Luka 14 – CCL & NIV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Luka 14:1-35

Yesu Mʼnyumba ya Mfarisi

1Pa tsiku lina la Sabata, Yesu atapita kukadya ku nyumba ya Mfarisi wodziwika, Afarisi anamulonda mosamalitsa. 2Poteropo, patsogolo pake panali munthu amene anadwala matenda otupa mimba ndi miyendo. 3Yesu anafunsa Afarisi ndi akatswiri amalamulo kuti, “Kodi ndi zololedwa kuchiritsa pa tsiku la Sabata kapena ayi?” 4Koma iwo sanayankhe. Tsono atamutenga munthuyo, Iye anamuchiritsa ndipo anamuwuza kuti azipita.

5Kenaka Iye anawafunsa kuti, “Kodi ngati mmodzi mwa inu ali ndi mwana wamwamuna kapena ngʼombe imene yagwera mʼchitsime tsiku la Sabata, kodi simungamuvuwulemo tsiku lomwelo?” 6Ndipo iwo analibe choyankha.

Kudzichepetsa ndi Kulandira Ulemu

7Iye ataona momwe alendo amasankhira malo aulemu pa tebulo, Iye anawawuza fanizo ili: 8“Pamene wina wakuyitanani ku phwando la ukwati, musakhale pa malo aulemu ayi, chifukwa mwina anayitananso munthu wina wolemekezeka kuposa inu. 9Ngati zitatero, ndiye kuti munthu uja amene anakuyitani inu nonse awiri adzakuwuzani kuti, ‘Mupatseni munthu uyu malo anu.’ Pamenepo inu mudzachita manyazi, pokakhala malo wotsika. 10Koma akakuyitanani, khalani pa malo otsika, kuti amene anakuyitanani uja adzakuwuzeni kuti, ‘Bwenzi, bwera udzakhale pa malo aulemu pano.’ Pamenepo inu mudzalandira ulemu pamaso pa alendo anzanu onse. 11Pakuti aliyense wodzikuza adzamuchepetsa, ndipo aliyense wodzichepetsa adzamukweza.”

12Kenaka Yesu anati kwa mwini malo uja, “Ukakonza chakudya chamasana kapena chamadzulo, usamayitane abwenzi ako, abale ako, anthu afuko lako kapena anzako achuma; ngati iwe utero, iwo adzakuyitananso, choncho udzalandiriratu mphotho yako. 13Koma ukakonza phwando, itana anthu osauka, ofa ziwalo, olumala ndi osaona. 14Pamenepo udzakhala wodala, chifukwa iwo sangakubwezere kanthu, koma Mulungu ndiye adzakubwezera pa chiukitso cha olungama.”

Fanizo la Phwando Lalikulu

15Mmodzi mwa amene amadya naye atamva izi, anati kwa Yesu, “Ndi wodala munthu amene adzadye nawo mu ufumu wa Mulungu.”

16Yesu anayankha kuti, “Munthu wina ankakonza phwando lalikulu ndipo anayitana alendo ambiri. 17Nthawi yaphwando itakwana anatuma wantchito wake kuti akawuze onse amene anayitanidwa kuti, ‘Bwerani, pakuti zonse zakonzeka.’

18“Koma onse anayamba kupereka zifukwa mofanana. Woyamba anati, ‘Ine ndangogula kumene munda, ndipo ndikuyenera kupita kuti ndikawuone. Pepani mundikhululukire.’

19“Wina anati, ‘Ndangogula kumene ngʼombe khumi zokoka ngolo ndipo kupita kukaziyesa. Pepani mundikhululukire.’

20“Wina anatinso, ‘Ine ndangokwatira kumene, choncho sinditha kubwera.’

21“Wantchitoyo anabwera ndikudzamuwuza bwana wakeyo zimenezi. Pamenepo mphwandoyo anapsa mtima ndipo analamula wantchito wakeyo kuti, ‘Pita msangamsanga kunja mʼmisewu ndi mʼmakwalala a mu mzinda ndipo ukabweretse osauka, ofa ziwalo, osaona ndi olumala.’

22“Wantchitoyo anati, ‘Bwana, zimene munanena zachitika koma malo akanalipobe.’

23“Ndipo mbuye uja anawuza wantchito wake kuti, ‘Pita kunja ku misewu ikuluikulu ndi kunja kwa mpanda ndipo ukawawuze kuti alowe, kuti nyumba yanga idzaze. 24Ine ndikukuwuzani inu kuti palibe ndi mmodzi yemwe mwa anthu amene anayitanidwa adzalawa phwandolo.’ ”

Dipo la Kutsatira Yesu

25Gulu lalikulu la anthu linkayenda naye Yesu ndipo atatembenukira kwa iwo anati, 26“Ngati wina aliyense abwera kwa Ine ndipo sadana ndi abambo ndi amayi ake, mkazi wake ndi ana, abale ake ndi alongo ake, inde ngakhale moyo wake omwe, iye sangakhale ophunzira wanga. 27Ndipo aliyense amene sasenza mtanda wake ndi kunditsata Ine sangakhale ophunzira wanga.

