Machitidwe a Atumwi 17 – CCL & CST

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Machitidwe a Atumwi 17:1-34

Paulo ku Tesalonika

1Atadutsa ku Amfipoli ndi Apoloniya, anafika ku Tesalonika, kumene kunali sunagoge ya Ayuda. 2Paulo, monga mwachizolowezi chake, analowa mʼsunagoge, ndipo anakambirana nawo Mawu a Mulungu kwa masabata atatu, 3kuwafotokozera ndi kuwatsimikizira kuti Khristu anayenera kufa ndi kuuka. Iye anati, “Yesu amene ndikukulalikirani ndiye Khristu.” 4Ena mwa Ayuda anakopeka mtima ndipo anatsatira Paulo ndi Sila, monganso linachitira gulu lalikulu la Agriki woopa Mulungu, pamodzi ndi amayi odziwika ambiri.

5Koma Ayuda ena anachita nsanje; kotero anasonkhanitsa anthu akhalidwe loyipa ochokera pa msika ndipo napanga gulu nayambitsa chipolowe mu mzindawo. Anathamangira ku nyumba ya Yasoni kukafuna Paulo ndi Sila kuti awabweretse pa gulu la anthu. 6Koma atalephera kuwapeza, anakokera Yasoniyo ndi abale ena ku bwalo la akulu a mzindawo akufuwula kuti, “Anthu awa, Paulo ndi Sila, amene akhala akusokoneza dziko lonse lapansi, tsopano afikanso kuno. 7Yasoni ndiye anawalandira mʼnyumba mwake. Onsewa akuchita zotsutsana ndi malamulo a Kaisara pomanena kuti palinso mfumu ina, yotchedwa Yesu.” 8Atamva zimenezi, gulu la anthu ndi akulu a mzinda anavutika mu mtima. 9Iwo analipiritsa Yasoni ndi anzakewo ndipo anawamasula.

Ku Bereya

10Mdima utagwa, abale anatumiza Paulo ndi Sila ku Bereya. Atafika kumeneko anapita ku sunagoge ya Ayuda. 11Tsopano anthu a ku Bereya anali akhalidwe labwino kusiyana ndi Atesalonika, pakuti iwo analandira mawu ndi chidwi chachikulu ndipo ankasanthula Malemba tsiku ndi tsiku kuti aone ngati zimene ankanena Paulozo zinali zoona. 12Ayuda ambiri anakhulupirira, monga anachitiranso amayi ndi amuna ambiri odziwika a Chigriki.

13Ayuda a ku Tesalonika atadziwa kuti Paulo akulalikira Mawu a Mulungu ku Bereya, anapitanso kumeneko, ndi kuwutsa mitima ya anthu nayambitsa chisokonezo. 14Nthawi yomweyo abale anatumiza Paulo ku nyanja koma Sila ndi Timoteyo anatsalira ku Bereya. 15Anthu amene anamuperekeza Paulo nafika naye ku Atene, ndipo anabwerera ku Bereya atawuzidwa kuti Sila ndi Timoteyo amutsatire msanga.

Ku Atene

16Paulo akudikira Timoteyo ndi Sila ku Atene, anavutika mu mtima kwambiri poona kuti mzindawo unali odzaza ndi mafano. 17Tsono anakambirana ndi Ayuda ndi Agriki amene amaopa Mulungu mʼsunagoge, komanso anthu amene amapezeka pa msika tsiku ndi tsiku ndi ena amene amakumana nawo. 18Gulu la Aepikureya ndi Astoiki, anthu anzeru, anayamba kutsutsana naye. Ena a iwo anafunsa kuti, “Kodi wolongololayu akufuna kunena chiyani?” Enanso anati, “Akuoneka ngati akulalikira milungu yachilendo.” Iwo ananena zimenezi chifukwa Paulo amalalikira Uthenga Wabwino wa Yesu ndi kuuka kwa akufa. 19Kenaka iwo anamutenga nafika naye ku bwalo la Areopagi kumene anamufunsa kuti, “Kodi tingadziweko chiphunzitso chatsopano chimene ukuchifotokozachi? 20Iwe ukubweretsa zinthu zina zachilendo mʼmakutu mwathu, ndipo ife tikufuna tidziwe tanthauzo lake.” 21Atene onse ndi alendo amene amakhala kumeneko samachita kanthu kena koma kufotokoza ndi kumvera fundo zatsopano.

