Marko 12 – CCL & SNC

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Marko 12:1-44

Fanizo la Alimi

1Kenaka Iye anayamba kuyankhula nawo mʼmafanizo: “Munthu wina analima munda wamphesa. Anamanga mpanda mozungulira, nakumba dzenje lofinyiramo mphesa ndipo anamanga nsanja. Anawubwereketsa munda wamphesawo kwa alimi ena napita ku dziko lina. 2Pa nthawi yokolola anatumiza wantchito kwa alimiwo kuti akatenge kuchokera kwa iwo zina mwa zipatso za munda wamphesa. 3Koma iwo anamugwira, namumenya ndi kumupirikitsa wopanda kanthu. 4Kenaka anatumizanso wantchito wina kwa iwo. Iwo anamumenya munthuyo pamutu ndipo anamuzunza mochititsa manyazi. 5Anatumizanso wina, ndipo iwo anamupha. Anatumizanso ena ambiri; ena a iwo anawamenya, ena anawapha.

6“Munthu uja anatsala ndi mwana mmodzi, wamwamuna amene amamukonda. Pomaliza anamutumiza mwanayo nati, ‘Adzamuchitira ulemu mwana wanga.’

7“Koma alimi aja anati kwa wina ndi mnzake, ‘Uyu ndi mlowamʼmalo. Tiyeni timuphe, ndipo cholowacho chidzakhala chathu.’ 8Ndipo anamutenga ndi kumupha, ndipo anamuponya kunja kwa munda wamphesa.

9“Kodi nanga mwini munda wamphesa adzachita chiyani? Iye adzabwera ndi kupha alimiwo nadzapereka munda wamphesawo kwa ena. 10Kodi simunawerenge lemba lakuti:

“ ‘Mwala umene amisiri omanga nyumba anawukana

wakhala mwala wa pa ngodya.

11Ambuye achita zimenezi,

ndipo ndi zodabwitsa mʼmaso mwathu?’ ”

12Ndipo akulu a ansembe, aphunzitsi a malamulo ndi akuluakulu anafunafuna njira yoti amugwirire Iye chifukwa amadziwa kuti anayankhula fanizoli mowatsutsa iwo. Koma amaopa gulu la anthu; ndipo anamusiya napita.

Za Kupereka Msonkho kwa Kaisara

13Pambuyo pake anatuma ena a Afarisi ndi Aherode kwa Yesu kuti adzamukole mawu ake. 14Iwo anabwera kwa Iye nati, “Aphunzitsi, ife tikudziwa kuti Inu ndi munthu amene mumanena zoona. Inu simutengeka ndi anthu, chifukwa simusamala kuti ndi ndani; koma mumaphunzitsa njira ya Mulungu molingana ndi choonadi. Kodi ndi koyenera kupereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi? 15Kodi ife tipereke msonkho kapena ayi?”

Koma Yesu anadziwa chinyengo chawo. Iye anafunsa kuti, “Bwanji mukufuna kundipeza chifukwa? Bweretsani ndalama kuti ndiyione.” 16Iwo anamubweretsera ndalama, ndipo anawafunsa kuti, “Kodi nkhope iyi ndi ya ndani? Nanga malembawa ndi a ndani?”

Iwo anayankha kuti, “Za Kaisara.”

17Ndipo Yesu anawawuza kuti, “Perekani kwa Kaisara zake za Kaisara ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.”

Ndipo anazizwa naye.

Za Ukwati ndi Kuuka kwa Akufa

18Kenaka Asaduki, amene amati kulibe kuuka kwa akufa, anabwera kwa Iye ndi funso. 19Iwo anati, “Aphunzitsi, Mose anatilembera kuti munthu akamwalira ndi kusiya mkazi wopanda ana, mʼbale wa munthu womwalirayo akuyenera kukwatira mkaziyo kuti amuberekere ana mʼbale wakeyo. 20Tsopano panali abale asanu ndi awiri. Woyamba anakwatira namwalira wosabereka ana. 21Wachiwiri anakwatira mkazi wamasiyeyo, koma iye anamwalira wosabereka mwana. Zinali chimodzimodzi ndi wachitatu. 22Kunena zoona, palibe ndi mmodzi yemwe wa asanu ndi awiriwo anasiya ana. Pomaliza, mkaziyo anamwaliranso. 23Pa kuuka kwa akufa, adzakhala mkazi wa yani pakuti anakwatiwa ndi onse asanu ndi awiri?”

24Yesu anawafunsa kuti, “Kodi si pamenepa nanga pomwe mumalakwira chifukwa simukudziwa malemba kapena mphamvu za Mulungu? 25Pamene akufa auka, sadzakwatira kapena kukwatiwa; adzakhala ngati angelo kumwamba. 26Tsopano kunena zakuti akufa amauka, kodi simunawerenge mʼbuku la Mose, pa nkhani yachitsamba choyaka moto, mmene Mulungu anati kwa iye, ‘Ine ndine Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo?’ 27Iye si Mulungu wa anthu akufa, koma wa amoyo. Inu mwalakwitsa kwambiri!”

