Machitidwe a Atumwi 20 – CCL & KJV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Machitidwe a Atumwi 20:1-38

Paulo Apita ku Makedoniya ndi ku Grisi

1Litatha phokoso, Paulo anayitanitsa ophunzira ndipo atawalimbikitsa anawatsanzika ndipo ananyamuka kupita ku Makedoniya. 2Iye anayendera madera a kumeneko, nalimbitsa mtima anthu, ndipo pomaliza pake anapita ku Grisi. 3Kumeneko anakhala miyezi itatu. Popeza kuti Ayuda anakonza zomuchita chiwembu pamene amati azinyamuka kupita ku Siriya pa sitima ya pamadzi, iye anaganiza zobwereranso kudzera ku Makedoniya. 4Iye anapita pamodzi ndi Sopatro mwana wa Puro wa ku Bereya, Aristariko ndi Sekundo a ku Tesalonika, Gayo wa ku Derbe ndi Timoteyo, ndipo a ku Asiya anali Tukiko ndi Trofimo. 5Anthu amenewa anatsogola ndipo anakatidikira ku Trowa. 6Koma ife tinayenda pa sitima ya pamadzi kuchokera ku Filipi chitatha Chikondwerero cha Buledi wopanda Yisiti. Patapita masiku asanu tinakumana nawo enawo ku Trowa, ndipo tinakhala kumeneko masiku asanu ndi awiri.

Paulo Aukitsa Utiko ku Trowa

7Pa tsiku loyamba la Sabata, tinasonkhana kuti tidye mgonero. Paulo analalikira kwa anthu chifukwa anaganiza zoti achoke tsiku linalo, ndipo analalika mpaka pakati pa usiku. 8Munali nyale zambiri mʼchipinda chammwamba mʼmene tinasonkhanamo. 9Pa chipinda chachitatu chammwamba cha nyumbayo, pa zenera, panakhala mnyamata wina dzina lake Utiko, amene ankasinza pomwe Paulo amayankhulabe. Atagona tulo, iye anagwa pansi kuchokera pa chipinda chammwamba ndipo anamutola atafa. 10Paulo anatsika, nadziponya pa mnyamatayo, namukumbatira. Paulo anati, “Musadandaule, ali moyo!” 11Kenaka Paulo anakweranso, mʼchipinda muja nanyema buledi nadya. Atayankhula mpaka kucha, anachoka. 12Anthu anatenga mnyamatayo kupita kwawo ali moyo ndipo anatonthozedwa mtima kwambiri.

Paulo Alawirana ndi Akulu Ampingo a ku Efeso

13Ife tinatsogola kukakwera sitima ya pa madzi kupita ku Aso, kumene tinayembekeza kukatenga Paulo. Iye anakonza motero chifukwa amayenda wapansi. 14Pamene anakumana nafe ku Aso tinamutenga ndipo tinapita ku Mitilene. 15Mmawa mwake tinachoka kumeneko pa sitima ya pamadzi ndipo tinafika pafupi ndi Kiyo. Tsiku linalo tinawolokera ku Samo, ndipo tsiku linanso tinafika ku Mileto. 16Paulo anali atatsimikiza kuti alambalale Efeso kuopa kutaya nthawi ku Asiya, pakuti ankafulumira kuti akafike ku Yerusalemu kuti ngati nʼkotheka kuti tsiku la Pentekosite akakhale ali ku Yerusalemu.

17Paulo ali ku Mileto, anatumiza mawu ku Efeso kuyitana akulu ampingo. 18Iwo atafika, Paulo anati, “Inu mukudziwa mmene ndinakhalira nanu nthawi yonse imene ndinali nanu kuyambira tsiku loyamba limene ndinafika ku Asiya. 19Ndinatumikira Ambuye modzichepetsa kwambiri ndiponso ndi misozi, ngakhale ndinayesedwa kwambiri ndi ziwembu za Ayuda. 20Inu mukudziwa kuti, sindinakubisireni kanthu kalikonse kopindulitsa koma ndinakuphunzitsani poyera komanso nyumba ndi nyumba. 21Ine ndinawuza Ayuda komanso Agriki kuti ayenera kutembenukira kwa Mulungu polapa ndikuti akhulupirire Ambuye athu Yesu.

22“Ndipo tsopano, mokakamizidwa ndi Mzimu, ndikupita ku Yerusalemu, sindikudziwa zimene zikandichitikire kumeneko.” 23Chimene ndikudziwa ndi chakuti Mzimu Woyera wandichenjeza mu mzinda uliwonse kuti ndende ndi mavuto zikundidikira. 24Koma sindilabadira konse za moyo wanga ngati kuti ndi wa mtengo wapatali kwa ine, malingana ndikatsirize ntchito yanga ndi utumiki umene Ambuye Yesu anandipatsa, ntchito yochitira umboni Uthenga Wabwino wachisomo cha Mulungu.

25“Tsopano ndikudziwa kuti inu nonse amene ndinakuyenderani ndi kumakulalikirani ufumu wa Mulungu simudzaonanso nkhope yanga. 26Chifukwa chake, ine ndikukuwuzani lero kuti ndilibe mlandu ndi munthu aliyense. 27Pakuti sindinakubisireni pokulalikirani chifuniro chonse cha Mulungu. 28Mudziyangʼanire nokha ndiponso muyangʼanire gulu lankhosa limene Mzimu Woyera anakuyikani kuti mukhale oyangʼanira ake. Khalani abusa a mpingo wa Mulungu umene Iye anawugula ndi magazi ake. 29Ndikudziwa kuti ndikachoka ine, padzafika mimbulu yolusa pakati panu imene sidzalekerera gulu lankhosalo. 30Ngakhale pakati pa inu nokha padzapezeka anthu oyankhula zonama ndi cholinga chofuna kukhala ndi ophunzira kuti awatsate. 31Tsono inu, samalani! Kumbukirani kuti kwa zaka zitatu, usana ndi usiku ndiponso ndi misozi sindinaleke kuchenjeza aliyense wa inu.