22Paulo anayimirira mʼbwalo la Areopagi nati: “Inu anthu a ku Atene! Ine ndikuona kuti mʼnjira zonse ndinu opembedza kwambiri. 23Pakuti pamene ndimayenda ndi kuona zinthu zimene mumazipembedza, ndapezanso guwa lansembe lolembedwapo kuti, kwa mulungu wosadziwika. Tsopano chimene mumachipembedza osachidziwa ndi chimene ndikuchilalikira.

24“Mulungu amene analenga dziko lapansi ndiponso zonse zili mʼmenemo ndiye Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi ndipo sakhala mʼnyumba zachipembedzo zomangidwa ndi manja. 25Ndipo satumikiridwa ndi manja a anthu ngati kuti Iye amasowa kanthu, chifukwa Iye ndiye amapereka moyo ndi mpweya kwa anthu onse ndi zina zonse. 26Kuchoka kwa munthu mmodzi Iye analenga mtundu uliwonse wa anthu, kuti akakhale pa dziko lonse lapansi; ndipo Iye anakonzeratu nthawi yawo ndiponso malo enieni kumene adzakhale. 27Mulungu anachita izi kuti anthu amufunefune, ndikuti pomufunafunapo amupeze ngakhale kuti Iye sali kutali ndi aliyense wa ife. 28‘Pakuti timakhala mwa Iye, kuyenda mwa Iye ndi kukhala moyo mwa Iye.’ Monga olemba ndakatulo anu ena akuti, ‘Ife ndi zidzukulu zake.’

29“Tsono popeza ndife ana a Mulungu, tisaganize kuti umulungu wake ndi wofanana ndi ndalama zagolide, zasiliva, mwala, kapenanso fanizo lopangidwa mwaluso la nzeru za anthu. 30Nthawi imene anthu sankadziwa, Mulungu anawalekerera koma tsopano akulamulira kuti anthu onse, kulikonse atembenuke mtima. 31Pakuti Iye wayika tsiku limene adzaweruze dziko lapansi mwa chilungamo kudzera mwa Munthu amene anamusankha. Iye watsimikizira anthu onse zimenezi pomuukitsa.”

32Atamva za kuuka kwa akufa, ena a iwo anaseka, koma enanso anati, “Ife tikufuna tidzamvenso zimenezi tsiku lina.” 33Ndipo Paulo anatuluka mʼBwalolo. 34Anthu ena ochepa anamutsatira Paulo ndipo anakhulupirira. Pakati pawo panali Dionisiyo mmodzi wa bwalo la Areopagi ndi mayi wina wotchedwa Damalisi ndi enanso.

Nueva Versión Internacional (Castilian)

Hechos 17:1-34

En Tesalónica

1Atravesando Anfípolis y Apolonia, Pablo y Silas llegaron a Tesalónica, donde había una sinagoga de los judíos. 2Como era su costumbre, Pablo entró en la sinagoga y tres sábados seguidos discutió con ellos. Basándose en las Escrituras, 3les explicaba y demostraba que era necesario que el Mesías padeciera y resucitara. Les decía: «Este Jesús que les anuncio es el Mesías». 4Algunos de los judíos se convencieron y se unieron a Pablo y a Silas, como también lo hicieron un buen número de mujeres prominentes y muchos griegos que adoraban a Dios.

5Pero los judíos, llenos de envidia, reclutaron a unos maleantes callejeros, con los que armaron una turba y empezaron a alborotar la ciudad. Asaltaron la casa de Jasón en busca de Pablo y Silas, con el fin de procesarlos públicamente. 6Pero, como no los encontraron, arrastraron a Jasón y a algunos otros hermanos ante las autoridades de la ciudad, gritando: «¡Estos que han trastornado el mundo entero han venido también acá, 7y Jasón los ha recibido en su casa! Todos ellos actúan en contra de los decretos del emperador, afirmando que hay otro rey, uno que se llama Jesús». 8Al oír esto, la multitud y las autoridades de la ciudad se alborotaron; 9entonces estas exigieron fianza a Jasón y a los demás para dejarlos en libertad.