Lamulo Lalikulu Koposa

28Mmodzi wa aphunzitsi amalamulo anabwera namva iwo akukambirana motsutsana. Poona kuti Yesu anawapatsa yankho labwino, anamufunsa Iye kuti, “Mwa malamulo onse, kodi lopambana koposa ndi liti?”

29Yesu anayankha kuti, “Lamulo loposa onse ndi ili: ‘Tamvani inu Aisraeli! Yehova Mulungu wathu, Yehova ndi mmodzi! 30Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse ndi mphamvu zako zonse.’ 31Lachiwiri ndi ili: ‘Konda mnansi wako monga iwe mwini.’ Palibe lamulo lina loposa amenewa.”

32Munthuyo anayankha kuti, “Mwanena bwino Aphunzitsi. Mwalondola ponena kuti Mulungu ndi mmodzi ndipo palibe wina wofanana naye koma Iye yekha. 33Kumukonda Iye; ndi mtima wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu zako zonse, ndi kukonda mnansi wako monga iwe mwini, ndi zopambana kuposa zopereka ndi nsembe zopsereza.”

34Yesu ataona kuti wayankha mwanzeru, anati kwa iye, “Iwe suli kutali ndi ufumu wa Mulungu.” Ndipo kuyambira pamenepo panalibe ndi mmodzi yemwe anayesa kumufunsanso.

Khristu ndi Mwana wa Yani?

35Yesu akuphunzitsa mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu, anafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani aphunzitsi amalamulo amanena kuti, ‘Khristu ndi Mwana wa Davide?’ 36Pajatu Davide mwini wake, poyankhula mwa Mzimu Woyera, ananena kuti,

“Ambuye anati kwa Ambuye anga:

‘Khalani pa dzanja langa lamanja

kufikira nditayika adani anu

pansi pa mapazi anu.’

37Davide mwini wake amutchula Iye, ‘Ambuye.’ Nanga angakhale bwanji mwana wake?”

Gulu lalikulu la anthu linamvetsera ndi chisangalalo.

Yesu Achenjeza Anthu za Aphunzitsi a Malamulo

38Pamene ankaphunzitsa, Yesu anati, “Samalani ndi aphunzitsi a malamulo. Amakonda kuyendayenda atavala mikanjo ikuluikulu ndi kumalonjeredwa mʼmisika. 39Ndipo amakhala pa mipando yofunika kwambiri mʼmasunagoge ndi malo aulemu pa maphwando. 40Amawononga chuma cha akazi amasiye ndiponso amapemphera mapemphero aatali odzionetsera. Anthu oterewa adzalangidwa kwambiri.”

Chopereka cha Mayi Wamasiye

41Yesu anakhala pansi moyangʼanana ndi pamene amaperekera zopereka ndipo amaona anthu akupereka ndalama zawo mʼthumba la Nyumba ya Mulungu. Anthu ambiri olemera anaponya ndalama zambiri. 42Koma mkazi wamasiye, wosauka anabwera ndi kuyikamo tindalama tiwiri ta kopala, tongokwanira theka la ndalama.

43Yesu anayitana ophunzira ake nati, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti mayi wosauka wamasiyeyu waponya zambiri mʼthumbali kuposa ena onsewa. 44Iwo apereka molingana ndi chuma chawo; koma iye, mwaumphawi wake, wapereka zonse anali nazo ngakhale zoti akanagulira chakudya.”

Slovo na cestu

Marek 12:1-44

Ježíš vypráví podobenství o boháči

1Začal pak vyprávět následující příběh: „Jeden člověk založil vinici. Obehnal ji plotem, postavil lis na víno a vystavěl hlídkovou věž. Potom vinici pronajal pachtýřům a sám odcestoval. 2Když přišla doba vinobraní, pověřil jednoho ze svých sluhů, aby od pachtýřů vybral podíl z úrody, který mu náležel. 3Ale pachtýři sluhu ztloukli a vyhodili s prázdnou.

4Majitel tam poslal jiného. Po něm začali házet kamení, těžce ho zranili na hlavě a vyhnali. 5Poslal tam tedy dalšího a toho zabili. Tak majitel vinice postupně vyslal ještě několik svých lidí. Ke všem se chovali surově, některé ztloukli, jiné ubili. 6Nakonec tam vypravil svého jediného milovaného syna. Domníval se, že před ním přece jen budou mít respekt.

7Ale nájemci si řekli: ‚To je jediný dědic. Zabijme ho a vinice bude naše.‘ 8A tak se stalo. Syna zavraždili a tělo vyhodili z vinice ven.

9Co si myslíte, že udělá ten majitel, až přijde? Spravedlivě je odsoudí k smrti a vinici pronajme jiným. 10Vzpomeňte si, že v Bibli je psáno:

‚Kámen, kterým stavitelé opovrhli,

se nakonec stal kamenem nejdůležitějším

– svorníkem klenby.

11Pán Bůh to tak učinil

a my stojíme v údivu.‘ “

12Židovští vůdci pochopili, že ten příběh platil jim, že oni jsou těmi proradnými pachtýři. Rádi by byli Ježíše zatkli, ale báli se davu. Prozatím od toho museli upustit.

