Machitidwe a Atumwi 25 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Machitidwe a Atumwi 25:1-27

Paulo ku Bwalo la Milandu la Festo

1Patapita masiku atatu Festo atafika mʼdera lake, anachoka ku Kaisareya ndi kupita ku Yerusalemu. 2Kumeneko akulu a ansembe ndi atsogoleri a Chiyuda anabwera kwa iye ndi kumufotokozera mlandu wa Paulo. 3Iwo anamupempha Festo kuti awakomere mtima potumiza Paulo ku Yerusalemu, pakuti anali atakonzekera chiwembu kuti amuphe Pauloyo pa njira. 4Festo anayankha kuti, “Paulo akusungidwa ku Kaisareya, ndipo ndipita kumeneko posachedwa. 5Ena mwa atsogoleri anu apite nane kumeneko, kuti akafotokoze mlandu wa munthuyu, ngati anachita kanthu kalikonse kolakwika.”

6Festo atakhala nawo masiku asanu ndi atatu kapena khumi iye anapita ku Kaisareya, ndipo mmawa mwake anayitanitsa bwalo nalamula kuti abweretse Paulo pamaso pake. 7Paulo atafika, Ayuda amene anafika kuchokera ku Yerusalemu anayima momuzungulira. Iwo anamunenera zinthu zoopsa zambiri zimene sakanatha kubweretsa umboni wake.

8Kenaka Paulo ananena mawu ake odziteteza kuti, “Ine sindinalakwirepo lamulo la Ayuda, kapena Nyumba ya Mulungu kapenanso Kaisara.”

9Festo, pofuna kuti Ayuda amukonde anafunsa Paulo kuti, “Kodi iwe ukufuna kupita ku Yerusalemu, kuti kumeneko ukafotokoze mlandu wako pamaso panga?”

10Paulo anayankha kuti, “Ine tsopano ndayima pamaso pa bwalo la milandu la Kaisara, ndiko kumene ayenera kundiweruza. Ine sindinalakwire Ayuda, monga inu mukudziwa bwino. 11Koma ngati ndili wolakwa, ngati ndachita kanthu koyenera kuphedwa, ine sindikukana kufa. Koma ngati mlandu umene abweretsa Ayudawa siwoona, palibe munthu angathe kundipereka mʼmanja mwawo. Ndikupempha kuti ndikaweruzidwe ndi Kaisara!”

12Festo atakambirana ndi akuluakulu abwalo lake, anati, “Popeza wapempha kupita kwa Kaisara, kwa Kaisara udzapitadi!”

Festo Afotokozera Mfumu Agripa

13Patapita masiku ochepa mfumu Agripa pamodzi ndi Bernisi anabwera ku Kaisareya kudzalonjera Festo. 14Atakhala kumeneko masiku angapo, Festo anafotokozera mfumuyo za mlandu wa Paulo. Iye anati, “Kuli munthu wina kuno amene Felike anamusiya mʼndende. 15Nditapita ku Yerusalemu akulu a ansembe ndi akuluakulu a Ayuda anandifotokozera mlandu wake ndipo anandipempha kuti ndigamule kuti ndi wolakwa.

16“Ine ndinawayankha kuti si mwambo wa Aroma kungomupereka munthu ayi. Munthu woyimbidwa mlanduyo amayenera kukumana nawo omunenezawo, kuti iye akhale ndi mwayi woyankhapo pa zimene akumuyimba mlanduzo. 17Atabwera kuno pamodzi ndi ine, sindinachedwetse mlanduwo, koma ndinayitanitsa bwalo mmawa mwake ndi kulamula kuti amubweretse munthuyo. 18Omuyimba mlandu aja atayimirira kuti ayankhule, iwo sananene cholakwa chilichonse chimene ndimayembekezera. 19Mʼmalo mwake, anatsutsana naye pa fundo zina za chipembedzo chawo ndi za munthu wakufa, dzina lake Yesu, amene Paulo akuti ali moyo. 20Ine ndinathedwa nzeru wosadziwa momwe ndikanafufuzira nkhaniyi; kotero ndinafunsa ngati akanafuna kupita ku Yerusalemu kuti akaweruzidwe kumeneko. 21Koma Paulo anapempha kuti akaonekere pamaso pa mfumu ya Chiroma, ndipo ndinalamula kuti asungidwe mpaka pamene ndidzamutumize kwa Kaisara.”

22Ndipo Agripa anati kwa Festo, “Ine ndikufuna ndimumve ndekha munthu ameneyu.” Iye anayankha kuti, “Mudzamumva mawa.”