En Berea

10Tan pronto como se hizo de noche, los hermanos enviaron a Pablo y a Silas a Berea, quienes al llegar se dirigieron a la sinagoga de los judíos. 11Estos eran de sentimientos más nobles que los de Tesalónica, de modo que recibieron el mensaje con toda avidez y todos los días examinaban las Escrituras para ver si era verdad lo que se les anunciaba. 12Muchos de los judíos creyeron, y también un buen número de griegos, incluso mujeres distinguidas y no pocos hombres.

13Cuando los judíos de Tesalónica se enteraron de que también en Berea estaba Pablo predicando la palabra de Dios, fueron allá para agitar y alborotar a las multitudes. 14En seguida los hermanos enviaron a Pablo hasta la costa, pero Silas y Timoteo se quedaron en Berea. 15Los que acompañaban a Pablo lo llevaron hasta Atenas. Luego regresaron con instrucciones de que Silas y Timoteo se reunieran con él tan pronto como les fuera posible.

En Atenas

16Mientras Pablo los esperaba en Atenas, le dolió en el alma ver que la ciudad estaba llena de ídolos. 17Así que discutía en la sinagoga con los judíos y con los griegos que adoraban a Dios, y a diario hablaba en la plaza con los que se encontraban por allí. 18Algunos filósofos epicúreos y estoicos entablaron conversación con él. Unos decían: «¿Qué querrá decir este charlatán?» Otros comentaban: «Parece que es predicador de dioses extranjeros». Decían esto porque Pablo les anunciaba las buenas nuevas de Jesús y de la resurrección. 19Entonces se lo llevaron a una reunión del Areópago.

―¿Se puede saber qué nueva enseñanza es esta que usted presenta? —le preguntaron—. 20Porque nos viene usted con ideas que nos suenan extrañas, y queremos saber qué significan.

21Es que todos los atenienses y los extranjeros que vivían allí se pasaban el tiempo sin hacer otra cosa más que escuchar y comentar las últimas novedades.

22Pablo se puso en medio del Areópago y tomó la palabra:

―¡Ciudadanos atenienses! Observo que ustedes son sumamente religiosos en todo lo que hacen. 23Al pasar y fijarme en sus lugares sagrados, encontré incluso un altar con esta inscripción: A un dios desconocido. Pues bien, eso que ustedes adoran como algo desconocido es lo que yo les anuncio.

24»El Dios que hizo el mundo y todo lo que hay en él es Señor del cielo y de la tierra. No vive en templos construidos por hombres, 25ni se deja servir por manos humanas, como si necesitara de algo. Por el contrario, él es quien da a todos la vida, el aliento y todas las cosas. 26De un solo hombre hizo todas las naciones17:26 todas las naciones. Alt. todo el género humano. para que habitaran toda la tierra; y determinó los períodos de su historia y las fronteras de sus territorios. 27Esto lo hizo Dios para que todos lo busquen y, aunque sea a tientas, lo encuentren. En verdad, él no está lejos de ninguno de nosotros, 28“puesto que en él vivimos, nos movemos y existimos”. Como algunos de sus propios poetas griegos han dicho: “De él somos descendientes”.

29»Por tanto, siendo descendientes de Dios, no debemos pensar que la divinidad sea como el oro, la plata o la piedra: escultura hecha como resultado del ingenio y de la destreza del ser humano. 30Pues bien, Dios pasó por alto aquellos tiempos de tal ignorancia, pero ahora manda a todos, en todas partes, que se arrepientan. 31Él ha fijado un día en que juzgará al mundo con justicia, por medio del hombre que ha designado. De ello ha dado pruebas a todos al levantarlo de entre los muertos».

32Cuando oyeron de la resurrección, unos se burlaron; pero otros le dijeron:

―Queremos que usted nos hable en otra ocasión sobre este tema.

33En ese momento Pablo salió de la reunión. 34Algunas personas se unieron a Pablo y creyeron. Entre ellos estaba Dionisio, miembro del Areópago, también una mujer llamada Dámaris, y otros más.