Masalimo 135 – CCL & BPH

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 135:1-21

Salimo 135

1Tamandani Yehova.

Tamandani dzina la Yehova;

mutamandeni, inu atumiki a Yehova,

2amene mumatumikira mʼnyumba ya Yehova,

mʼmabwalo a nyumba ya Mulungu wathu.

3Tamandani Yehova, pakuti Yehova ndi wabwino;

imbani nyimbo zotamanda dzina lake, pakuti nʼkokoma kutero,

4Pakuti Yehova wasankha Yakobo kuti akhale wake,

Israeli kuti akhale chuma chake chapamtima.

5Ndikudziwa kuti Yehova ndi wamkulu,

kuti Ambuye athu ndi wamkulu kuposa milungu yonse.

6Yehova amachita chilichonse chimene chimamukomera,

kumwamba ndi dziko lapansi,

ku nyanja zazikulu ndi ku malo ake onse akuya.

7Iye amatulutsa mitambo kuchokera ku malekezero a dziko lapansi,

amatumiza zingʼaningʼani pamodzi ndi mvula

ndipo amatulutsa mphepo ku malo ake osungiramo.

8Anakantha ana oyamba kubadwa a Igupto,

ana oyamba kubadwa a anthu ndi nyama.

9Iye anatumiza zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa pakati pako, iwe Igupto,

kutsutsana ndi Farao pamodzi ndi atumiki ake onse.

10Iye anakantha mitundu yambiri ya anthu

ndi kupha mafumu amphamvu:

11Sihoni mfumu ya Aamori,

Ogi mfumu ya Basani,

ndi maufumu onse a ku Kanaani;

12ndipo anapereka dziko lawo ngati cholowa,

cholowa cha anthu ake Aisraeli.

13Dzina lanu, Inu Yehova, ndi losatha mpaka muyaya,

mbiri yanu, Inu Yehova, idziwika mibado yonse.

14Pakuti Yehova adzaonetsa kuti anthu ake ngosalakwa,

ndipo adzachitira chifundo atumiki ake.

15Mafano a mitundu ya anthu ndi siliva ndi golide,

opangidwa ndi manja a anthu.

16Pakamwa ali napo koma sayankhula

maso ali nawo, koma sapenya;

17makutu ali nawo, koma sakumva

ndipo mʼkamwa mwawo mulibe mpweya uliwonse.

18Iwo amene amapanga mafanowo adzakhala ngati mafanowo,

chimodzimodzinso iwo amene amadalira mafanowo.

19Inu nyumba ya Israeli, tamandani Yehova;

inu nyumba ya Aaroni, tamandani Yehova;

20Inu nyumba ya Levi, tamandani Yehova;

Inu amene mumaopa Iye, tamandani Yehova.

21Wodalitsika ndi Yehova kuchokera mʼZiyoni,

amene amakhala mu Yerusalemu.

Tamandani Yehova.

Bibelen på hverdagsdansk

Salmernes Bog 135:1-21

Herren er stor

1Halleluja!

Lovpris Herren, I hans tjenere,

2I, som tjener i Guds hus,

I, som arbejder i templets forgård.

3Pris Herren, for han er god.

Lovsyng hans herlighed og nåde,

4for Herren har udvalgt Israel.

Jakobs efterkommere er hans ejendomsfolk.

5Jeg ved, at Herren er stor,

større end alle de andre folks guder.

6Han gør alt, hvad han vil,

på jorden, i himlen og i havets dyb.

7Han kalder uvejrsskyer sammen,

sender lynene af sted,

slipper stormen løs

og lader regnen styrte ned.

8Alle de førstefødte i Egypten slog han ihjel,

både blandt mennesker og dyr.

9Han udførte vældige tegn og undere

for øjnene af Farao og hele hans folk.

10Han tilintetgjorde stærke nationer,

besejrede mægtige herskere,

11amoritterkongen Sihon, kong Og af Bashan

og alle kongerne i Kana’ans land.

12Han gav deres lande til sit eget folk,

Israel fik det som sin arvelod.

13Herre, dit ry vil altid bestå,

din berømmelse kender ingen grænser.

14For Herren fører sit folks sag,

han er barmhjertig mod sine tjenere.

15Andre folkeslag dyrker afguder,

som de selv har lavet af sølv og guld.

16Afguderne har mund, men kan ikke tale.

De har øjne, men kan ikke se.

17De har ører, men kan ikke høre,

for der er ingen livsånde i dem.

18De mennesker, der formede afgudsbillederne,

er lige så tåbelige som deres guder.

19Pris Herren, Israels folk!

Pris Herren, Arons slægt!

20Pris Herren, alle I levitter!

Pris Herren, alle I, som kender ham!

21Lovet være Herren, som bor på Zion,

han som har sin bolig i Jerusalem.

Halleluja!