32“Tsopano ine ndikukuperekani kwa Mulungu ndiponso kwa mawu a chisomo chake, amene ali ndi mphamvu zokulitsa inu ndi kukupatsani chuma pakati pa onse amene anayeretsedwa. 33Ine sindinasirire siliva kapena golide kapena zovala za munthu aliyense. 34Inu nomwe mukudziwa kuti manja angawa ananditumikira kuti tipeze zimene ine ndi anzanga tinkazifuna. 35Pa zonse zimene ndinachita, ndinakuonetsani kuti pogwira ntchito molimbika motere tiyenera kuthandiza ofowoka, pokumbukira mawu a Ambuye Yesu akuti, ‘Kupereka kumadalitsa kuposa kulandira.’ ”

36Atanena zimenezi, anagwada pansi pamodzi ndi ena onse, napemphera. 37Onse analira pamene amamukumbatira ndi kupsompsona. 38Chimene chinamvetsa chisoni kwambiri ndi mawu ake akuti sadzaonanso nkhope yake. Kenaka iwo anamuperekeza ku sitima yapamadzi.

King James Version

Acts 20:1-38

1And after the uproar was ceased, Paul called unto him the disciples, and embraced them, and departed for to go into Macedonia. 2And when he had gone over those parts, and had given them much exhortation, he came into Greece, 3And there abode three months. And when the Jews laid wait for him, as he was about to sail into Syria, he purposed to return through Macedonia. 4And there accompanied him into Asia Sopater of Berea; and of the Thessalonians, Aristarchus and Secundus; and Gaius of Derbe, and Timotheus; and of Asia, Tychicus and Trophimus. 5These going before tarried for us at Troas. 6And we sailed away from Philippi after the days of unleavened bread, and came unto them to Troas in five days; where we abode seven days. 7And upon the first day of the week, when the disciples came together to break bread, Paul preached unto them, ready to depart on the morrow; and continued his speech until midnight. 8And there were many lights in the upper chamber, where they were gathered together. 9And there sat in a window a certain young man named Eutychus, being fallen into a deep sleep: and as Paul was long preaching, he sunk down with sleep, and fell down from the third loft, and was taken up dead. 10And Paul went down, and fell on him, and embracing him said, Trouble not yourselves; for his life is in him. 11When he therefore was come up again, and had broken bread, and eaten, and talked a long while, even till break of day, so he departed. 12And they brought the young man alive, and were not a little comforted.

13¶ And we went before to ship, and sailed unto Assos, there intending to take in Paul: for so had he appointed, minding himself to go afoot. 14And when he met with us at Assos, we took him in, and came to Mitylene. 15And we sailed thence, and came the next day over against Chios; and the next day we arrived at Samos, and tarried at Trogyllium; and the next day we came to Miletus. 16For Paul had determined to sail by Ephesus, because he would not spend the time in Asia: for he hasted, if it were possible for him, to be at Jerusalem the day of Pentecost.

17¶ And from Miletus he sent to Ephesus, and called the elders of the church. 18And when they were come to him, he said unto them, Ye know, from the first day that I came into Asia, after what manner I have been with you at all seasons, 19Serving the Lord with all humility of mind, and with many tears, and temptations, which befell me by the lying in wait of the Jews: 20And how I kept back nothing that was profitable unto you, but have shewed you, and have taught you publickly, and from house to house, 21Testifying both to the Jews, and also to the Greeks, repentance toward God, and faith toward our Lord Jesus Christ. 22And now, behold, I go bound in the spirit unto Jerusalem, not knowing the things that shall befall me there: 23Save that the Holy Ghost witnesseth in every city, saying that bonds and afflictions abide me. 24But none of these things move me, neither count I my life dear unto myself, so that I might finish my course with joy, and the ministry, which I have received of the Lord Jesus, to testify the gospel of the grace of God. 25And now, behold, I know that ye all, among whom I have gone preaching the kingdom of God, shall see my face no more. 26Wherefore I take you to record this day, that I am pure from the blood of all men. 27For I have not shunned to declare unto you all the counsel of God.

28¶ Take heed therefore unto yourselves, and to all the flock, over the which the Holy Ghost hath made you overseers, to feed the church of God, which he hath purchased with his own blood. 29For I know this, that after my departing shall grievous wolves enter in among you, not sparing the flock. 30Also of your own selves shall men arise, speaking perverse things, to draw away disciples after them. 31Therefore watch, and remember, that by the space of three years I ceased not to warn every one night and day with tears. 32And now, brethren, I commend you to God, and to the word of his grace, which is able to build you up, and to give you an inheritance among all them which are sanctified. 33I have coveted no man’s silver, or gold, or apparel. 34Yea, ye yourselves know, that these hands have ministered unto my necessities, and to them that were with me. 35I have shewed you all things, how that so labouring ye ought to support the weak, and to remember the words of the Lord Jesus, how he said, It is more blessed to give than to receive.

36¶ And when he had thus spoken, he kneeled down, and prayed with them all. 37And they all wept sore, and fell on Paul’s neck, and kissed him, 38Sorrowing most of all for the words which he spake, that they should see his face no more. And they accompanied him unto the ship.