Machitidwe a Atumwi 19 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Machitidwe a Atumwi 19:1-41

Paulo ku Efeso

1Apolo ali ku Korinto, Paulo anadutsa mʼmayiko a ku mtunda ndipo anafika ku Efeso. Kumeneko anapeza ophunzira ena. 2Iye anawafunsa kuti, “Kodi munalandira Mzimu Woyera pamene munakhulupirira?”

Iwo anayankha kuti, “Ayi, ife sitinamvepo kuti kuli Mzimu Woyera.”

3Tsono Paulo anawafunsa kuti, “Nanga munabatizidwa ndi ubatizo wotani?”

Iwo anati, “Ubatizo wa Yohane.”

4Paulo anati, “Ubatizo wa Yohane unali wa kutembenuka mtima. Iye anawuza anthu kuti akhulupirire amene amabwera, ameneyo ndiye Yesu.” 5Atamva zimenezi, anabatizidwa mʼdzina la Ambuye Yesu. 6Pamene Paulo anawasanjika manja, Mzimu Woyera anadza pa iwo ndipo anayankhula mʼmalilime ndipo ananenera. 7Anthu onsewo analipo khumi ndi awiri.

8Paulo analowa mʼsunagoge ndipo anayankhula molimba mtima kwa miyezi itatu, kuwatsutsa mowakopa za ufumu wa Mulungu. 9Koma ena anawumitsa mitima; anakana kukhulupirira ndipo ananyoza Njirayo pa gulu la anthu. Kotero Paulo anawasiya. Iye anatenga ophunzirawo ndipo amakambirana tsiku ndi tsiku mʼsukulu ya Turano. 10Izi zinachitika kwa zaka ziwiri, kotero kuti Ayuda onse ndi Agriki amene amakhala ku Asiya anamva Mawu a Ambuye.

11Mulungu anachita zodabwitsa zapadera kudzera mwa Paulo. 12Kotero kuti mipango yopukutira thukuta ndi yovala pogwira ntchito, zomwe zinakhudza thupi la Paulo amapita nazo kwa odwala ndipo amachiritsidwa ndiponso mizimu yoyipa mwa iwo imatuluka.

Za Ana a Skeva

13Ayuda ena amene ankayendayenda kutulutsa mizimu yoyipa anayesa kugwiritsa ntchito dzina la Ambuye Yesu pa amene anali ndi ziwanda. Iwo popemphera amati, “Ine ndikulamulira utuluke, mʼdzina la Yesu amene Paulo amamulalikira.” 14Amene ankachita zimenezi anali ana asanu ndi awiri a Skeva, mkulu wa ansembe wa Chiyuda. 15Tsiku lina mzimu woyipa unawayankha kuti, “Yesu ndimamudziwa ndiponso Paulo ndimamudziwa, nanga inu ndinu ndani?” 16Pamenepo munthu amene anali ndi mzimu woyipa anawalumphira nawagwira onse. Iye anawamenya kwambiri, kotero kuti anathawa mʼnyumbamo ali maliseche, akutuluka magazi.

17Ayuda ndi Agriki okhala ku Efeso atamva zimenezi, anachita mantha, ndipo anthu anachitira ulemu dzina la Ambuye Yesu koposa. 18Ambiri a iwo amene tsopano anakhulupirira anafika ndi kuvomereza poyera ntchito zawo zoyipa. 19Ambiri amene amachita za matsenga anasonkhanitsa mabuku awo pamodzi nawatentha pamaso pa anthu onse. Atawonkhetsa mtengo wa mabukuwo, unakwanira ndalama zasiliva 50,000. 20Kotero Mawu a Ambuye anapitirira kufalikira ndipo anagwira ntchito mwamphamvu.

21Zonsezi zitachitika Paulo anatsimikiza zopita ku Yerusalemu kudzera ku Makedoniya ndi ku Akaya. Iye anati, “Kuchokera kumeneko, ndiyenera kukafikanso ku Roma.” 22Iye anatuma anthu awiri amene amamuthandiza, Timoteyo ndi Erasto ku Makedoniya, pamene iye anakhalabe ku Asiya kwa kanthawi.