28“Taganizani, ngati wina mwa inu akufuna kumanga nsanja, kodi iye sayamba wakhala pansi ndi kuganizira za mtengo wake kuti aone ngati ali ndi ndalama zokwanira kuti atsirizire? 29Pakuti ngati ayika maziko ndi kulephera kutsiriza, aliyense amene adzayiona adzamuseka, 30nanena kuti, ‘Munthu uyu anayamba kumanga koma sanathe kutsiriza.’

31“Kapena mfumu imene ikupita ku nkhondo kukamenyana ndi mfumu ina, kodi siyamba yakhala pansi ndi kulingalira ngati ingathe ndi anthu 10,000 kulimbana ndi amene akubwera ndi 20,000? 32Ngati singathe, idzatuma nthumwi pomwe winayo ali kutali ndi kukapempha mgwirizano wamtendere. 33Mʼnjira yomweyo, wina aliyense wa inu amene sasiya zonse ali nazo sangakhale ophunzira wanga.

34“Mchere ndi wabwino, koma ngati usukuluka adzawukoleretsanso ndi chiyani? 35Suyeneranso ngakhale mʼnthaka kapena kudzala la manyowa; umatayidwa kunja.

“Amene ali ndi makutu akumva, amve.”

New International Version

Luke 14:1-35

Jesus at a Pharisee’s House

1One Sabbath, when Jesus went to eat in the house of a prominent Pharisee, he was being carefully watched. 2There in front of him was a man suffering from abnormal swelling of his body. 3Jesus asked the Pharisees and experts in the law, “Is it lawful to heal on the Sabbath or not?” 4But they remained silent. So taking hold of the man, he healed him and sent him on his way.

5Then he asked them, “If one of you has a child14:5 Some manuscripts donkey or an ox that falls into a well on the Sabbath day, will you not immediately pull it out?” 6And they had nothing to say.

7When he noticed how the guests picked the places of honor at the table, he told them this parable: 8“When someone invites you to a wedding feast, do not take the place of honor, for a person more distinguished than you may have been invited. 9If so, the host who invited both of you will come and say to you, ‘Give this person your seat.’ Then, humiliated, you will have to take the least important place. 10But when you are invited, take the lowest place, so that when your host comes, he will say to you, ‘Friend, move up to a better place.’ Then you will be honored in the presence of all the other guests. 11For all those who exalt themselves will be humbled, and those who humble themselves will be exalted.”

12Then Jesus said to his host, “When you give a luncheon or dinner, do not invite your friends, your brothers or sisters, your relatives, or your rich neighbors; if you do, they may invite you back and so you will be repaid. 13But when you give a banquet, invite the poor, the crippled, the lame, the blind, 14and you will be blessed. Although they cannot repay you, you will be repaid at the resurrection of the righteous.”

The Parable of the Great Banquet

15When one of those at the table with him heard this, he said to Jesus, “Blessed is the one who will eat at the feast in the kingdom of God.”

16Jesus replied: “A certain man was preparing a great banquet and invited many guests. 17At the time of the banquet he sent his servant to tell those who had been invited, ‘Come, for everything is now ready.’

18“But they all alike began to make excuses. The first said, ‘I have just bought a field, and I must go and see it. Please excuse me.’

19“Another said, ‘I have just bought five yoke of oxen, and I’m on my way to try them out. Please excuse me.’

20“Still another said, ‘I just got married, so I can’t come.’

21“The servant came back and reported this to his master. Then the owner of the house became angry and ordered his servant, ‘Go out quickly into the streets and alleys of the town and bring in the poor, the crippled, the blind and the lame.’

22“ ‘Sir,’ the servant said, ‘what you ordered has been done, but there is still room.’

23“Then the master told his servant, ‘Go out to the roads and country lanes and compel them to come in, so that my house will be full. 24I tell you, not one of those who were invited will get a taste of my banquet.’ ”

The Cost of Being a Disciple

25Large crowds were traveling with Jesus, and turning to them he said: 26“If anyone comes to me and does not hate father and mother, wife and children, brothers and sisters—yes, even their own life—such a person cannot be my disciple. 27And whoever does not carry their cross and follow me cannot be my disciple.

28“Suppose one of you wants to build a tower. Won’t you first sit down and estimate the cost to see if you have enough money to complete it? 29For if you lay the foundation and are not able to finish it, everyone who sees it will ridicule you, 30saying, ‘This person began to build and wasn’t able to finish.’

31“Or suppose a king is about to go to war against another king. Won’t he first sit down and consider whether he is able with ten thousand men to oppose the one coming against him with twenty thousand? 32If he is not able, he will send a delegation while the other is still a long way off and will ask for terms of peace. 33In the same way, those of you who do not give up everything you have cannot be my disciples.

34“Salt is good, but if it loses its saltiness, how can it be made salty again? 35It is fit neither for the soil nor for the manure pile; it is thrown out.

“Whoever has ears to hear, let them hear.”