Luka 5 – CCL & SNC

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Luka 5:1-39

Yesu Ayitana Ophunzira Oyamba

1Tsiku lina Yesu anayima mʼmbali mwa nyanja ya Genesareti, gulu la anthu litamuzungulira likumvetsera mawu a Mulungu. 2Iye anaona mabwato awiri ali mʼmphepete mwa nyanja, asodzi amene ankachapa makhoka awo atawasiya pamenepo. 3Iye analowa mʼbwato limodzi limene linali la Simoni, ndi kumupempha kuti alikankhire mʼkati mwa nyanja pangʼono. Kenaka Iye anakhala pansi nayamba kuphunzitsa anthu ali mʼbwatomo.

4Atatha kuyankhula anati kwa Simoni, “Kankhirani kwa kuya ndipo muponye makhoka kuti mugwire nsomba.”

5Simoni anayankha kuti, “Ambuye, tagwira ntchito molimbika usiku wonse, koma sitinagwire kanthu. Koma pakuti mwatero, ndiponya makhoka.”

6Atachita izi, anagwira nsomba zambiri kotero kuti makhoka awo anayamba kungʼambika. 7Choncho anakodola anzawo a bwato linalo kuti abwere ndi kuwathandiza, ndipo anabwera nadzaza mabwato onse awiri mpaka kuyamba kumira.

8Simoni Petro ataona izi, anagwa pa mawondo a Yesu nati, “Chokani kwa ine Ambuye: Ine ndine munthu wochimwa!” 9Iye ndi anzake onse anadabwa ndi nsomba zimene anagwira, 10chimodzimodzinso Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo, anzake a Simoniyo.

Kenaka Yesu anati kwa Simoni, “Musachite mantha; kuyambira tsopano ndidzakusandutsani asodzi a anthu.” 11Kenaka anakokera mabwato awo ku mtunda, nasiya zonse namutsata Iye.

Yesu Achiritsa Munthu Wakhate

12Yesu ali ku mudzi wina, munthu amene anali ndi khate thupi lonse anabwera kwa Iye. Munthuyo ataona Yesu, anagwa chafufumimba ndipo anamupempha Iye kuti, “Ambuye, ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.”

13Yesu anatambasula dzanja lake namukhudza munthuyo. Iye anati, “Ine ndikufuna, yeretsedwa!” Ndipo nthawi yomweyo khate lake linachoka.

14Kenaka Yesu anamulamula kuti, “Usawuze wina aliyense, koma pita, kadzionetse kwa wansembe ndi kukapereka nsembe zimene Mose anakulamulirani za kuyeretsedwa kwanu monga umboni kwa iwo.”

15Koma mbiri yake inafalikirabe kwambiri kotero kuti magulu a anthu anabwera kudzamvetsera ndi kuti achiritsidwe ku matenda awo. 16Koma Yesu nthawi zambiri ankachoka kupita ku malo a yekha kukapemphera.

Yesu Achiritsa Wofa Ziwalo

17Tsiku lina pamene ankaphunzitsa, Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo, amene anachokera ku midzi yonse ya Galileya ndi ku Yudeya ndi Yerusalemu, anakhala pansi pomwepo. Ndipo mphamvu ya Ambuye inalipo yakuti Iye achiritse odwala. 18Amuna ena anabwera atanyamula munthu wofa ziwalo pa mphasa ndipo anayesa kumulowetsa mʼnyumba kuti amugoneke pamaso pa Yesu. 19Atalephera kupeza njira yochitira zimenezi chifukwa cha gulu la anthu, anakwera naye pa denga ali pa mphasa pomwepo ndi kumutsitsira mʼkati pakati pa gulu la anthu, patsogolo penipeni pa Yesu.

20Yesu ataona chikhulupiriro chawo, anati, “Mnzanga, machimo ako akhululukidwa.”

21Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo anayamba kuganiza mwa iwo okha kuti, “Kodi munthu uyu ndi ndani amene ayankhula zamwano? Kodi ndani amene angakhululukire machimo kupatula Mulungu?”