Chipolowe ku Efeso

23Pa nthawi yomweyo panachitika chipolowe chachikulu chifukwa cha Njira ya Ambuye. 24Mmisiri wantchito zasiliva, dzina lake Demetriyo, amene amapanga mafano asiliva a Atemi ankabweretsa phindu lalikulu kwa amisiri a kumeneko. 25Iye anasonkhanitsa pamodzi amisiriwo, pamodzinso ndi anthu ena ogwira ntchito yomweyo ndipo anati, “Anthu inu, mukudziwa kuti ife timapeza chuma chathu kuchokera pa ntchito imeneyi. 26Ndipo inu mukuona ndi kumva kuti munthu uyu Paulo wakopa ndi kusokoneza anthu ambiri a ku Efeso ndiponso pafupifupi dziko lonse la Asiya. Iye akunena kuti milungu yopangidwa ndi anthu si milungu ayi. 27Choopsa ndi chakuti sikungowonongeka kwa ntchito yathu yokha ayi, komanso kuti nyumba ya mulungu wamkulu wamkazi Atemi idzanyozedwa ndipo mulungu wamkazi weniweniyo amene amapembedzedwa ku Asiya konse ndi dziko lapansi, ukulu wake udzawonongekanso.”

28Atamva zimenezi, anakwiya kwambiri ndipo anayamba kufuwula kuti, “Wamkulu ndi Atemi.” 29Nthawi yomweyo mu mzinda wonse munabuka chipolowe. Anthu anagwira Gayo ndi Aristariko, anzake a Paulo a ku Makedoniya, ndipo anathamangira nawo ku bwalo la masewero. 30Paulo anafuna kulowa pakati pa gulu la anthu, koma ophunzira anamuletsa. 31Ngakhale olamulira ena aderalo, amene anali abwenzi a Paulo, anatumiza uthenga kumuletsa kuti asayesere kulowa mʼbwalomo.

32Munali chisokonezo mʼbwalomo pakuti ena amafuwula zina, enanso zina. Anthu ambiri sanadziwe ngakhale chomwe anasonkhanira. 33Ayuda anamukankhira Alekisandro kutsogolo, ndipo ena anafuwula kumulangiza iye. Iye anatambasula dzanja kuti anthu akhale chete kuti afotokozere anthu nkhaniyo. 34Koma pamene anthuwo anazindikira kuti ndi Myuda, onse pamodzi kwa maora awiri anafuwula kuti, “Wamkulu ndi Atemi wa ku Efeso!”

35Mlembi wa mzindawo anakhazikitsa bata gulu la anthuwo ndipo anati, “Anthu a ku Efeso, kodi ndani pa dziko lonse lapansi amene sadziwa kuti mzinda wa Efeso umayangʼanira nyumba ya mulungu wamkulu Atemi ndi fanizo lake, limene linagwa kuchokera kumwamba? 36Chifukwa chake popeza zinthu izi palibe amene angazikane, inu mukuyenera kukhala chete osachita kanthu kalikonse mofulumira. 37Inu mwabweretsa anthu awa pano, ngakhale kuti iwo sanabe mʼnyumba zathu zamapemphero kapena kunenera chipongwe mulungu wathu wamkazi. 38Ngati tsono Demetriyo ndi amisiri anzake ali ndi nkhani ndi munthu wina aliyense, mabwalo a milandu alipo, oweruza aliponso. Akhoza kukapereka nkhaniyo kwa oweruza milanduwo. 39Ngati mukufuna kubweretsa kanthu kali konse, ziyenera kukatsimikizidwa ndi bwalo lovomerezeka. 40Monga mmene zililimu, ife titha kuzengedwa mlandu woyambitsa chipolowe chifukwa cha zimene zachitika lerozi. Motero ife sitingathe kufotokoza za chipolowechi popeza palibe nkhani yake.” 41Iye atatha kunena zimenezi anawuza gulu la anthulo kuti libalalike.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

使徒行传 19:1-41

保罗在以弗所传道

1亚波罗哥林多时,保罗已取道内陆重回以弗所,在那里遇见几个门徒。 2保罗问他们:“你们信的时候有没有领受圣灵?”