Paulo Pamaso pa Agripa

23Mmawa mwake Agripa ndi Bernisi anabwera mwaulemu waukulu waufumu nalowa mʼbwalo la milandu pamodzi ndi akulu a asilikali ndiponso akuluakulu a mu mzindawo. Atalamula Festo kuti Paulo abwere, anabweradi. 24Festo anati, “Mfumu Agripa, ndi onse amene muli nafe pano, mukumuona munthu uyu! Ayuda onse anandipempha ine za uyu ku Yerusalemu ndiponso kuno ku Kaisareya, mofuwula kuti, ameneyu sayenera kukhala ndi moyo. 25Ine ndinapeza kuti iyeyu sanachite kanthu koyenera kufa, koma popeza anapempha kuti apite kwa mfumu ya Chiroma, ine ndinatsimikiza zomutumiza ku Roma. 26Koma ndilibe kanthu kenikeni koti ndilembere Wolemekezekayo za iyeyu. Nʼchifukwa chake ndabwera naye pamaso pa nonsenu, makamaka kwa inuyo mfumu Agripa, kuti mwina mukamufunsitsa ndikhale ndi choti ndilembe. 27Pakuti ine ndikuganiza kuti ndi chinthu chopanda nzeru kutumiza wamʼndende popanda kutchula zifukwa zenizeni za mlandu wake.”

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

使徒行傳 25:1-27

保羅在非斯都面前申辯

1非斯都上任三天後,便從凱撒利亞啟程上耶路撒冷2祭司長和猶太人的首領向他控告保羅3懇求他將保羅押回耶路撒冷,他們想在途中埋伏殺害保羅4非斯都卻拒絕道:「保羅現在關押在凱撒利亞,我很快會回到那裡。 5讓你們的首領跟我一起去吧,如果那人有什麼過犯,可以在那裡告他。」

6非斯都耶路撒冷只逗留了十天八天,便返回了凱撒利亞。第二天,他開庭審訊,命人將保羅帶上來。 7保羅被帶來後,那些從耶路撒冷下來的猶太人站在他周圍,指控他犯了各樣嚴重的罪,但是都沒有證據。 8保羅為自己辯護說:「我從來沒有違背猶太律法,褻瀆聖殿或反叛凱撒!」 9非斯都為了討好猶太人,就對保羅說:「你是否願意回耶路撒冷接受我的審訊?」

10保羅說:「我此刻正站在凱撒的法庭上,這就是我應該受審的地方。你很清楚,我並沒有做過什麼對不起猶太人的事。 11如果我做錯了,犯了該死的罪,我決不逃避!但他們對我的指控毫無根據,誰也不能把我交給他們。我要向凱撒上訴!」

12非斯都和議會商討後,說:「你說要上訴凱撒,就去見凱撒吧!」

非斯都請教亞基帕王

13過了幾天,亞基帕王和百妮姬一起到凱撒利亞問候非斯都14他們在那裡住了多日,非斯都對王提起保羅的案子,說:「我這裡有一個囚犯,是前任總督腓利斯留下來的。 15上次我去耶路撒冷的時候,猶太人的祭司長和長老控告他,要求我定他的罪。 16我告訴他們,按照羅馬人的規矩,被告還沒有跟原告對質和自辯之前,不能定他的罪。 17後來他們跟我一起來到這裡,我沒有耽誤,第二天就開庭,吩咐把那人帶出來審訊。 18他們都站起來當面指控他,但所告的並非我料想的罪行, 19不過是關於他們的宗教和一個叫耶穌的人的一些爭論。耶穌已經死了,保羅卻說他仍然活著。 20我不知如何審理這些事情,就問被告是否願意上耶路撒冷受審。 21保羅請求留下來,聽皇帝定奪,所以我下令仍然扣留他,等著送交凱撒。」

22亞基帕非斯都說:「我想親自聽聽他的申訴。」

非斯都說:「你明天就會聽到。」

23第二天,亞基帕百妮姬在眾千夫長和城中達官貴人的陪同下,聲勢浩大地進了法庭。非斯都下令把保羅帶上來後, 24說:「亞基帕王和在座的各位,你們看,就是這個人,所有的猶太人在這裡和耶路撒冷都請求我處死他。 25但我發現他並沒有犯什麼該死的罪。既然他要向皇帝上訴,我決定把他押去。 26只是關於這個人,我沒有確切的事由可以奏明皇帝25·26 希臘文是「主上」,用於對羅馬皇帝的尊稱。。所以,我把他帶到各位面前,特別是亞基帕王面前,以便在審訊之後,我可以有所陳奏。 27因為在我看來,解送犯人卻不奏明罪狀不合情理。」