Židé se ptají Ježíše na placení daně

13Poslali však za ním několik farizejů a členů Herodovy strany, aby ho vyprovokovali k nějakému žalovatelnému výroku.

14„Mistře,“ oslovili ho úlisně, „víme, že pravda je ti nade všechno; ať se to komu líbí či nelíbí, učíš pravdě tak, jak ji znáš od Boha. Řekni nám: máme platit Římu daně, nebo nemáme?“

15Ježíš však nastraženou past prohlédl. „Co to na mě zkoušíte, podejte mi peníz!“

16Když mu ho podali, zeptal se: „Čí obraz a jméno je na té minci?“ „Římského císaře,“ řekli.

17„Dávejte tedy císaři, co je císařovo, a co je Boží, dávejte Bohu.“ Tak jim to zase nevyšlo.

Židé se ptají Ježíše na vzkříšení

18Potom přišli se záludnou otázkou příslušníci skupiny saducejů, kteří nevěřili ve vzkříšení z mrtvých.

19Řekli: „Mistře, v Mojžíšově zákoně je psáno: Zemře-li ženatý muž a nezanechá po sobě žádného dědice, jeho svobodný bratr je povinen oženit se s vdovou a zplodit bratrovi potomka. 20Povíme ti příběh: Bylo sedm bratrů. Nejstarší se oženil, brzo však zemřel a nenechal po sobě žádných dětí. 21Druhý se oženil s vdovou, ale brzy zemřel bezdětný. Tak to stále pokračovalo, až zemřel i poslední. Nikdo z nich nezanechal dědice. 22Nakonec zemřela i ta žena.

23Naše otázka zní: Čí bude ta žena po vzkříšení? Vždyť ji mělo za manželku všech sedm.“

24Ježíš odpověděl: „Vaše chyba je v tom, že neznáte Bibli a nevěříte v Boží moc. Manželství je záležitostí pozemského života. 25Až lidé vstanou z mrtvých, nebudou už mezi nimi tělesné svazky. Přetrvají jen svazky ducha.

26-27A o vzkříšení samotném vůbec nepochybujte. Cožpak jste nečetli o Mojžíšovi a hořícím keři? Jak se tam Bůh tehdy představil? ‚Já jsem Bůh Abrahámův, Bůh Izákův, Bůh Jákobův.‘ Když o lidech zesnulých před mnoha staletími říká: ‚já JSEM jejich Bůh,‘ pak je jasné, že pro něj nikdy nepřestali existovat. Vidíte, jak jste vedle.“

Židé se ptají Ježíše na největší přikázání

28Tyto rozhovory sledoval jeden z učitelů zákona. Zdálo se mu, že Ježíš odpovídá znamenitě. A tak mu předložil svůj problém: „Které přikázání je nejdůležitější?“

29Ježíš nezaváhal:

„První přikázání zní takto: Slyš Izraeli, Pak Bůh je jediný Pán. 30Miluj ho z celého srdce, celou bytostí a ze všech sil.

31A to druhé: Miluj druhého člověka tak, jako miluješ sebe. Nejsou důležitější přikázání než tato.“

32„Mistře, tys dobře vystihl to podstatné,“ musel uznat tazatel. „Bůh je jen jeden a kromě něho není jiného. 33Milovat ho z celého srdce, celým rozumem a vší silou své vůle a druhé lidi milovat jako sebe – to je víc než všechny oběti zvířat na oltáři.“

34„Ty nejsi daleko od Božího království,“ ocenil jeho postoj Ježíš. Pak už se ho nikdo neodvážil na nic zeptat.

Židé nemohou odpovědět na Ježíšovu otázku

35Později, když Ježíš učil v chrámu, položil otázku: „Z čeho náboženští učitelé usuzují, že Kristus musí být potomkem krále Davida? 36Vždyť sám David napsal, inspirován Duchem svatým:

‚Bůh řekl mému Pánu:

Seď po mé pravici,

dokud ti tvé nepřátele nepoložím k nohám.‘

37Když ho David nazývá svým Pánem, jak by tedy mohl být Davidovým synem?“

Ježíš varuje před náboženskými vůdci

Ježíš měl vždycky mnoho pozorných posluchačů. 38Jednou je varoval:

„Dejte si pozor na učitele, kteří se na veřejnosti procházejí v krásných šatech a čekají, že je lidé budou uctivě zdravit a klanět se jim. 39Rádi si zajišťují přední sedadla v modlitebnách a čestná místa na hostinách. 40Vyjídají vdovské domy tím, že si dávají platit za modlitby, které úmyslně protahují. Protože učí jiné a takhle se chovají, Bůh je potrestá tím přísněji.“

Chudá vdova dává vše, co má

41Jednou si Ježíš sedl proti chrámové pokladně a pozoroval lidi. Mnozí bohatí tam vkládali značné částky peněz. 42Přišla také jedna chudá vdova a do pokladny vhodila dvě drobné mince.

43Ježíš si zavolal své učedníky a řekl jim: „Poslyšte, ta chudá vdova vlastně dala víc než boháči. 44Ti dávali jen přebytky, bez kterých se snadno obejdou, ale ta žena dala všechno, co měla na živobytí.“