Masalimo 144 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 144:1-15

Salimo 144

Salimo la Davide.

1Atamandike Yehova Thanthwe langa,

amene amaphunzitsa manja anga kuchita nkhondo;

zala zanga kumenya nkhondo.

2Iye ndiye Mulungu wanga wachikondi ndi malo anga otetezedwa,

linga langa ndi mpulumutsi wanga,

chishango changa mmene ine ndimathawiramo,

amene amagonjetsa mitundu ya anthu pansi panga.

3Inu Yehova, munthu nʼchiyani kuti mumamusamalira,

mwana wa munthu kuti muzimuganizira?

4Munthu ali ngati mpweya;

masiku ake ali ngati mthunzi wosakhalitsa.

5Ngʼambani mayiko akumwamba, Inu Yehova, ndipo tsikani pansi;

khudzani mapiri kuti atulutse utsi.

6Tumizani zingʼaningʼani ndi kubalalitsa adani;

ponyani mivi yanu ndi kuwathamangitsa.

7Tambasulani dzanja lanu kuchokera kumwamba;

landitseni ndi kundipulumutsa,

ku madzi amphamvu,

mʼmanja mwa anthu achilendo,

8amene pakamwa pawo ndi podzala ndi mabodza,

amene dzanja lawo lamanja ndi lachinyengo.

9Ndidzakuyimbirani nyimbo yatsopano Inu Mulungu;

ndidzakuyimbirani nyimbo pa zeze wa nsambo khumi,

10kwa Iye amene amapambanitsa mafumu,

amene amapulumutsa Davide mtumiki wake ku lupanga loopsa.

11Landitseni ndi kundipulumutsa,

mʼmanja mwa anthu achilendo,

amene pakamwa pawo ndi podzaza ndi mabodza,

amene dzanja lawo lamanja ndi lachinyengo.

12Ndipo ana aamuna pa chinyamata chawo

adzakhala ngati mbewu yosamalidwa bwino,

ana athu aakazi adzakhala ngati zipilala

zosemedwa bwino, zokongoletsera nyumba yaufumu.

13Nkhokwe zathu zidzakhala zodzaza

ndi zokolola za mtundu uliwonse.

Nkhosa zathu zidzaswana miyandamiyanda

pa mabusa athu.

14Ngʼombe zathu zidzanyamula katundu wolemera.

Sipadzakhala mingʼalu pa makoma,

sipadzakhalanso kupita ku ukapolo,

mʼmisewu mwathu simudzakhala kulira chifukwa cha mavuto.

15Odala anthu amene adzalandira madalitso awa;

odala anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

詩篇 144:1-15

第 144 篇

祈求拯救與豐裕

大衛的詩。

1耶和華——我的磐石當受稱頌,

祂使我能爭善戰。

2祂是我慈愛的上帝,

我的堡壘,我的避難所,

我的拯救者,我的盾牌,

我投靠祂。

祂使列國臣服於我。

3耶和華啊,

人算什麼,你竟顧念他?

世人算什麼,你竟眷顧他?

4因為人不過像一口氣,

他的年日不過像影子轉眼消逝。

5耶和華啊,

求你打開天門,親自降臨;

求你觸摸群山,使群山冒煙。

6求你發出閃電驅散敵人,

求你射出利箭擊潰他們。

7求你從天上伸手從驚濤駭浪中拯救我,

從外族人手中拯救我。

8他們滿口謊言,

起誓也心懷詭詐。

9上帝啊,我要向你唱新歌,

用十弦琴歌頌你。

10你使君王得勝,

救你的僕人大衛逃離刀劍的殺戮。

11求你從外族人手中拯救我,

他們滿口謊言,

起誓也心懷詭詐。

12願我們的兒子年輕時像茁壯的樹木,

我們的女兒像宮殿中精雕的柱子。

13願我們的倉庫堆滿各樣的穀物,

我們的羊在田野繁衍眾多,

成千上萬。

14願我們的牲口馱滿貨物144·14 牲口馱滿貨物」或譯「繁殖眾多」。

我們的城牆固若金湯,

無人被擄,街上沒有哭叫聲。

15生活在這種光景裡的人有福了!

尊耶和華為上帝的人有福了!