22Yesu anadziwa zomwe iwo amaganiza ndipo anafunsa kuti, “Kodi ndi chifukwa chiyani mukuganiza zimenezi mʼmitima mwanu? 23Kodi chapafupi ndi chiti: kunena kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kunena kuti, ‘Nyamuka ndipo yenda?’24Koma kuti inu mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali ndi ulamuliro pa dziko lapansi wokhululukira machimo, Iye anati kwa munthu wofa ziwaloyo, “Ine ndikuwuza iwe kuti, ‘Imirira, nyamula mphasa ndipo uzipita kwanu.’ ” 25Nthawi yomweyo anayimirira patsogolo pawo, nanyamula mphasa yake ndipo anapita kwawo akuyamika Mulungu. 26Aliyense anadabwa ndi kuchita mantha ndipo anayamika Mulungu. Iwo anadabwa kwambiri ndipo anati, “Lero taona zinthu zosayiwalika.”

Kuyitanidwa kwa Levi

27Zitatha izi, Yesu anachoka ndipo anaona wolandira msonkho dzina lake Levi atakhala mʼnyumba ya msonkho. Yesu anati kwa iye, “Nditsate Ine.” 28Ndipo Levi anayimirira, nasiya zonse ndi kumutsata Iye.

29Kenaka Levi anakonzera Yesu phwando lalikulu ku nyumba yake ndipo gulu lalikulu la amisonkho ndi ena ankadya naye pamodzi. 30Koma Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo amene anali a gulu lawo anadandaula kwa ophunzira ake, “Kodi ndi chifukwa chiyani mukudya ndi kumwa pamodzi ndi amisonkho ndi ochimwa?”

31Yesu anawayankha kuti, “Amene sakudwala safuna singʼanga, koma odwala. 32Ine sindinabwere kudzayitana olungama, koma ochimwa kuti atembenuke mtima.”

Yesu Afunsidwa za Kusala Kudya

33Iwo anati kwa Iye, “Ophunzira a Yohane amasala kudya ndi kupemphera kawirikawiri, monganso ophunzira a Afarisi, koma anu amangodya ndi kumwa.”

34Yesu anawayankha kuti, “Kodi alendo a mkwati angasale kudya pamene mkwati ali pakati pawo? 35Koma nthawi ikubwera pamene mkwati adzachotsedwa pakati pawo. Masiku amenewo adzasala kudya.”

36Iye anawawuza fanizo ili: “Palibe amene amangʼamba chigamba kuchokera pa chovala chatsopano ndi kuchisokerera pa chakale. Ngati atatero, ndiye kuti adzangʼamba chovala chatsopanocho, ndipo chigamba chochokera pa chovala chatsopano chija sichidzagwirizana ndi chakale. 37Ndipo palibe amene amakhuthulira vinyo watsopano mʼmatumba a vinyo akale. Ngati atatero, vinyo watsopanoyo adzaphulitsa zikopazo, vinyo adzatayika ndipo zikopa za vinyozo zidzawonongeka. 38Ayi, vinyo watsopano ayenera kuthiridwa mʼmatumba a vinyo azikopa zatsopano. 39Ndipo palibe amene atamwa vinyo wakale amafuna watsopano, pakuti amati, ‘Wakale ndi okoma.’ ”

Slovo na cestu

Lukáš 5:1-39

Ježíšova rada přinese zázračný úlovek

1Jednoho dne stál Ježíš u Genezaretského jezera. Lidé se kolem něho tlačili a chtěli slyšet jeho kázání. 2Všiml si, že u břehu jsou dvě lodi. Opodál prali rybáři svoje sítě. 3Posadil se do jedné lodi, která patřila Šimonovi, a požádal ho, aby ho zavezl kousek od břehu. Odtud pak kázal zástupům. 4Když skončil, navrhl Šimonovi: „Zajeď s lodí na hloubku a roztáhněte sítě k lovu.“ 5Šimon namítal: „Pane, celou noc jsme se namáhali, ale marně. Když to však říkáš ty, zkusím to ještě jednou.“ 6Vypluli a zatáhli takové množství ryb, že se i sítě trhaly. 7Museli si zavolat na pomoc své přátele z druhé lodi. Obě lodi byly nakonec rybami tak naplněny, že se div nepotopily. 8Když to viděl Šimon, padl před Ježíšem na kolena a prosil: „Odejdi Pane, neobstojím v tvé blízkosti, jsem hříšný člověk.“ 9-10Všichni rybáři, kteří u toho byli – mezi nimi také Šimonovi přátelé, Jakub a Jan, synové Zebedeovi, žasli nad tím neobvyklým úlovkem. Ježíš řekl Šimonovi: „Neboj se! Učiním tě rybářem lidí. Budeš je získávat pro mne.“ 11Přirazili s loděmi ke břehu, všechno tam nechali a šli s Ježíšem.

