinkapitira ndi gulu lalikulu,

kutsogolera mayendedwe a ku Nyumba ya Mulungu

ndi mfuwu yachimwemwe ndi mayamiko

pakati pa anthu a pa chikondwerero.

5Nʼchifukwa chiyani uli ndi chisoni, iwe moyo wanga?

Nʼchifukwa chiyani wakhumudwa iwe mʼkati mwanga?

Yembekezera Mulungu,

pakuti ndidzamulambirabe,

Mpulumutsi wanga ndi 6Mulungu wanga.

Moyo wanga uli ndi chisoni mʼkati mwanga

kotero ndidzakumbukira Inu

kuchokera ku dziko la Yorodani,

ku mitunda ya Herimoni kuchokera ku phiri la Mizara.

7Madzi akuya akuyitana madzi akuya

mu mkokomo wa mathithi anu;

mafunde anu onse obwera mwamphamvu

andimiza.

8Koma usana Yehova amalamulira chikondi chake,

nthawi ya usiku nyimbo yake ili nane;

pemphero kwa Mulungu wa moyo wanga.

9Ine ndikuti kwa Mulungu Thanthwe langa,

“Nʼchifukwa chiyani mwandiyiwala?

Nʼchifukwa chiyani ndiyenera kuyenda ndikulira,

woponderezedwa ndi mdani?”

10Mafupa anga ali ndi ululu wakufa nawo

pamene adani anga akundinyoza,

tsiku lonse akunena kuti,

“Mulungu wako ali kuti?”

11Bwanji ukumva chisoni,

iwe mtima wanga?

Chifukwa chiyani ukuvutika chonchi mʼkati mwanga?

Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamutamandanso,

Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

詩篇 42:1-11

卷二:詩篇42—72

第 42 篇

流落異鄉者的禱告

可拉後裔作的訓誨詩,交給樂長。

1上帝啊,我的心切慕你,

像鹿切慕溪水。

2我心裡渴慕上帝,

渴慕永活的上帝,

我何時才能去朝拜祂呢?

3我不吃不喝,晝夜以淚洗面,

人們整天譏笑我:

「你的上帝在哪裡?」

4從前我帶領眾人浩浩蕩蕩去上帝的殿,

在歡呼、感恩聲中一起過節。

我回想這些事,

心中無限憂傷。

5我的心啊!

你為何沮喪?為何煩躁?

要仰望上帝,

因為我還要讚美祂——我的救主,我的上帝。

6我的上帝啊,我心中沮喪,

便在約旦河、黑門山和米薩山想起你。

7你的瀑布發出巨響,

迴盪在深淵之間,

你的洪濤巨浪淹沒我。

8白天耶和華將祂的慈愛澆灌我;

夜間我歌頌祂,

向賜我生命的上帝禱告。

9我對上帝——我的磐石說:

「你為何忘記我?

為何要我受仇敵的攻擊,使我哀傷不已呢?」

10仇敵的辱罵刺骨鑽心。

他們整天對我說:

「你的上帝在哪裡?」

11我的心啊!

你為何沮喪?為何煩躁?

要仰望上帝,

因為我還要讚美祂——我的救主,我的上帝。