他们说:“没有!我们从来没有听过圣灵的事。”

3保罗说:“那么,你们受的是什么洗礼呢?”

他们说:“是约翰的洗礼。”

4保罗说:“约翰的洗礼是悔改的洗礼,约翰告诉百姓要信在他以后来的那位——耶稣。”

5他们听后,立刻奉主耶稣的名受了洗。 6保罗把手按在他们身上时,圣灵便降在他们身上,他们就说方言,讲上帝的信息。 7这次共有十二个人。

8保罗一连三个月勇敢地在会堂里传道,与人辩论上帝国的事,劝导他们。 9可是有些人仍然顽固不信,还当众毁谤上帝的道。保罗便带着门徒离开他们,天天在推喇奴的学堂辩论。 10这样持续了两年,亚细亚全境的居民,无论是犹太人还是希腊人,都听见了主的道。 11上帝又借着保罗的手行了一些非凡的神迹, 12甚至只要将保罗身上的手帕或围裙放在病人身上,病人就痊愈了,邪灵也会离开所附的人。

13那时,有几个走江湖的犹太术士也想用耶稣的名赶鬼,他们向那些被邪灵附身的人说:“我奉保罗所传讲的耶稣之名,命令你们出来!” 14做这事的有犹太祭司长士基瓦的七个儿子。

15邪灵回答说:“耶稣,我认识;保罗,我也知道。但你们是谁?” 16被邪灵附身的人随即扑向他们,攻击他们,制服了他们,使他们赤着身子带着伤从屋里逃走了。

17以弗所犹太人和希腊人知道了这件事,都惊惧不已。主耶稣的名因此大受尊崇。 18许多已经信耶稣的人都前来认罪,公开承认自己的恶行。 19又有许多行邪术的人把他们的书堆在一起,当众焚烧。根据当时的估价,这些书约值五万银币。 20主的道就这样传开了,大大兴旺起来。

21这些事以后,保罗决定经过马其顿亚该亚回到耶路撒冷。他说:“到了那里之后,我必须去罗马看看。” 22于是,他派提摩太以拉都两位同工先去马其顿,自己暂时留在亚细亚

以弗所的骚乱

23就在这时,由于主的道,以弗所又起了很大的骚乱。 24一个名叫底米丢的银匠以制造亚底米女神银龛为业,使从事这门生意的工匠获利丰厚。 25他召集了工匠和同行的人,说:“各位都知道我们靠这一行发财, 26可是你们都看到了,也听见了,那个保罗以弗所亚细亚全境说服、误导了许多人,说什么人手所造的不是神。 27这样下去,不但我们的行业会遭人贬抑,连亚底米女神庙也会被人轻看,甚至全亚细亚及普世尊崇的女神也会威严扫地!”

28众人听后,怒气填胸,高声喊叫:“以弗所人的亚底米女神真伟大!” 29全城陷入一片混乱。众人抓住保罗的两个同伴——马其顿该犹亚里达古,拖着他们冲进戏院。 30保罗想进去,但门徒不许他去。 31他的好友——亚细亚的几位官员也派人劝他别冒险进入戏院。

32这时,戏院里面的人都在大喊大叫,混乱不堪。其实大部分人根本不知道自己为什么聚在那里。 33这时,人群中的犹太人把亚历山大推到前面,请他解释。亚历山大举手示意大家安静,听他发言。 34但众人认出他是个犹太人,便又开始一起高呼:“以弗所人的亚底米女神真伟大!”这样喊了两个小时。

35最后,城里的书记官出面调停,说:“各位以弗所市民,谁不知道以弗所城守护着亚底米女神庙和从宙斯那里掉下来的神像呢? 36既然这是无可否认的事实,你们就该安静,不可鲁莽行事。 37你们带来的这些人既没有偷庙里的东西,也没有亵渎我们的女神。 38如果底米丢和他的同行要控告谁,大可到法庭或总督那里提出诉讼。 39倘若你们还有其他的要求,也可以通过合法的会议解决。 40今天的骚乱实在没有道理,难免会被查问,到时候我们很难交代。” 41说完,便叫众人散去。