12V jednom městečku potkal Ježíš člověka s pokročilým malomocenstvím. Ubožák před ním poklekl a prosil: „Pane, kdybys chtěl, mohl bys mne uzdravit.“ 13Ježíš se ho dotkl a řekl: „Ano, chci, buď zdráv!“ V tom okamžiku malomocenství zmizelo. 14Ježíš mu poručil: „Nikomu o tom nevyprávěj, jdi, ukaž se knězi, ať tě prohlásí za zdravého, a pak obětuj předepsanou oběť vděčnosti.“ 15Zpráva o Ježíšovi se rychle šířila. Lidé za ním přicházeli v houfech, aby ho slyšeli a aby uzdravoval jejich nemoci. 16On si však vždycky našel čas, aby se v ústraní modlil.

Ježíš uzdravuje ochrnutého

17Jednoho dne se kolem Ježíše shromáždili farizejové a učitelé zákona z různých měst Galileje a Judska a dokonce i z Jeruzaléma. Posadili se kolem něho a naslouchali mu. I zde mu dal Bůh moc k uzdravování. 18-19Nějací lidé přinesli na nosítkách ochrnutého muže. Chtěli ho vnést dveřmi a položit před Ježíše, ale bylo tam tolik lidí, že nemohli projít. Vystoupili tedy na střechu a otvorem spustili nemocného i s lehátkem přímo před něho. Když 20Ježíš viděl, kolik důvěry v něho mají, řekl: „Příteli, tvoje hříchy jsou ti odpuštěny.“ 21Učitelé zákona a farizejové uvažovali: „Jak se může opovážit něco takového říci? To je přece rouhání. Nikdo jiný než Bůh nemůže odpouštět hříchy!“ 22Ježíš dobře věděl, co si myslí, a proto řekl: „To vám vadí? 23Co je snazší? Zvěstovat člověku odpuštění jeho hříchů, anebo ho uzdravit? 24Přesvědčím vás, že Syn člověka má na zemi právo odpouštět hříchy.“ Obrátil se k ochrnutému se slovy: „Vstaň, vezmi si svoje lehátko a jdi domů!“ 25A tak se stalo: před očima všech muž vstal, sbalil svou rohož, šel domů a cestou hlasitě děkoval Bohu. 26Celé shromáždění bylo vzrušeno a lidé, plni svaté bázně, chválili Boha a říkali: „Dnes jsme viděli neuvěřitelné věci.“

Ježíš stoluje s hříšníky v Matoušově domě

27Ježíš šel dál. Cestou uviděl v celnici výběrčího daní jménem Levi a řekl mu: „Pojď, staň se mým následovníkem!“ 28Levi nechal všeho, vstal a šel za Ježíšem. 29Doma pak vystrojil pro Ježíše a jeho žáky hostinu. Na ni pozval i mnoho svých dřívějších kolegů. 30To pohoršilo farizeje a učitele zákona, takže vytýkali učedníkům: „Proč jíte a pijete s lidmi, kterými každý slušný člověk pohrdá?“ 31Ježíš na to odpověděl: „Lékaře nepotřebují zdraví, ale nemocní. 32Nepřišel jsem volat k pokání ty, kteří mají o sobě dobré mínění, ale hříšníky.“

Spor o půst

33Někteří farizejové Ježíšovi předhazovali: „Janovi učedníci se často s postem modlí a právě tak i naši žáci. Jak to tedy, že tvoji hodují?“ 34Ježíš odpověděl: „Je přirozené, aby se svatebčané postili, když je ženich s nimi? 35Však přijde chvíle, kdy ženicha odvedou, a pak bude vhodný čas k půstu.“ 36Ještě přidal další přirovnání: „Nikdo si přece nevystřihne kus látky z nových šatů, aby si jím vyspravil starý oděv. Zničil by si tak šaty nové a na starých šatech by se záplata srazila a díra by byla ještě větší. 37Nikdo také nebude nalévat víno do starých kožených měchů, protože kvasící víno by staré měchy roztrhalo, a tak by obojí přišlo nazmar. 38Proto mladé víno patří do nových měchů. 39Vás ovšem znepokojuje moje poselství. Jako mladé víno nesnesou staré měchy, ani ono se nevtěsná do vašich starých tradic a zvyklostí. Jste jako pijáci, kteří si libují ve starém uleželém vínu.“