Masalimo 4 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 4:1-8

Salimo 4

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe wa zida za zingwe. Salimo la Davide.

1Ndiyankheni pamene ndiyitana Inu,

Inu Mulungu wa chilungamo changa.

Pumulitseni ku zowawa zanga;

chitireni chifundo ndi kumva pemphero langa.

2Anthu inu, mpaka liti mudzakhala mukusandutsa ulemerero wanga kukhala manyazi?

Mpaka liti mudzakonda zachabe ndi kufuna milungu yabodza?

Sela.

3Dziwani kuti Yehova wadziyikira padera anthu okhulupirika;

Yehova adzamva pamene ndidzamuyitana.

4Kwiyani koma musachimwe;

pamene muli pa mabedi anu,

santhulani mitima yanu ndi kukhala chete.

Sela

5Perekani nsembe zolungama

ndipo dalirani Yehova.

6Ambiri akufunsa kuti, “Ndani angationetse chabwino chilichonse?”

Kuwunika kwa nkhope yanu kutiwalire, Inu Yehova.

7Inu mwadzaza mtima wanga ndi chimwemwe chachikulu

kuposa kuchuluka kwa tirigu wawo ndi vinyo watsopano.

8Ine ndidzagona ndi kupeza tulo mwamtendere,

pakuti Inu nokha, Inu Yehova,

mumandisamalira bwino.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

詩篇 4:1-8

第 4 篇

求助的晚禱

大衛的詩,交給樂長,弦樂器伴奏。

1稱我為義人的上帝啊!

我呼求的時候,求你回答。

你曾救我脫離困境,

現在求你憐憫我,

垂聽我的禱告。

2世人啊!你們把我的榮耀變為羞辱要到何時呢?

你們追求虛謊之事要到何時呢?(細拉)

3要知道,耶和華已經把敬虔人分別出來,使之聖潔,歸祂自己。

祂必垂聽我的祈求。

4不要因生氣而犯罪;

躺在床上的時候要默然思想。(細拉)

5要獻上當獻的祭物,

信靠耶和華。

6許多人說:「誰會善待我們呢?」

耶和華啊,

求你的聖容光照我們。

7你使我比那收穫五穀新酒的人更喜樂。

8只有你耶和華使我安然居住,

我必高枕無憂。